Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jt tsamba 25-26
  • Gulu Lawo la Padziko Lonse ndi Ntchito Yawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gulu Lawo la Padziko Lonse ndi Ntchito Yawo
  • Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
  • Nkhani Yofanana
  • Oyang’anira Amene Amaweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Kakonzedwe ka Mboni za Yehova
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Gulu Lowoneka la Mulungu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
jt tsamba 25-26

Gulu Lawo la Padziko Lonse ndi Ntchito Yawo

PALI njira zambiri zogwiritsidwa ntchito poyendetsa ntchito yochitira umboni m’mayiko opitirira 230 mmene ikuchitika. Utsogoleri wonse umachokera ku Bungwe Lolamulira ku likulu la dziko lonse ku Brooklyn, New York. Bungwe Lolamulira limatumiza nthumwi zake chaka chilichonse kumadera osiyanasiyana padziko lonse kukakambirana ndi oimira maofesi a nthambi kumadera amenewo. Pa maofesi anthambi, pamakhala Makomiti a Nthambi okhala ndi mamembala ochokera pa atatu mpaka seveni amene amayang’anira ntchitoyo m’mayiko omwe akuwayang’anira. Maofesi ena anthambi ali ndi fakitale yosindikizira mabuku, ndipo ena ali ndi makina osindikizira amakono kwambiri. Dziko kapena dera limene limayang’aniridwa ndi nthambi iliyonse limagaŵidwa m’zigawo, ndipo zigawozo zimagaŵidwanso m’madera. Dera lililonse limakhala ndi mipingo pafupifupi 20. Woyang’anira chigawo amayendera madera m’chigawo chake. M’dera lililonse mumachitika misonkhano ikuluikulu iŵiri pachaka. Palinso woyang’anira dera, ndipo iye amayendera mpingo uliwonse m’dera lake nthaŵi zambiri kaŵiri pachaka, akumathandiza Mbonizo kulinganiza ndi kuchita ntchito yolalikira m’gawo lopatsidwa mpingo wawo.

Mpingo wawo umene uli kwanuko limodzi ndi Nyumba ya Ufumu ndilo phata lolengezera uthenga wabwino m’dera lanu. Dera la mpingo uliwonse limagaŵidwa m’magawo ang’onoang’ono. Magawo ameneŵa amapatsidwa kwa mmodzi ndi mmodzi wa Mbonizo amene amayesetsa kuchezera anthu panyumba iliyonse m’gawo lake. Mpingo uliwonse, wokhala ndi Mboni zoyambira pa zingapo kufika m’ma 200, umakhala ndi akulu amene amayang’anira ntchito zosiyanasiyana. Aliyense wa alengezi a uthenga wabwino amakhala wofunika kwambiri m’gulu la Mboni za Yehova. Aliyense wa Mboni za Yehova, kaya akutumikira ku likulu la dziko lonse, pamaofesi anthambi, kapena mumpingo, amagwirabe ntchito yolalikira m’munda akumauza ena za Ufumu wa Mulungu.

Malipoti a ntchito imeneyi potsirizira pake amakafika ku likulu la dziko lonse, ndipo buku la pachaka lotchedwa Yearbook limalembedwa ndi kufalitsidwa. Ndiponso, pamakhala lipoti limene limafalitsidwa chaka chilichonse m’magazini ya Nsanja ya Olonda ya January 1. Mabuku aŵiri ameneŵa amasonyeza zonse zimene Mboni zimachita chaka chilichonse pochitira umboni za Yehova ndi Ufumu wake wokhala m’manja mwa Kristu Yesu. M’zaka zaposachedwapa, Mbonizo limodzi ndi anthu okhala ndi chidwi, onse pamodzi okwanira pafupifupi 14,000,000, akhala akumafika chakha chilichonse pa mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Mboni za Yehova zimawononga maola opitirira 1,000,000,000 chaka chilichonse polengeza uthenga wabwino, ndipo atsopano opitirira 300,000 amabatizidwa. Zimagaŵira mabuku mamiliyoni mazanamazana.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena