Zimene Zili m’Bukulo
Munthu poloŵa m’laibulale nthaŵi yoyamba angadodome poona kuchuluka kwa mabuku. Koma atangomfotokozera pang’ono dongosolo la maikidwe a mabukuwo, iye amadziŵa mwamsanga mmene angapezere zomwe akufuna. Momwemonso, kufunafuna zina zake m’Baibulo kumakhala kwapafupi ndithu ngati mukudziŵa dongosolo la maikidwe a zamkati mwake.
LIWU lakuti “Baibulo” lachokera ku liwu lachigiriki lakuti bi·bliʹa, limene linatanthauza “mipukutu yagumbwa” kapena “mabuku.”1 Kwenikweni Baibulo ndi nkhokwe—laibulale—ya mabuku 66, amene analembedwa pazaka ngati 1,600, kuyambira chaka cha 1513 B.C.E. mpaka pafupifupi chaka cha 98 C.E.
Mabuku 39 oyambirira, amene amapanga pafupifupi zitatu mwa zigawo zinayi za zimene zili m’Baibulo, amatchedwa Malemba Achihebri, pakuti analembedwa makamaka m’chinenerocho. Mabuku ameneŵa tingawagaŵe mwachisawawa m’magulu atatu: (1) Mbiri, Genesis mpaka Estere, mabuku 17; (2) Ndakatulo, Yobu mpaka Nyimbo ya Solomo, mabuku 5; ndi (3) Ulosi, Yesaya mpaka Malaki, mabuku 17. Malemba Achihebri amafotokoza za mbiri yoyambirira ya dziko lapansi ndi ya anthu limodzinso ndi mbiri ya mtundu wakale wa Israyeli kuchokera pamene unayamba mpaka zaka za zana lachisanu B.C.E.
Mabuku enawo 27 amatchedwa Malemba Achigiriki Achikristu, pakuti analembedwa m’Chigiriki, chinenero cha dziko lonse panthaŵiyo. Kwenikweni iwo aikidwa m’dongosolo la nkhani zake: (1) mabuku 5 a mbiri—Mauthenga Abwino ndi Machitidwe, (2) makalata 21, ndipo (3) Chivumbulutso. Malemba Achigiriki Achikristu amafotokoza ziphunzitso ndi ntchito za Yesu Kristu ndi za ophunzira ake m’zaka za zana loyamba C.E.