Buku Lofalitsidwa Kopambana pa Dziko Lonse Lapansi
“Baibulo ndi buku limene anthu ambiri kopambana aliŵerenga m’mbiri yonse. . . . Makope ambiri a Baibulo afalitsidwa koposa buku lina lililonse. Ndiponso, Baibulo latembenuzidwa mobwerezabwereza kwambiri m’zinenero zambiri koposa buku lina lililonse.”—“The World Book Encyclopedia.”1
M’ZINTHU zina, mabuku ochuluka amachita ngati anthu. Amaonekera, ndiyeno angatchuke, ndiponso—kusiyapo mabuku angapo a akatswiri—nkukalamba ndi kufa. Nthaŵi zambiri malaibulale amakhala ngati manda a mabuku ambirimbiri amene anatha ntchito, amene saŵerengedwa, ndipo, mwa njira imeneyo, ngakufa.
Komabe, Baibulo nlosiyana kwambiri ndi mabuku a akatswiri omwe. Ngakhale kuti makope ake oyamba analembedwa zaka 3,500 zapitazo, lidakali lamoyo kwambiri. Ndilo buku lofalitsidwa kopambana padziko lapansi.a Chaka chilichonse, makope ngati 60 miliyoni a Baibulo lathunthu kapena zigawo zake amafalitsidwa. Kope loyamba kusindikiza pamakina linalembedwa pamakina opangidwa ndi Mjeremani, Johannes Gutenberg cha ku ma 1455. Chiyambire nthaŵiyo, mabaibulo mamiliyoni zikwi zinayi (athunthu kapena zigawo zake) asindikizidwa. Kulibe buku lina lililonse, ngakhale la chipembedzo, limene lingafanane nalo mpang’ono pomwe.
Baibulo lilinso buku limene latembenuzidwa kopambana m’mbiri. Baibulo lathunthu kapena zigawo zake zatembenuzidwa m’zinenero zoposa 2,100.b Anthu oposa 90 peresenti mwa anthu onse padziko lapansi atha kupeza chigawo cha Baibulo m’chinenero chawo.2 Motero bukuli ladutsa malire ndi kuloŵa m’maiko ambiri ndipo lagwetsa zopinga zonga kusankhana fuko ndi mtundu.
Mwina ziŵerengero zokha sizingakupatseni chifukwa champhamvu chimene chingakusonkhezereni kulipenda Baibulo. Ngakhale ndi tero, ziŵerengero za makope ake amene afalitsidwa ndi kutembenuzidwa zimachititsa chidwi, kutsimikiza kuti Baibulo lakopa anthu a mtundu uliwonse. Inde, buku limeneli limene anthu amagula kwambiri kuposa onse ndiponso limene latembenuzidwa kopambana m’mbiri yonse ya munthu muyenera kulipenda.
[Mawu a M’munsi]
a Anthu amalingalira kuti buku lachiŵiri lofalitsidwa kopambana ndilo kabuku kofiira kakuti Quotations From the Works of Mao Tse-tung, kamene makope ake okwana ngati 800 miliyoni agulitsidwa kapena kufalitsidwa.
b Ziŵerengero za zinenerozo zatengedwa pa ziŵerengero zofalitsidwa ndi United Bible Societies.
[Chithunzi patsamba 6]
Baibulo la Gutenberg, m’Chilatini, buku lathunthu loyamba kusindikizidwa pamakina