Phunziro 7
Kuyandikira kwa Mulungu m’Pemphero
Kodi n’chifukwa ninji kupemphera nthaŵi zonse kuli kofunika? (1)
Kodi tiyenera kupemphera kwa yani, ndipo motani? (2, 3)
Kodi nkhani zoyenera kupempherera n’zotani? (4)
Kodi muyenera kupemphera liti? (5, 6)
Kodi Mulungu amamva mapemphero onse? (7)
1. Pemphero ndilo kulankhula kwa Mulungu modzichepetsa. Muyenera kupemphera kwa Mulungu nthaŵi zonse. Mwa kutero mungamve kukhala pafupi naye kwambiri monga bwenzi lapamtima. Yehova ali wamkulukulu ndi wamphamvu koposa, koma amamvetsera mapemphero athu! Kodi mumapemphera kwa Mulungu nthaŵi zonse?—Salmo 65:2; 1 Atesalonika 5:17.
2. Pemphero ndi mbali ya kulambira kwathu. Chifukwa chake, tiyenera kupemphera kwa Yehova Mulungu yekha. Pamene Yesu anali padziko lapansi, nthaŵi zonse anapemphera kwa Atate wake, osati kwa wina aliyense. Tiyenera kuchita chimodzimodzi. (Mateyu 4:10; 6:9) Komabe, mapemphero athu onse ayenera kuperekedwa m’dzina la Yesu. Izi zimasonyeza kuti timalemekeza malo a Yesu ndi kuti tili ndi chikhulupiriro m’nsembe yake ya dipo.—Yohane 14:6; 1 Yohane 2:1, 2.
3. Popemphera tiyenera kulankhula ndi Mulungu kuchokera mumtima. Sitiyenera kupereka mapemphero oloŵeza pamtima kapena kuwaŵerenga m’buku la mapemphero ayi. (Mateyu 6:7, 8) Tingapemphere tili mumkhalidwe uliwonse wolemekezeka, nthaŵi iliyonse, ndipo kulikonse. Mulungu amamva ngakhale mapemphero achinsinsi operekedwa chamumtima. (1 Samueli 1:12, 13) Ndi bwino kupeza malo abata kopanda munthu aliyense kumene tingaperekere mapemphero athu aumwini.—Marko 1:35.
4. Kodi ndi nkhani zotani zimene mungapempherere? Chilichonse chokhudza ubwenzi wanu ndi iye. (Afilipi 4:6, 7) Pemphero lachitsanzo limasonyeza kuti tiyenera kupempherera dzina la Yehova ndi chifuno chake. Tingapemphenso kuti atipatse zosoŵa zathu zakuthupi, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kuti atithandize kukaniza ziyeso. (Mateyu 6:9-13) Mapemphero athu sayenera kukhala adyera. Tiyenera kupempherera kokha zinthu zimene zimagwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.—1 Yohane 5:14.
5. Mungapemphere nthaŵi iliyonse imene mtima wanu ukusonkhezerani kuyamika kapena kutamanda Mulungu. (1 Mbiri 29:10-13) Muyenera kupemphera pamene muli ndi mavuto ndi pamene chikhulupiriro chanu chikuyesedwa. (Salmo 55:22; 120:1) Kuli bwino kupemphera musanadye chakudya. (Mateyu 14:19) Yehova amatipempha kupemphera “nthaŵi yonse.”—Aefeso 6:18.
6. Tifunika kupemphera makamaka pamene tachita tchimo lalikulu. Panthaŵi zotero tiyenera kupempha Yehova kuti atichitire chifundo ndi kutikhululukira. Ngati timuululira machimo athu ndi kuchita zonse zotheka kuti tisawabwerezenso, Mulungu ali ‘wokonzeka kukhululukira.’—Salmo 86:5; Miyambo 28:13.
7. Yehova amamva mapemphero a anthu olungama okha. Kuti Mulungu amve mapemphero anu, muyenera kumayesetsa kutsatira malamulo ake. (Miyambo 15:29; 28:9) Muyenera kudzichepetsa popemphera. (Luka 18:9-14) Mufunika kugwirira ntchito pa zimene mukupempherera. Mukatero, mudzasonyeza kuti muli ndi chikhulupiriro ndi kuti mukufunadi zimene mukupemphazo. Mpokhapo pamene Yehova adzayankha mapemphero anu.—Ahebri 11:6.