Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gf phunziro 14 tsamba 22-23
  • Mabwenzi a Mulungu Amapeŵa Zoipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mabwenzi a Mulungu Amapeŵa Zoipa
  • Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Nkhani Yofanana
  • Machitachita Amene Mulungu Amadana Nawo
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tikondweretse Mulungu?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Chigawo 13
    Mverani Mulungu
  • Kodi Mulungu Adzawononganso Anthu Oipa?
    Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
gf phunziro 14 tsamba 22-23

PHUNZIRO 14

Mabwenzi a Mulungu Amapeŵa Zoipa

Satana amanyengerera anthu kuti achite zinthu zoipa. Munthu amene amafuna kukhala bwenzi la Mulungu ayenera kudana ndi zimene Yehova amadana nazo. (Salmo 97:10) Nazi zina mwa zimene mabwenzi a Mulungu amazipeŵa:

Zinthu zimene Yehova amadana nazo zimaphatikizapo kuchita machimo a chiwerewere, kuledzera, kuchotsa mimba, kuba, kunama, kukwiya mopitirira malire komanso njuga

Machimo a chiwerewere. “Usachite chigololo.” (Eksodo 20:14) Kugonana ukwati usanachitike ndi tchimonso.—1 Akorinto 6:18.

Kuledzera. “Oledzera . . . sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:10.

Umbanda, Kuchotsa mimba. “Usaphe.”—Eksodo 20:13.

Kuba. “Usabe.”—Eksodo 20:15.

Kunama. Yehova amadana ndi “lilime lonama.”—Miyambo 6:17.

Chiwawa ndi Mkwiyo Wopitirira. ‘Yehova adana ndi iye wakukonda chiwawa.’ (Salmo 11:5) “Ntchito za thupi [zimaphatikizapo] . . . zopsa mtima.”—Agalatiya 5:19, 20.

Njuga. “Musayanjane ndi . . . wosirira [mwadyera].”—1 Akorinto 5:11.

Chidani chosankhana fuko ndi mtundu. “Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.”—Mateyu 5:43, 44.

Zinthu zimene Mulungu amatiuza zimakhala kaamba ka ubwino wathu. Nthaŵi zina kumakhala kovuta kupeŵa zinthu zoipa. Koma ndi chithandizo cha Yehova komanso cha Mboni zake, mukhoza kupeŵa kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo.—Yesaya 48:17; Afilipi 4:13; Ahebri 10:24, 25.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena