PHUNZIRO 5
Kupuma Koyenerera
POLANKHULA, n’kofunika kwambiri kupuma m’malo oyenerera. Zili choncho kaya mukukamba nkhani, kapena mukulankhula ndi munthu. Popanda kupuma koteroko, zimene mukulankhula zingamveke ngati phokoso lopanda tanthauzo m’malo mwa mawu opereka maganizo omveka bwino. Kupuma koyenera kumathandiza kumveketsa bwino zimene mukunena. Kumathandizanso kugogomeza mfundo zanu zazikulu kuti zisaiŵalike msanga.
Kodi mungadziŵemo motani moyenera kupuma? Nanga kupumako kuyenera kukhala kwa utali wotani?
Kupuma pa Zizindikiro Zopumira. Zizindikiro zopumira zakhala mbali yofunika kwambiri m’chinenero cholemba. Zingasonyeze pothera pa ndemanga kapena funso. M’zinenero zina, zingasonyezenso mawu ogwidwa a munthu wina kapena ochokera ku gwero lina. Kupuma kwina kumasonyeza mgwirizano wa mbali imodzi ya sentensi ndi mbali zina. Munthu akamaŵerenga yekha amaziona zizindikiro zopumirazo. Koma pamene akuŵerengera ena, mawu ake ayenera kupereka tanthauzo la chizindikiro chilichonse cholembedwa m’nkhaniyo. (Kuti mumve zambiri, onani Phunziro 1, “Kuŵerenga Molondola.”) Kusapuma pa zizindikiro zopumira kungalepheretse ena kumvetsa zimene mukuŵerenga kapenanso kusokoneza tanthauzo la mawu.
Kuwonjezera pamenepo, mmene malingaliro akhalira m’sentensi amaonetsanso moyenera kupuma. Katswiri wina woimba anati: “Kunena za kuimba manoti okha oimbira, iyayi, ndimafanana ndi oimba piyano ambiri. Koma luso lenileni la kuimba lagona pa kapumidwe ka pakati pa manotiwo.” N’chimodzimodzi ndi kulankhula. Kupuma m’malo oyenerera kumawonjezera kukoma ndi tanthauzo la nkhani yanu yokonzedwa bwinoyo.
Pokonzekera kuŵerenga pamaso pa anthu, mungachite bwino kuika zizindikiro m’nkhani imene mudzaŵerenga. Lembani kamzera kowongoka pamene mufuna kuima pang’ono kapena kuzengerezapo pang’ono. Lembani timizera towongoka tiŵiri toyandikana pamene mufuna kupuma motalikirapo pang’ono. Ngati muona kuti mawu ena akukuvutani m’sentensi, moti akukupangitsani kupuma m’malo olakwika, lumikizani pamodzi kagulu ka mawu ovutawo ndi pensulo. Ndiyeno ŵerengani kagulu ka mawuko kuchokera poyambira mpaka pothera pake. N’zimene amachita ambiri odziŵa kukamba nkhani.
Kaŵirikaŵiri, kupuma m’kulankhula kwa tsiku ndi tsiku sikukhala kovuta chifukwa mumadziŵa zimene mukufuna kunena. Komabe, ngati muli ndi chizoloŵezi chopuma kaŵirikaŵiri mosatsatira lingaliro lili pamenepo, kulankhula kwanu kudzakhala kopanda mphamvu ndi kosamveka bwino. Njira zimene mungawongolere chizoloŵezicho zaperekedwa m’Phunziro 4, “Kulankhula Mosadodoma.”
Kupuma Kosintha Ganizo. Pamene mukusintha kuchoka pamfundo yaikulu kupita pa ina, kupuma kumapatsa omvera anu mpata wa kusinkhasinkha, kukulondolani, kuzindikira kusinthako, ndi kumvetsa bwino ganizo lotsatira limene muti mulifotokoze. Kupuma pochoka pa ganizo lina kupita pa lina n’kofunika kwambiri mofanana ndi mmene muyenera kuyendetsera galimoto pang’onopang’ono pofuna kukhota kuchoka mumsewu wina kuloŵa wina.
Chifukwa china chimene okamba nkhani ena amafulumirira kuchoka pamfundo ina kupita pa ina osapuma n’chakuti amayesa kufotokoza mfundo zochuluka kwambiri. Kwa ena, chizoloŵezi chawocho chimangoonetsa kalankhulidwe kawo ka tsiku ndi tsiku. Mwinanso amakhala pakati pa anthu olankhula motero. Koma zimenezo zimalepheretsa kaphunzitsidwe kogwira mtima. Ngati muli ndi mfundo ina yofunikira ena kuimva ndi kuikumbukira, ifotokozeni modekha kuti imveke bwino. Dziŵani kuti kupuma polankhula n’kofunika kuti mfundo zimveke bwinobwino.
Ngati mudzakamba nkhani kuchokera pa autilaini, konzani mfundo zanu m’njira yoonetsa bwino lomwe malo opumira pakati pa mfundo zazikulu. Ngati mukakamba nkhani yoŵerenga, ikani zizindikiro m’malo osinthira kuchoka pamfundo yaikulu kupita pa ina.
Kupuma kosintha ganizo kumakhala kotalikirapo kuposa kupuma chabe. Komabe, sikuyenera kutalika mochita kunyanyira. Ngati kutalika kwambiri, kumaonetsa kuti simunakonzekere bwino ndipo mukuyesa kutolera zoti munene.
