Phunziro 10
Machitachita Amene Mulungu Amadana Nawo
Kodi muyenera kuziona motani zinthu zimene Mulungu amati n’zoipa? (1)
Kodi ndi mitundu iti ya kugonana imene ili yolakwa? (2)
Kodi Mkristu ayenera kuona motani kunama? (3) juga? (3) kuba? (3) chiwawa? (4) kukhulupirira mizimu? (5) kuledzera? (6)
Kodi ndi motani mmene munthu angamasukire ku machitachita oipa? (7)
1. Atumiki a Mulungu amakonda chabwino. Koma ayeneranso kuphunzira kudana nacho choipa. (Salmo 97:10) Zimenezo zimatanthauza kupeŵa machitachita amene Mulungu amawada. Kodi ena a machitachita amenewo ngotani?
2. Chisembwere: Kugonana popanda ukwati, chigololo, kugona nyama, kugonana ndi wachibale, ndi mathanyula zonsezo zili machimo aakulu kwa Mulungu. (Levitiko 18:6; Aroma 1:26, 27; 1 Akorinto 6:9, 10) Ngati mwamuna ndi mkazi ali osakwatirana koma akukhala pamodzi, ayenera kupatukana kapena kukwatirana mwa lamulo.—Ahebri 13:4.
3. Kunama, Juga, Kuba: Yehova Mulungu sanama. (Tito 1:2) Anthu amene afuna chiyanjo chake ayenera kupeŵa kunama. (Miyambo 6:16-19; Akolose 3:9, 10) Juga yamtundu uliwonse ndi dyera. Chotero Akristu satengamo mbali m’juga yamtundu uliwonse, monga malotale, juga ya mahachi, ndi bingo. (Aefeso 5:3-5) Ndipo Akristu samaba. Iwo sagula katundu amene akudziŵa kuti ngwakuba kapena kutenga zinthu popanda chilolezo.—Eksodo 20:15; Aefeso 4:28.
4. Kupsa Mtima, Chiwawa: Mkwiyo wosalamulirika ungatsogolere ku chiwawa. (Genesis 4:5-8) Munthu wachiwawa sangakhale bwenzi la Mulungu. (Salmo 11:5; Miyambo 22:24, 25) Kulipsira kapena kubwezera choipa pa zoipa zimene ena angatichitire nkulakwa.—Miyambo 24:29; Aroma 12:17-21.
5. Matsenga ndi Kukhulupirira Mizimu: Anthu ena amanenerera mphamvu ya mizimu pofuna kuchiritsa nthenda. Ena amalodza adani awo kuwadwalitsa kapena ngakhale kuwapha. Mphamvu imene ili kumbuyo kwa machitachita onsewa ndi Satana. Chotero Akristu sayenera konse kutengamo mbali m’zilizonse za zimenezi. (Deuteronomo 18:9-13) Kukhala pafupi ndi Yehova ndiko chitetezo chenicheni pamene ena afuna kutilodza.—Miyambo 18:10.
6. Kuledzera: Kumwa pang’ono vinyo, moŵa, kapena chakumwa chaukali china, sikulakwa. (Salmo 104:15; 1 Timoteo 5:23) Koma kumwetsa ndi kuledzera ndiko kulakwa pamaso pa Mulungu. (1 Akorinto 5:11-13; 1 Timoteo 3:8) Kumwetsa moŵa kungawononge thanzi lanu ndi kusokoneza banja lanu. Kungakuchititseninso kugonja msanga paziyeso zina.—Miyambo 23:20, 21, 29-35.
7. Anthu amene amachita zinthu zimene Mulungu amati n’zoipa “sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.” (Agalatiya 5:19-21) Ngati mumakondadi Mulungu ndipo mukufuna kumkondweretsa, mukhoza kuwonjoka ku machitachita ameneŵa. (1 Yohane 5:3) Phunzirani kuda zimene Mulungu amati n’zoipa. (Aroma 12:9) Yanjanani ndi anthu amene ali ndi zizoloŵezi zaumulungu. (Miyambo 13:20) Mabwenzi okhwima achikristu angakuthandizeni. (Yakobo 5:14) Koposa zonse, dalirani chithandizo cha Mulungu mwa pemphero.—Afilipi 4:6, 7, 13.
[Zithunzi pamasamba 20, 21]
Mulungu amadana ndi kuledzera, kuba, juga, ndi machitachita achiwawa