Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 23 tsamba 116-121
  • Mphamvu ya Mawu ndi Kupuma

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mphamvu ya Mawu ndi Kupuma
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • **********
  • Kupuma Koyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Mphamvu ya Mawu Yoyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Uphungu Umalimbikitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kusinthasintha Mawu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 23 tsamba 116-121

Phunziro 23

Mphamvu ya Mawu ndi Kupuma

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kulankhula momveka bwino?

1 Ngati ena satha kukumvani, phindu la zimene mukunenazo limatayika. Komanso, mawu akakhala okwera kwambiri, amasokosera omvetsera ndi kupangitsa mfundo zabwino zimene mwakonza kusamveka. Kufunika kwa kusamala za mphamvu ya mawu athu kumaoneka m’Nyumba za Ufumu zambiri, pamene aja okhala kutsogolo akamayankha pamisonkhano samveka kumbuyo. Nthaŵi zina munthu wolankhula papulatifomu angakhale wopanda mphamvu ya mawu yokwanira ndipo amalephera kugwira mtima omvetsera ake. Mu utumiki wakumundanso timakumana ndi anthu okhala ndi vuto lakumva komanso pamakhala mapokoso ena, kaya ndi ochokera m’nyumba zimene tikufikapozo kapena kunja. Zonsezi zimasonyeza kuti m’pofunika kuti tiyesetse kulankhula ndi mphamvu ya mawu yoyenera.

2 Mphamvu ya mawu pamlingo woyenera. Kuti tidziŵe bwino mphamvu ya mawu yoyenerera tiyenera kudzifunsa kuti, Kodi ndinali kulankhula ndi mphamvu yofunikira? Ndiko kuti, kodi munali kumveka kwa okhala kumbuyo popanda kusokosera akutsogolo? Zimenezo zingakhale zokwanira kwa wophunzira watsopano, koma awo ozoloŵerapo ayenera kudziŵanso bwino mbali zotsatirazi za mfundoyo. Woyang’anira sukulu ayenera kudziŵa kuti wophunzira aliyense adzam’patsa uphungu pamlingo wotani pamfundoyi.

3-10. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene imatithandiza kudziŵa mphamvu ya mawu imene tiyenera kugwiritsa ntchito?

3 Mphamvu ya mawu yoyenerana ndi mikhalidwe. Mlankhuli ayenera kuzindikira mikhalidwe yosiyanasiyana imene angalankhulirepo nkhani. Akatero amakulitsa mphamvu zake za kuzindikira, ndipo amakhala wokhoza kusinthasintha komanso amatha kuwafika pamtima omvetsera ake mosavuta ndi kusatayana nawo.

4 Mikhalidwe imasiyana malinga ndi maholo osiyanasiyana komanso chiŵerengero cha omvetsera. Kuti muchite malinga ndi mikhalidweyo mufunikira kusintha mawu anu. Kupereka nkhani m’Nyumba ya Ufumu kumafuna mphamvu ya mawu yokulirapo kuposa m’chipinda chochezera cha nyumba ya wokondwerera watsopano. Ndiponso, gulu laling’ono lokhala pafupi ndi pulatifomu, monga pokumana kaamba ka utumiki wakumunda, limafunikira mphamvu ya mawu yocheperapo kuposa pamene holoyo yadzaza, monga pamsonkhano wa utumiki.

5 Koma ngakhale mikhalidwe imeneyi, simangokhala chomwecho nthaŵi zonse. Pamabuka mapokoso adzidzidzi m’kati ndi kunja kwa holo. Galimoto kapena sitima zodutsa pafupi, mapokoso a zifuyo, kulira kwa ana, komanso anthu ofika mochedwa—zonsezi zimafuna kusintha mphamvu ya mawu anu. Kulephera kuzindikira zimenezo ndi kusasintha mawu anu kuti amveke kudzapangitsa mfundo zina zofunika kuphonyeka.

6 Mipingo yambiri ili ndi zipangizo zokuzira mawu. Koma ngati wina sasamala pozigwiritsa ntchito, akumati akakweza mawu mogonthetsa m’khutu kenako n’kutsitsa moti osamvekanso, afunikira kupatsidwa uphungu kaamba kosazindikira mikhalidwe imeneyi. (Onani Phunziro 13 pa kagwiritsidwe ka cholankhulira.)

7 Nthaŵi zina mlankhuli angapeze mfundo imeneyi ya mphamvu ya mawu kukhala yovuta chifukwa cha chibadwa cha mawu ake. Ngati limenelo lili vuto lanu ndipo mawu anu sangathe kufika patali, woyang’anira sukulu adzaganizira zimenezo popereka uphungu. Iye angaperekepo maganizo a njira zimene mungatsate poyesayesa kukulitsa mphamvu ya mawu anu. Komabe, kamvekedwe ka mawu anu ili mfundo yosiyana ya uphungu ndipo sadzaigogomeza poyang’anira mphamvu ya mawu anu.

8 Sikuti mikhalidwe yonse ingasamalidwe m’nkhani imodzi. Uphungu uyenera kuperekedwa pankhani imene yangolankhulidwayo, osati pamikhalidwe ina imene sinachitike koma yooneka kukhala yothekera. Komabe, ngati kuoneka kukhala kofunikira, woyang’anira sukulu angachenjeze wophunzira za mavuto amene angakumane nawo pamikhalidwe ina, ngakhale kuti wophunzirayo wayamikiridwa pankhani yake ndipo pasilipi lake la uphungu palembedwa “B”.

9 Kodi wophunzira angadziŵe bwanji kuti mphamvu ya mawu ake ili yokwanira? Chopimira chabwino ndi kuona kalabadiridwe ka omvetsera. Mlankhuli wodziŵa bwino amati pamene akulankhula mawu oyamba amayang’anitsitsa aja amene akhala kumbuyo kwa holo kuti aone mmene akuchitira pofuna kudziŵa ngati akumva mosavutikira, ndiyeno amasintha mphamvu ya mawu ake mofunikira. Atazoloŵera mkhalidwe wa holoyo, sakhalanso ndi vuto.

10 Njira ina ndiyo kuona mmene alankhuli ena amachitira papologalamu imodzimodziyo. Kodi iwo amamveka mosavuta? Kodi amagwiritsa ntchito mphamvu ya mawu yaikulu motani? Sinthani yanu moyenera.

11, 12. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti mphamvu ya mawu iyenerane ndi nkhani?

11 Mphamvu ya mawu yoyenerana ndi nkhani. Mbali imeneyi ya kukambirana kwathu za mphamvu ya mawu siyenera kusokonezedwa ndi kusintha mawu. Pakali pano tingofuna kunena za kulinganiza mphamvu ya mawu ndi nkhani imene ikulankhulidwa. Mwachitsanzo, poŵerenga mawu achiweruzo m’Malemba, mwachionekere mphamvu ya mawu idzasiyana ndi mmene tingaŵerengere uphungu wonena za chikondi pakati pa abale. Yerekezaninso Yesaya 36:11 ndi mavesi 12 ndi 13 ndipo onani kusiyana kumene kuyenera kuti kunalipo m’kaŵerengedwe ka mawu amenewa. Mphamvu ya mawu iyenera kukhala yoyenerana ndi nkhaniyo koma siyenera kuchitidwa mopambanitsa.

12 Pofuna kudziŵa mphamvu ya mawu imene mungagwiritse ntchito, pendani mosamalitsa nkhani yanu ndi cholinga chanu. Ngati mukufuna kusintha malingaliro a omvetsera anu, musawawombe ndi mawu amphamvu kwambiri. Komabe, ngati mukufuna kuwasonkhezera kuchita ntchito inayake mokangalika, mwina mungakulitseko mphamvu ya mawu. Ngati nkhaniyo ikufuna nyonga, musaifooketse mwa kulankhula mofeŵa kwambiri.

**********

13-16. Fotokozani phindu la kupuma.

13 Polankhula nkhani yanu, kupuma m’malo oyenera n’kofunika kwambiri mofanana ndi mphamvu ya mawu yoyenera. Popanda kupuma, tanthauzo la mawu silionekera bwino ndipo mfundo zazikulu zimene omvetsera anu ayenera kukumbukira sizikhomerezeka m’maganizo mwawo. Kupuma kumakupatsani chidaliro ndi kukhazikika maganizo, kumakulolani kupuma mpweya kwabwino ndi mpata wokhazika maganizo pansi mukafika pamfundo zovuta m’nkhani yanu. Kupuma kumasonyeza omvetsera kuti zonse zili bwino, kuti simuli wamantha mopambanitsa, kuti mukuganizira omvetsera anu, ndi kuti muli ndi kanthu kena kamene mukufuna kuti iwo akamve ndi kukakumbukira.

14 Mlankhuli watsopano sayenera kuchedwa kudziŵa luso la kupuma m’malo oyenera. Choyamba, ayenera kukhutira kuti zimene akufuna kunena zili zofunika ndi kuti akufuna kuti zikakumbukiridwe. Mayi powongolera mwana wake nthaŵi zina amayamba wanena kanthu kena kuti akope maganizo a mwanayo. Iye sadzanena mawu ena kufikira mwanayo atatchera khutu mokwanira. Ndiyeno adzanena zimene zili m’maganizo mwake. Cholinga chake akufuna atsimikize kuti mwanayo sadzanyalanyaza zimene akufuna kunena ndi kutinso azizikumbukira.

15 Anthu ena sapuma konse ayi, ngakhale m’kulankhula kwawo kwa masiku onse. Ngati limenelo lilinso vuto lanu mufunikira kukulitsa luso limeneli kuti utumiki wanu wakumunda uzikhala wogwira mtima. Kulankhula kwathu m’mundamo kumakhala m’njira yokambirana. Kuti muzipuma mwanjira yoti mwininyumba asadudukire koma kuti amvetsere ndi kuyembekeza pamafunika kupuma koyenera. Koma luso la kupuma ndi kukuchita moyenerera pokambirana n’lofunika kwambiri komanso lopindulitsa mofanana ndi polankhula nkhani papulatifomu.

16 Vuto limodzi lalikulu kwambiri ponena za kupuma m’malo oyenera m’nkhani ndilo kukhala ndi zambiri zolankhula. Peŵani zimenezo. Lolani nthaŵi zopuma; n’zofunika kwambiri.

17-21. Fotokozani kufunika kwa kupuma pa chizindikiro chopumira.

17 Kupuma pa chizindikiro chopumira. Cholinga chopumira pa chizindikiro cha kupuma ndicho kumveketsa ganizo; kulekanitsa malingaliro ofanana; mawu, ziganizo, mapeto a masentensi ndi ndime. Kaŵirikaŵiri kusintha kumeneko kungasonyezedwe ndi kusintha mawu, koma kupuma kumathandizanso kumveketsa bwino zimene zikunenedwa. Ndipo monga mmene makoma ndi masemikoloni alili ndi ntchito zosiyana pogaŵa masentensi, kupumanso kuyenera kuchitidwa mosiyanasiyana malinga ndi ntchito yake.

18 Kupuma m’malo osayenera kukhoza kusinthiratu ganizo la sentensi. Chitsanzo cha zimenezi ndi mawu a Yesu pa Luka 23:43, NW, “Zoonadi ndikukuuza iwe lero, Udzakhala nane m’Paradaiso.” Ngati komayo kapena popumira pakanakhala pakati pa mawu akuti “iwe” ndi “lero” ganizo lake likanakhala losiyana kotheratu, monga mmene anthu ambiri amasulira molakwa lemba limeneli. Choncho kupuma m’malo oyenera n’kofunika kuti kupereke ganizo lofunikira.

19 Phunzirani kupuma polankhula kuchokera m’maganizo mwa kutsatira zizindikiro zonse pamene muŵerenga. Chizindikiro chokha chopumira chimene nthaŵi zina mungachinyalanyaze poŵerenga ndi koma. Mukafika pakoma, zili kwa inu kusankha kupuma kapena kusapuma. Koma semikoloni, fulusitopu, koteshonimaki, ndi ndime, zonsezo muyenera kuzilabadira.

20 Kungakhale kothandiza poŵerenga nkhani yoŵerenga kapena chigawo china m’Baibulo kulembamo zizindikiro. Lembani kamzera konga mphini pakati pa mawu pofunikira kupuma (kapena pofunikira kuŵerenga mongozengereza pang’ono); ngati pakufunika kupuma kotalikirapo lembani mphini ziŵiri kapena “X.”

21 Komabe ngati pochita pulakatisi kuŵerenga mupeza kuti masentensi ena akukuvutani ndipo kaŵirikaŵiri mukupuma m’malo olakwika, mungalembe zizindikiro ndi pensulo zolumikiza pamodzi mawu onse opanga ganizo. Ndiyeno, pamene muŵerenga, musapume kapena kuzengereza mpaka mutafika pothera mawu amene mwalumikizawo. Alankhuli ambiri ozoloŵera amachita zimenezo.

22-24. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kupuma pofuna kusintha ganizo?

22 Kupuma posintha ganizo. Pochoka pamfundo ina yaikulu kupita pa ina, kuima kumapatsa mpata omvetsera kuti alingalirepo. Komanso kumapeŵetsa kumva zinthu molakwa. Kumapatsanso maganizo mpata wakuti akonzeke, kuti azindikire kusinthako ndi kutsatira mfundo yatsopano imene ikufotokozedwa. Kupuma posintha maganizo kwa mlankhuli n’kofunika kwambiri mofanana ndi mmene woyendetsa galimoto amachepetsera liŵiro pofuna kukhota.

23 M’nkhani yolankhula kuchokera m’maganizo, mfundo zake ziyenera kukhala zolinganizidwa bwino pa autilaini kuti zipereke mpata wopuma pakati pa mfundo zazikulu. Zimenezi siziyenera kudodometsa kugwirizanika kwa nkhaniyo, koma malingaliro ake ayenera kukhala oumbika bwino kwambiri moti mungathe kulongosola mfundo yakutiyakuti mpaka pachimake, kenako n’kupuma, kenakonso n’kupita paganizo lina latsopano. Ngati kuli kofunika, mofika pachimake moteromo limodzinso ndi mosintha mwake mungaikemo zizindikiro zokukumbutsani pa autilaini yanu.

24 Kupuma posintha ganizo kaŵirikaŵiri kumakhala kotalikirapo kuposa kwa pachizindikiro chopumira; komabe, kupuma kotalikirapo sikuyenera kuchitidwa mopambanitsa m’nkhani chifukwa nkhaniyo ingatalike kwambiri. Ndiponso, kupumako kungaoneke kusakhala kwachibadwa.

25-28. Fotokozani mmene kupuma kumatithandizira kugogomeza mfundo komanso pa mikhalidwe yosokoneza.

25 Kupuma kogogomeza. Kupuma kogogomeza kaŵirikaŵiri kumakhala kokopa maganizo. Kumadzutsa chiyembekezo kapena kumapatsa omvetsera mpata woti alingalire.

26 Kupuma kaye pofika pamfundo yaikulu kumadzutsa chiyembekezo. Kupuma pambuyo pake kumalola tanthauzo lonse la lingalirolo kuloŵa m’maganizo. Ntchito ziŵirizi za kupuma n’zosiyana, choncho muyenera kusankha kupuma kumene kungakhale koyenerera bwino panthaŵiyo kapena mungagwiritse ntchito konse kuŵiri.

27 Kupuma kogogomeza kuyenera kuchitidwa pamawu ofunika kwambiri, ngati mungopuma wambawamba phindu lake limatayika.

28 Kupuma pamene mkhalidwe wafuna kuti mutero. Zododometsa kaŵirikaŵiri zimafuna kuti wolankhula nkhaniyo aime kaye pang’ono. Ngati chododometsacho si chachikulu kwambiri ndipo mungangowonjezera mphamvu yanu ya mawu ndi kupitirizabe, mungachite bwino kwambiri. Komabe, ngati chododometsacho chikhoza kusokoneza kwambiri nkhaniyo, pumani kaye. Omvetsera anu adzayamikira kuwaganizira kwanu. Ndi iko komwe, nthaŵi zambiri amalephera kumvetsera chifukwa cha zododometsa zina zing’onozing’ono zimene zimakopa maganizo awo. Choncho pumani mofunikira, kuti mutsimikize kuti omvetsera anu akupeza phindu lokwanira pazinthu zabwino zimene mukuwauza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena