Chigawo 6
Chifukwa Chake Mulungu Walola Kuvutika
1, 2. Kodi ndi motani mmene makolo athu oyamba anawonongera chiyambi chawo chabwino kwambiri chimene Mulungu anawapatsa?
KODI chinalakwikwa n’chiyani? Kodi chinachitika n’chiyani kuwononga chiyambi chabwino kwambiri chimene Mulungu anapatsa makolo athu oyambirira m’Paradaiso wa Edeni? Kodi n’chifukwa ninji, mmalo mwa mtendere ndi chigwirizano cha Paradaiso, kuipa ndi kuvutika zafunga kwa zaka zikwi zambiri?
2 Chifukwa chake chili chakuti Adamu ndi Hava anagwiritsira ntchito molakwa ufulu wawo wakudzisankhira. Iwo analephera kuzindikira chenicheni chakuti sanalengedwe kupeza chipambano mosadalira pa Mulungu ndi malamulo ake. Iwo anasankha kukhala osadalira pa Mulungu, akumaganiza kuti kutero kukawongolera miyoyo yawo. Chotero iwo analumpha malire aufulu wakudzisankhira operekedwa ndi Mulungu.—Genesis, chaputala 3.
Nkhani ya Ulamuliro Wachilengedwe Chonse
3-5. Kodi n’chifukwa ninji Mulungu sanangowononga Adamu ndi Hava ndi kuyambiranso?
3 Kodi n’chifukwa ninji Mulungu sanangowononga Adamu ndi Hava ndi kuyambiranso ndi anthu ena aŵiri? N’chifukwa chakuti ulamuliro wake wachilengedwe chonse, ndiko kuti, kuyenera kwake kwachikhalire kwa kulamulira, kunakayikiridwa.
4 Funso linali lakuti: Kodi ndani ali ndi kuyenera kwakulamulira, ndipo ndi ulamuliro wayani umene uli wolungama? Kukhala kwake wamphamvuyonse ndi Mlengi wazolengedwa zonse kumapatsa Mulungu kuyenera kwa kuzilamulira. Popeza kuti iye ali wanzeru zonse, ulamuliro wake n’ngwabwino kopambana kwa zolengedwa zonse. Komatu ulamuliro wa Mulungu tsopano unakayikiridwa. Ndiponso, kodi panali kanthu kena kolakwika ndi cholengedwa chake—munthu? Tidzapenda pambuyo pake mmene funso la umphumphu wa munthu likuloŵetsedweramo.
5 Mwa kukhala kwa munthu wosadalira pa Mulungu, funso lina linadzutsidwa lakuti: Kodi anthu akachita bwinopo ngati salamulidwa ndi Mulungu? Ndithudi Mlengi anadziŵa yankho, koma njira yotsimikizirika yoti anthu azindikire nayo inali kuwalola kukhala ndi ufulu wotheratuwo umene iwo anafuna. Iwo anasankha njirayo mwaufulu wawo wakusankha, chotero Mulungu anaulola.
6, 7. Kodi n’chifukwa ninji Mulungu walola anthu kukhala ndi ufulu wotheratu kwa nthaŵi yaitali chonchi?
6 Mwakupatsa anthu nthaŵi yokwanira ya kuyesa ufulu wawo wotheratu Mulungu akathetseratu makani a kuti kaya anthu angachite bwinopo molamulidwa ndi Mulungu kapena modzilamulira okha. Ndipo nthaŵi yololedwa ikafunikira kukhala yaitali mokwanira kulola anthu kufika pachimake pa zimene iwo analingalira kukhala zipambano zawo zandale zadziko, za maluso a zopangapanga (indasitale), za sayansi, ndi za mankhwala.
7 Chifukwa chake, Mulungu wapatsa anthu mwaŵi wokwanira kufikira kutsiku lathu kusonyeza popanda chikayikiro chilichonse kuti kaya ngati ulamuliro wa anthu wopanda Mulungu ungapambane. Chotero anthu akhoza kusankha pakati pa kukoma mtima ndi nkhalwe, pakati pa chikondi ndi chidani, pakati pa chilungamo ndi chisalungamo. Koma iwo akayang’anizananso ndi zotulukapo za chosankha chawo: ubwino ndi mtendere kapena kuipa ndi kuvutika.
Chipanduko cha Zolengedwa za Uzimu
8, 9. (a) Kodi chipanduko chinayamba motani m’chigawo chauzimu? (b) Kodi ndani kuphatikiza pa Adamu ndi Hava amene Satana anasonkhezera kupanduka?
8 Palinso mfundo ina yoti ilingaliridwe. Makolo athu oyamba sanali okha amene anapandukira lamulo la Mulungu. Koma kodi wina ndani amene analiko pa nthaŵiyo? Zolengedwa zauzimu. Mulungu asanalenge anthu, analenga moyo wampangidwe wapamwamba, chiŵerengero chachikulu cha angelo, kukhala m’chigawo chakumwamba. Nawonso analengedwa ali ndi ufulu wakudzisankhira ndiponso ndikufunika kwa kugonjera kuulamuliro wa Mulungu.—Yobu 38:7; Salmo 104:4; Chivumbulutso 5:11.
9 Baibulo limasonyeza kuti chipanduko choyamba chinachitikira m’chigawo chauzimu. Cholengedwa chauzimu chinafuna ufulu wotheratu. Iye anafunadi anthu kumlambira. (Mateyu 4:8, 9) Wopanduka wauzimu ameneyu anafikira kukhala woyambitsa m’kusonkhezera Adamu ndi Hava kupanduka, akumanena bodza kuti Mulungu anali kuwamana kanthu kena kabwino. (Genesis 3:1-5) Chotero iye akutchedwa Mdyerekezi (Woneneza) ndi Satana (Wotsutsa). Pambuyo pake, iye anasonkhezera zolengedwa zina zauzimu kupanduka. Izo zinafikira kudziŵika monga ziŵanda.—Deuteronomo 32:17; Chivumbulutso 12:9; 16:14.
10. Kodi chotulukapo chachipanduko cha zolengedwa zaumunthu ndi zauzimu n’chiyani?
10 Anthu, mwakupandukira Mulungu, anadzigonjetsera kuchisonkhezero cha Satana ndi ziŵanda zake. Ndicho chifukwa chake Baibulo limatcha Satana “mulungu wanthaŵi yapansi pano,” amene “wachititsa khungu maganizo a osakhulupilira.” Chifukwa chake, Mawu a Mulungu amanena kuti “dziko lonse ligona m’mphamvu ya woipayo.” Yesu mwiniyo anatcha Satana “wolamulira wa dziko lino.”—2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19; Yohane 12:31.
Nkhani Ziŵiri
11. Kodi Satana anakayikira Mulungu pankhani ina iti?
11 Satana anadzutsa nkhani ina imene inakayikira Mulungu. Kwenikweni, iye ananeneza kuti Mulungu analakwa m’njira imene Iye analenga nayo anthu ndi kuti palibe aliyense amene akanafuna kuchita cholungama pamene ali pansi pa chitsenderezo. Kunena zowona, iye ananena kuti atakhala pansi pa chiyeso akatukwanadi Mulungu. (Yobu 2:1-5) Mwanjira iyi Satana anakayikira umphumphu wa anthu.
12-14. Kodi ndi motani mmene nthaŵi ikavumbulira chowonadi ponena za nkhani ziŵirizi zodzutsidwa ndi Satana?
12 Chifukwa chake, Mulungu walola nthaŵi yokwanira kuti zolengedwa zonse zaluntha ziwone mmene nkhaniyi kuphatikizapo nkhani ya ulamuliro wa Mulungu ikathetsedwera. (Yerekezerani ndi Eksodo 9:16.) Chochitika chotsirizira cha mbiri ya anthu chikavumbula chowonadi pankhani ziŵiri zimenezi.
13 Choyamba, kodi nthaŵi ikasonyezanji ponena za nkhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse, kuyenera kwa ulamuliro wa Mulungu? Kodi anthu akatha kudzilamulira okha bwino kwambiri koposa Mulungu? Kodi dongosolo lililonse la ulamuliro wa anthu losachokera kwa Mulungu likachititsa dziko lachimwemwe lopanda nkhondo, upandu, ndi chisalungamo? Kodi pali lililonse limene likachotsa umphaŵi ndi kupereka ulemerero kwa onse? Kodi pali lililonse limene likagonjetsa matenda, ukalamba, ndi imfa? Ulamuliro wa Mulungu unalinganizidwira kuchita zonsezo.—Genesis 1:26-31.
14 Ponena za nkhani yachiŵiri, kodi nthaŵi ikasonyezanji ponena za kuyenerera kwa cholengedwa chaumunthu? Kodi kunali kulakwa kuti Mulungu analenga anthu mwanjira imene anachitira? Kodi aliyense wa iwo akachita chinthu cholungama poyesedwa? Kodi anthu alionse akasonyeza kuti anafuna ulamuliro wa Mulungu mmalo mwa ulamuliro wodziimirira wa anthu?
[Chithunzi patsamba 13]
Mulungu wapereka nthaŵi yoti anthu afike pachimake cha zipambano zawo
[Mawu a Chithunzi]
Shuttle: Based on NASA photo