Kodi Amakhulupirira Chiyani?
A MBONI ZA YEHOVA amakhulupirira Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi. Zinthu za chilengedwe zodabwitsa kwambiri zotizinga zimaonetsa kuti chilengedwechi chinapangidwa ndi Mlengi wanzeru ndi wamphamvu kwambiri. Monga mmene ntchito za amuna ndi akazi zimaonetsera maluso awo, zimateronso ntchito za Yehova Mulungu. Baibulo limatiuza kuti “chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake . . . popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.” Ndiponso, popanda mawu, “zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 1:20; Salmo 19:1-4.
Anthu saumba mbiya kapena kupanga mawailesi akanema ndi makompyuta popanda cholinga. Dziko lapansi limodzi ndi zolengedwa zake, zomera ndi nyama n’zodabwitsa kwambiri kuposa zonsezo. Kapangidwe ka thupi la munthu limodzi ndi mamiliyoni mamiliyoni a maselo ake n’zosatheka ifeyo kuzimvetsa—ngakhale ubongo weniweniwo umene timaganiza nawo n’ngwodabwitsa moti sititha kuumvetsa! Ngati anthu amakhala ndi cholinga popanga zinthu zawo zosadabwitsa kwenikwenizo, kunena zoona Yehova Mulungu ayenera kuti anali ndi cholinga polenga zinthu zodabwitsazo! Miyambo 16:4 imati iye ali nacho cholinga mwakunena kuti: “Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zawo.”
Yehova anali ndi cholinga popanga dziko lapansi, monga momwe anauzira anthu aŵiri oyamba kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, . . . , mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwaŵa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Chifukwa chakuti anthu aŵiri oyambawo sanamvere, analephera kudzaza dziko lapansi ndi mabanja olungama amene akanasamalira bwino dziko lapansi limodzi ndi zomera ndi nyama zake. Koma kulephera kwawo sikunalepheretsenso cholinga cha Yehova. Patapita zaka zikwi zambirimbiri, olemba Mawu analemba kuti: “Mulungu amene anaumba dziko lapansi . . . , sanalilenga mwachabe.” Iye “analiumba akhalemo anthu.” Silidzawonongedwa, koma ‘dziko likhalabe masiku onse.’ (Yesaya 45:18; Mlaliki 1:4) Cholinga cha Yehova popanga dziko lapansi chidzakwaniritsidwa: “Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.”—Yesaya 46:10.
Chotero, Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti dziko lapansi lidzakhapo ku nthaŵi zonse ndipo anthu onse, amoyo ndi akufa, amene adzayenerera cholinga cha Yehova chokhazikitsira dziko lapansi lokongola, adzakhalapo ndi moyo kosatha. Anthu onse analandira kupanda ungwiro kuchokera kwa Adamu ndi Hava, choncho onse ndi ochimwa. (Aroma 5:12) Baibulo limatiuza kuti: “Mphoto yake ya uchimo ndi imfa.” “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Aroma 6:23; Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4, 20) Koma ndi motani mmene iwo angakhalirenso ndi moyo ndi kulandira nawo madalitso a m’dziko lapansi? Ndi kokha mwa nsembe ya dipo la Kristu Yesu, pakuti iye anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” “Onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu ake, nadzatulukira.”—Yohane 5:28, 29; 11:25; Mateyu 20:28.
Kodi zimenezi zidzatheka motani? Zafotokozedwa mu “uthenga wabwino wa Ufumu,” umene Yesu anayamba kuulalikira pamene anali padziko lapansi. (Mateyu 4:17-23) Koma lerolino, Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wabwino m’njira yapadera kwambiri.
[Tchati patsamba 13]
ZIMENE A MBONI ZA YEHOVA AMAKHULUPIRIRA
Zimene Amakhulupirira Zifukwa za M’malemba
Baibulo ndi Mawu a Mulungu 2 Tim. 3:16, 17;
ndipo ndiwo choonadi 2 Pet. 1:20, 21; Yoh. 17:17
Baibulo n’lodalirika Mat. 15:3; Akol. 2:8
kuposa miyambo
Dzina la Mulungu ndi Yehova Salmo 83:18; Yes. 26:4; 42:8; Eks. 6:3
Kristu ndi Mwana wa Mulungu Mat. 3:17; Yoh. 8:42;
Kristu anali woyamba kulengedwa Akol. 1:15; Chiv. 3:14
pa zolengedwa zonse za Mulungu
Kristu anafera pa mtengo Agal. 3:13; Mac. 5:30
wowongoka, osati pa mtanda
Moyo waumunthu wa Kristu Mat. 20:28; 1 Tim. 2:5, 6;
unalipiridwa monga dipo 1 Pet. 2:24
m’malo mwa anthu omvera
Nsembe ya Kristu imodzi Aroma 6:10;
yokha inali yokwanira Aheb. 9:25-28
Kristu anaukitsidwa kwa akufa 1 Pet. 3:18; Aroma 6:9;
monga munthu wauzimu wosafa Chiv. 1:17, 18
Tsopano tikukhala mu ‘nthaŵi Mat. 24:3-14; 2 Tim. 3:1-5;
yamapeto’ Luka 17:26-30
Ufumu wokhala m’manja mwa Yes. 9:6, 7; 11:1-5;
Kristu udzalamulira mwa Dan. 7:13, 14; Mat. 6:10
chilungamo ndi mtendere
Dziko lapansi silidzawonongedwa Mlal. 1:4; Yes. 45:18;
kapena kukhala lopanda anthu Salmo 78:69
Mulungu adzachotsa Chiv. 16:14, 16; Zef. 3:8;
maulamuliro amene alipoŵa Dan. 2:44; Yes. 34:2;
pankhondo ya Armagedo 55:10, 11
Oipa adzawonongedwa ndi Mat. 25:41-46;
kusadzakhalakonso 2 Ates. 1:6-9
Anthu oyanjidwa ndi Mulungu Yoh. 3:16; 10:27, 28;
adzalandira moyo wosatha 17:3; Marko 10:29, 30
Pali njira imodzi yokha ya ku moyo Mat. 7:13, 14; Aef. 4:4, 5
Imfa ya anthu inadza ndi Aroma 5:12; 6:23
tchimo la Adamu
Munthu yense pamodzi ndi Ezek. 18:4; Mlal. 9:10;
mzimu wake amathera pa imfa Salmo 6:5; 146:4;
Helo ndi manda a anthu onse Yobu 14:13;
Chiyembekezo cha akufa 1 Akor. 15:20-22;
n’cha kuukitsidwa Yoh. 5:28, 29; 11:25, 26
Imfa ya kwa Adamu idzatha 1 Akor. 15:26, 54;
Kagulu kankhosa 144,000 zokha Luka 12:32; Chiv. 14:1, 3;
ndiko kakupita kumwamba 1 Akor. 15:40-53;
kukalamulira limodzi ndi Kristu Chiv. 5:9, 10
A m’gulu la 144,000 amabadwanso 1 Pet. 1:23; Yoh. 3:3;
monga ana a Mulungu auzimu Chiv. 7:3, 4
Pangano latsopano limapangidwa Yer. 31:31; Aheb. 8:10-13
ndi Israyeli wauzimu
Mpingo wa Kristu unamangidwa Aef. 2:20; Yes. 28:16;
pa iyemwini Mat. 21:42
Mafano sayenera kugwiritsidwa Eks. 20:4, 5; Lev. 26:1;
ntchito polambira 1 Akor. 10:14;
Kukhulupirira zamizimu Deut. 18:10-12;
kuyenera kupeŵedwa Agal. 5:19-21; Lev. 19:31
Satana ndiye wolamulira 1 Yoh. 5:19; 2 Akor. 4:4;
dziko wosaoneka Yoh. 12:31
Mkristu sayenera kukhala 2 Akor. 6:14-17;
m’mabungwe ophatikiza 11:13-15; Agal. 5:9;
zipembedzo zosiyanasiyana Deut. 7:1-5
Mkristu ayenera kulekana ndi dziko Yak. 4:4; 1 Yoh. 2:15;
Malamulo onse a anthu amene Mat. 22:20, 21;
sawombana ndi malamulo 1 Pet. 2:12; 4:15
a Mulungu tiyenera kuwamvera
Kuloŵetsa magazi m’thupi Gen. 9:3, 4; Lev. 17:14;
kudzera m’kamwa kapena Mac. 15:28, 29
m’mitsempha ndi kuphwanya
malamulo a Mulungu
Malamulo a m’Baibulo onena 1 Akor. 6:9, 10;
za makhalidwe abwino Aheb. 13:4; 1 Tim. 3:2;
tiyenera kuwatsatira Miy. 5:1-23
Lamulo losunga Sabata Deut. 5:15; Eks. 31:13;
linaperekedwa kwa Aisrayeli Aroma 10:4; Agal. 4:9, 10;
okha ndipo linatha limodzi ndi Akol. 2:16, 17
Chilamulo cha Mose
Kukhala ndi gulu lapamwamba Mat. 23:8-12; 20:25-27;
la atsogoleri achipembedzo ndi Yobu 32:21, 22
mayina apamwamba aulemu
wapadera n’kosayenera
Munthu sanachite kusinthika Yes. 45:12; Gen. 1:27;
koma anachita kulengedwa Mat. 19:4
Kristu anapereka chitsanzo 1 Pet. 2:21; Aheb. 10:7;
chimene tiyenera kutengera Yoh. 4:34; 6:38
potumikira Mulungu
Ubatizo womiza thupi lonse Marko 1:9, 10; Yoh. 3:23;
m’madzi ndi chizindikiro Mac. 19:4, 5
cha kudzipatulira
Akristu amasangalala popereka Aroma 10:10; Aheb. 13:15;
poyera umboni wa choonadi Yes. 43:10-12
cha m’Malemba
[Chithunzi patsamba 12]
DZIKO LAPANSI . . . linalengedwa ndi Yehova . . . limasamalidwa ndi anthu . . . anthu adzakhalamo kwamuyaya