Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 10/8 tsamba 8-9
  • Chifukwa Chimene Mulungu Analola Kuvutika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chimene Mulungu Analola Kuvutika
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwiritsira Molakwa Ufuluwo
  • Chimene Kupita Kwanthaŵi Kukuphunzitsa
  • Kodi N’chiyani Chakhala Chotulukapo Chachipanduko?
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Chifukwa Chake Mulungu Walola Kuvutika
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Nthaŵi Yomwe Mulungu Walola Anthu Kuvutika Ili Pafupi Kutha
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kodi Nchifukwa Ninji Kuvutika ndi Chisalungamo Zili Zochuluka Motero?
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 10/8 tsamba 8-9

Chifukwa Chimene Mulungu Analola Kuvutika

‘Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize.’—Yeremiya 10:23, 24.

MAWU amenewo analembedwa zaka zikwi zambiri pambuyo pa kulengedwa kwa anthu. Yeremiya anazindikira kuti mpaka kudzafika m’tsiku lake, mbiri ya anthu inali yatsoka yokha yokha itayerekezedwa ndi chiyambi chabwino chimene Mulungu anapatsa makolo athu oyambirira.

Malingaliro a Yeremiya achilikizidwa ndi zaka zowonjezereka zoposa 2,500 chiyambire nthaŵi yake. Tsoka la anthu laposapo kuipa. Kodi chinalakwika nchiyani?

Kugwiritsira Molakwa Ufuluwo

Makolo athu oyambirira anaiwala nsonga yakuti iwo sanalengedwe kuti apite patsogolo pawokha popanda Mulungu ndi malamulo ake. Iwo anasankhapo kukhala opatuka kwa Mulungu ndi kudziimira pawokha, akumaganiza kuti kuteroko kukawongolera miyoyo yawo. Komatu uku kunali kuwugwiritsira molakwa ufulu wawo. Iwo anakaponda kunja kwa mabande oikidwa ndi Mulungu a ufulu.—Genesis, mutu 3.

Kodi nchifukwa ninji Mulungu sanangowononga Adamu ndi Hava ndi kuyambanso ndi banja lina la anthu? Chifukwa chakuti ulamuliro wake wa chilengedwe chonse ndi njira yake ya kulamulira inakaikiridwa. Kukhala kwake Mulungu Wamphamvuyonse ndi Mlengi wa zolengedwa zonse kumampatsa iye kuyenerera kwa kuzilamulira. Popeza kuti iye Ngwanzeru Zonse, kulamulira kwake nkwabwino ku zolengedwa zonse. Koma kulamulira kwa Mulungu tsopano kunatokosedwa.

Kodi anthu akachita bwinopo kuposa kulamulidwa ndi Mulungu? Mlengi anadziŵadi yankho la funso limenelo. Njira yotsimikizirika yakuti anthu atsimikizire inali kungowalola ufulu wopanda polekezera umene anaukhumbawo. Chotero, chifukwa chimodzi, pakati pa zambiri, chimene Mulungu walolera kuipa ndi kuvutika ndicho kusonyeza mosakaikira kaya kulamulira kwa anthu kodziimira pawokha kwa iye kukakhala ndi chipambano.a

Adamu ndi Hava anadzibweretsera kuvutika okha ndi mbadwa zawo. Iwo ‘anatuta zimene anafesa.’ (Agalatiya 6:7) ‘Anamchitira zovunda si ndiwo ana ake [a Mulungu], chirema nchawo.’—Deuteronomo 32:5.

Makolo athu oyambirira anachenjezedwa kuti kudziimira pawokha kuchoka pa kulamulidwa ndi Mulungu kukatulukapo imfa kwa iwo. (Genesis 2:17) Ichi chinatsimikizira kukhala chowona. Mwa kumusiya Mulungu, iwo anasiya magwero awo a thanzi ndi moyo. Iwo anafokerafokera kufikira imfa inawapha.—Genesis 3:19.

Pambuyo pake, Mulungu analola nthaŵi yokwanira kuti banja la anthu lidzisonyeze mokwanira kaya dongosolo lirilonse la ndale zadziko, lamayanjano, kapena lachuma limene iwo angapange popanda kulamulira kwake lingatsimikizire kukhala lokhutiritsa mokwanira. Kodi lirilonse la madongosolowa lingabweretse dziko lachimwemwe, lamtendere lopanda upandu kapena nkhondo? Kodi lirilonse la awa lingapange kukhupuka kwa zinthu zakuthupi kaamba ka onse? Kodi lirilonse la awa lingagonjetse matenda, ukalamba, ndi imfa? Ufumu wa Mulungu udalinganizidwa kuthetsa zinthu zonsezi.—Genesis 1:26-31.

