Phunziro 14
Kakonzedwe ka Mboni za Yehova
Kodi Mboni za Yehova zamakono zinayamba liti? (1)
Kodi misonkhano ya Mboni za Yehova imachitika motani? (2)
Kodi ndalama zolipirira zinthu zimachokera kuti? (3)
Kodi ndani amene amatsogolera mumpingo? (4)
Kodi ndi misonkhano yaikulu iti imene imachitika chaka ndi chaka? (5)
Kodi kumalikulu ndi kumaofesi awo a nthambi kumachitika ntchito yotani? (6)
1. Mboni za Yehova zamakono zinayamba m’ma 1870. Poyamba, zinali kutchedwa Ophunzira Baibulo. Koma mu 1931 zinalandira dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova. (Yesaya 43:10) Kuchokera pachiyambi chochepa gululi lakula kufikira Mboni zokwana mamiliyoni, zimene zili zokangalika kulalikira m’maiko oposa 230.
2. Mipingo yambiri ya Mboni za Yehova imakhala ndi misonkhano katatu pamlungu. Muli aufulu kupezekapo pa uliwonse wa imeneyi. (Ahebri 10:24, 25) Zimene amaphunzira zimachokera m’Baibulo. Misonkhano imayamba ndi kutha ndi pemphero. Ndiponso “nyimbo zauzimu” zokhudza mtima zimaimbidwa pamisonkhano yawo yambiri. (Aefeso 5:18, 19) Kuloŵa n’kwaulere, ndipo sipamayendetsedwa mbale ya zopereka.—Mateyu 10:8.
3. Mipingo yambiri imachitira misonkhano yawo m’Nyumba za Ufumu. Izo nthaŵi zambiri zimakhala nyumba zabwino zomangidwa ndi Mboni zimene zili antchito odzifunira. Simudzaonamo mafano, mitanda, kapena zinthu zina zonga zimenezo m’Nyumba ya Ufumu. Ndalama zolipirira zinthu zimachokera m’zopereka zaufulu. Kwa aja amene afuna kuchita zopereka, pamakhala bokosi la zopereka.—2 Akorinto 9:7.
4. Mumpingo uliwonse, muli akulu, kapena oyang’anira. Iwo amatsogolera pakuphunzitsa mumpingo. (1 Timoteo 3:1-7; 5:17) Amathandizidwa ndi atumiki otumikira. (1 Timoteo 3:8-10, 12, 13) Amuna ameneŵa sali pamwamba pa ena onse mumpingo. (2 Akorinto 1:24) Iwo samapatsidwa maina apadera aulemu. (Mateyu 23:8-10) Samavala zosiyana ndi ena. Ndipo samalipiridwa pa ntchito yawo. Akuluwo mwaufulu amasamalira zosoŵa zauzimu za mpingo. Amapereka chitonthozo ndi chitsogozo panthaŵi za mavuto.—Yakobo 5:14-16; 1 Petro 5:2, 3.
5. Mboni za Yehova zimachitanso misonkhano yaikulu kapena misonkhano yachigawo chaka ndi chaka. Panthaŵi imeneyi mipingo yambiri imasonkhana kudzamvetsera pulogalamu yapadera ya chilangizo cha Baibulo. Ubatizo wa ophunzira atsopano umakhalapo nthaŵi zonse papulogalamu ya msonkhano wadera kapena wachigawo.—Mateyu 3:13-17; 28:19, 20.
6. Malikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova ali ku New York. Kumeneko kuli Bungwe Lolamulira, kagulu kapakati ka akulu achidziŵitso amene amayang’anira mpingo wa dziko lonse. Palinso maofesi a nthambi oposa 100 padziko lonse. Kumalo ameneŵa, antchito odzifunira amathandiza kusindikiza ndi kutumiza mabuku a Baibulo. Ndiponso malangizo amaperekedwa olinganizira ntchito yolalikira. Bwanji osakonza ulendo wokacheza ku ofesi ya nthambi imene ili pafupi ndi kwanu?