Kupuma Kotsindika. Kupuma kotsindika kumakhala koonekera. Kumachitidwa patsogolo kapena pambuyo pa ndemanga kapena funso limene limafunsidwa mwamphamvu. Kupuma koteroko kumapatsa omvera mpata wosinkhasinkha zimene zangonenedwa kumene, kapena kumawapatsa chidwi pa zimene zitsatire. Mitundu ya kupumayi n’njosiyana. Sankhani kumene mukufuna kugwiritsa ntchito. Koma kumbukirani kuti kupuma kotsindika kuyenera kuchitidwa kokha pa mawu ofunikira kwenikweni. Kuima chisawawa kumakhala kopanda phindu.
Yesu ataŵerenga mokweza m’Malemba mu sunagoge ku Nazarete, anagwiritsa ntchito luso la kupuma. Choyamba anaŵerenga za ntchito yake m’mpukutu wa mneneri Yesaya. Koma asanafotokoze tanthauzo lake, anakulunga mpukutuwo, naubwezera kwa kalinde, ndi kukhala pansi. Kenako, ena m’sunagogemo ali maso dwii pa iye, ndiyeno iye anati: “Lero lembo ili lakwaniritsidwa m’makutu anu.”—Luka 4:16-21.
Kupuma Pamene Mikhalidwe Yafuna Kuti Mutero. Nthaŵi zina, zosokoneza zina zingachititse kuti muyambe mwaima polankhula. Phokoso la galimoto yodutsa kapena kulira kwa mwana kungafune kuti muyambe mwadukiza makambirano anu ndi mwini nyumba mu utumiki wa kumunda. Pamsonkhano waukulu, ngati phokoso si lalikulu kwambiri, mungangokweza mawu anu ndi kupitiriza. Koma ngati phokoso ndi lalikulu komanso lopitirira, yambani mwaima. Ndi iko komwe, omvera anu amakhala asakumvetsera. Choncho, pumani m’njira yopindulitsa, ndi cholinga chothandiza omvera anu kupindula kwathunthu ndi zimene mukufuna kuwauza.
Kupuma Kopereka Mpata Wolabadira. Ngakhale kuti mungakambe nkhani popanda omvera kulankhulapo, m’pofunikabe kuwapatsa mpata wolabadira, osati ndi mawu, koma m’maganizo. Ngati mupereka mafunso ochititsa omvera anu kulingalira, komano mukulephera kupuma moyenerera, phindu lenileni la mafunso amenewo limatayika.
Ndiponso, si polankhula papulatifomu pokha pamene kupuma kuli kofunikira kwambiri, komanso polalikira kwa ena. Anthu ena amachita ngati samapuma polankhula. Ngati ndilo vuto lanu, yesetsani mwakhama kukulitsa luso limenelo. Mukatero, mudzatha kumalankhula bwino ndi ena ndi kukhalanso wolankhula mogwira mtima mu utumiki wa kumunda. Kupuma ndi mphindi yokhala chete, ndipo ena anenetsadi kuti chete amaunika, amatsindika, amakopa chidwi, ndipo amatsitsimutsa khutu.
Kulankhulana kwa tsiku ndi tsiku kumakhala kupatsana maganizo. Ena amakhala ndi chidwi chokumvetserani pokhapokha inunso mutamawamvetsera ndi kuonetsa chidwi pa zimene akunena. Zimenezi zimafuna kuti muzipuma ndi kuwapatsa mpata wokwanira kuti iwonso alankhule maganizo awo.
Mu utumiki wa kumunda, ulaliki wathu umakhala wogwira mtima ngati tiuchita m’njira yokambirana ndi anthu. Ambiri a Mboni za Yehova, apeza kuti zimakhala bwino kulonjerana ndi anthu choyamba, kenako kutchula nkhani yanu, ndiyeno n’kupereka funso. Amaima kaye popatsa mpata winayo kuti ayankhe, kenako amayamikira zimene mwininyumbayo wanena. M’kati mwa kukambiranako, angapatse mwininyumbayo mipata ingapo yakuti alankhulepo. Amazindikira kuti, kuti athandize kwambiri munthuyo, afunikira kudziŵa maganizo ake pankhaniyo.—Miy. 20:5.
N’zoona kuti si aliyense amene angalabadire m’njira yabwino. Koma zimenezo sizinalepheretse Yesu kupereka mpata wabwino ngakhale kwa adani ake kuti alankhule. (Marko 3:1-5) Kupatsa munthu winayo mpata woti alankhule kumam’limbikitsa kulingalira, ndipo akhoza kutulutsa za pansi pa mtima wake. Ndi iko komwe, chimodzi mwa zolinga za utumiki wathu ndi kulimbikitsa anthu kuyankha mochokera pansi pa mtima mwa kuwauza nkhani zofunika kwambiri zochokera m’Mawu a Mulungu zimene ayenera kusankhapo chochita.—Aheb. 4:12.
Kupuma m’malo oyenerera polankhula mu utumiki ndi luso lapadera. Pamene kupuma kuchitika mwaluso, malingaliro amamveka bwinobwino ndipo nthaŵi zambiri amakumbukika kwa nthaŵi yaitali.