Chimene Kupita Kwanthaŵi Kukuphunzitsa

Posachedwapa mbiri inamveketsa chowonadi cha pa Aroma 5:12 ichi: “Imfa inafikira anthu onse.” Vesi limeneli likulongosola kuti ‘uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo.’ Pamene makolo athu oyambirira anagalukira kulamulira kwa Mulungu, iwo anakhala olemala, opanda ungwiro. Chiremachi nchimene iwo ankachipatsira kwa ana awo. Monga chotulukapo, tonsefe takhala tikubadwa olemala, okhoterera kudwala ndi kufa.

Kupita kwanthaŵi kwavumbulanso mmene anthu ogwidwa ndi uchimo amachitirana mowopsya okhaokha. Pakhala nkhondo zowopsya zambirimbiri, chidani chaufuko ndi chachipembedzo, zilango zankhanza, upandu woipa wa mtundu uliwonse, ndi machitidwe adyera ndi aumbombo. Ndiponso, umphaŵi ndi njala zakhalitsa mnkhole anthu mamiliyoni osaŵerengeka.

M’zaka zikwi zambiri zapitazo, anthu ayesera mtundu wokhutiritsa uliwonse wa boma. Komabe, limodzi ndi limodzi la awa lalephera kukhutiritsa zosowa za anthu. Posachedwapa, maboma Achikomyunizimu akhala akukanidwa m’maiko ambiri. M’maiko a ufumu wa democracy mulinso upandu wofalikira, umphaŵi, m’gwedegwede wachuma, ndi ziphuphu. Ndithudi, mitundu yonse ya maboma a anthu yatsimikizira kukhala yoperewera.

Kuwonjezera apa, Mulungu walola nthaŵi kwa anthu kufikira pamwamba pa zotumba zawo za sayansi ndi zinthu zakuthupi. Koma kodi kumeneku nkupitadi patsogolo pamene nthungo ndi uta zalowedwa mmalo ndi mamisaelo a nyukiliya? pamene anthu angapange ulendo wonka mumlengalenga komano osakhalira pamodzi mumtendere padziko lapansi? pamene anthu mamiliyoni ambiri amawopa kutulukira panja usiku chifukwa cha upandu?

Chimene kuyesedwa kwanthaŵiyi kwasonyeza nchakuti nkosathekeranso kwa anthu ‘kulongosola mapazi awo’ mwachipambano monga mmene kuliri kosatheka kwa iwo kukhala opanda zakudya, madzi, ndi mpweya. Ife tinalinganizidwira kudalira pa chitsogozo cha Mpangi wathu motsimikizirikadi monga mmene tinalengedwera kudalira pa zakudya, madzi, ndi mpweya.—Mateyu 4:4.

Mwa kulola kuipa ndi kuvutika, Mulungu wazisonyeza zotulukapo zachisoni za kugwiritsira molakwa ufuluwo kosadzabwerezanso. Iyi ndi mphatso ya mtengo wapatali kwenikweni kuti mmalo mwa kulanda ufuluwu mwa anthu, Mulungu waŵalola iwo kuwona mmene kuwugwiritsira ntchito molakwa kumatanthauza.

Ponena zaufuluwu, bukhu lakuti “Statement of Principles of Conservative Judaism” likuti: “Patapanda kukhala kuthekera kwenikweni kwa kupanga chosankha cholakwika kwa anthu atayang’anizana ndi chinthu chabwino ndi choipa, liwu lenileni la chosankha limakhala lopanda tanthauzo. . . . Kuvutika kwambiri kwa anthu m’dziko kumachititsidwa mwachindunji ndi kugwiritsira kwathu molakwa ufulu wopatsidwa kwa ife.”

Motsimikizirikadi, Yeremiya anali wolondola pamene anati: ‘Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’ Ndipo Solomo nayenso anali wolondola pamene anati: ‘Wina apweteka mnzake pomlamulira.’—Mlaliki 8:9.

Mwachigogogo, ichi chimafotokoza mwafanizo kusathekera kwa munthu kuthetsa kuvutika! Ngakhale Solomo, ndi nzeru zake zonsezo, chuma ndi mphamvu sanathe kuwongolera chisoni chochokera m’kulamulira kwa munthu.

Nangano, kodi ndimotani mmene Mulungu adzabweretsera mapeto a kuvutika? Kodi iye adzawalipira anthu kaamba ka kuvutika kwawo kwakumbuyo?

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka kufotokozedwa kokwanira kwa nkhani zonse zophatikizidwa, onani bukhu lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, mitu 11 ndi 12, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 9]

Mulungu anawapatsa anthu chiyambi changwiro, koma mbiri yakale yasonyeza kuti atadziimira pawokha popanda Mulungu, anthu sangathe ‘kulongosola mapazi awo’ mwachipambano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena