PHUNZIRO 26
Kukamba Nkhani M’njira Yotsatirika
MUSANAKONZE mfundozo kuti zikhale m’ndondomeko yotsatirika, khalani ndi cholinga m’maganizo mwanu. Kodi cholinga chanu ndi kungowadziŵitsa ena za nkhani—chiphunzitso, maganizo, mkhalidwe wabwino, makhalidwe a anthu, kapena moyo wakutiwakuti? Kodi mukufuna kukavomereza kapena kutsutsa maganizo ena ake? Kodi cholinga chanu ndicho kuthandiza ena kuti aziyamikira kanthu kena kapena kuwalimbikitsa kuchita kanthu kena? Kaya mukalankhula kwa munthu mmodzi kapena ku gulu la anthu, kuti mukatero mogwira mtima, muyenera kuganizira zimene anthuwo akuzidziŵa kale pakhaniyo ndi mmene akuionera. Mutachita zimenezo, lembani nkhaniyo m’njira yoti ikakuthandizeni kukwaniritsa cholingacho.
Ponena za utumiki wa Saulo (Paulo) ku Damasiko, pa Machitidwe 9:22 timaŵerenga kuti ‘anadodometsa Ayuda okhala m’Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Kristu.’ Kodi umboni womvekera bwino umenewo unaphatikizapo mfundo zotani? Malinga ndi mbiri ya utumiki wa Paulo pambuyo pake ku Antiokeya ndi ku Tesalonika, iye choyamba anafotokoza mfundo yakuti Ayuda analandira Malemba Achihebri ndipo anakhulupirira zimene malembawo ananena za Mesiya. Ndiyeno m’Malembawo, Paulo anasankhamo mbali zimene zinafotokoza moyo wa Mesiya ndi utumiki wake. Anagwira mawu mbali zimenezo naziyerekeza ndi zimene zinam’chitikiradi Yesu. Potsirizira pake, anapereka chifukwa chomvekera bwino chakuti, Yesu ndiye Kristu, kapena kuti Mesiya. (Mac. 13:16-41; 17:2, 3) Inunso mukamafotokoza choonadi cha m’Baibulo m’njira yotsatirika, chikhoza kukhala ndi mphamvu yokhutiritsa anthu.
Kukonza Kakambidwe ka Nkhani. Nkhani yanu mungaiyale m’njira zosiyanasiyana zotsatirika. Mukhozanso kuphatikiza njira zingapo m’nkhani imodzi, ngati mukuona kuti zingakhale zothandiza. Nazi njira zingapo zimene mungagwiritse ntchito.
Njira ya timitu ta nkhani. Uku ndiko kugaŵa nkhani yanu m’magawo, gawo lililonse likumaloza ku cholinga chanu. Magawo amenewo angakhale mfundo zazikulu zimene zikuthandiza kumveketsa nkhani yanu. Angakhalenso zifukwa zovomereza kapena kutsutsa nkhani ina. Mukhoza kuwonjezerapo mfundo zina zokhudzana ndi nkhaniyo, kapena kuchotsapo mfundo zina ngakhale kuti n’zokhudzana ndi nkhaniyo; zimadalira mtundu wa omvera anu kapena cholinga chanu pa nkhaniyo.
Nachi chitsanzo cha njira ya timitu ta nkhani. Nkhani yaifupi yonena za dzina la Mulungu ingaphatikizepo izi, (1) chifukwa chake kuli kofunikira kudziŵa dzina la Mulungu, (2) kuti dzinalo ndani, ndipo (3) mmene tingalemekezere dzinalo.
Tikhoza kuphunzira zambiri za kuyala nkhani mwa njira ya timitu ta nkhani mwa kuyang’ana m’mabuku olembedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ogwiritsa ntchito pa maphunziro a Baibulo a panyumba. (Mat. 24:45) Mabuku ameneŵa kaŵirikaŵiri amakhala ndi mitu ya nkhani yambiri imene ingathandize ophunzira kudziŵa mfundo zazikulu za choonadi cha m’Baibulo. Mabuku okulirapo amakhalanso ndi timitu tam’kati togaŵa mutu uliwonse. Kamutu kalikonse kamathandiza wophunzirayo kukonzekera mfundo zotsatira kamutuko ndipo kamathandizanso kuona chithunzi chonse cha nkhaniyo.
Njira yofotokoza kututa zimene munthu amafesa. Kufotokoza zimene munthu amatuta malinga ndi zimene amafesa ndi njira ina yokambira nkhani mwa ndondomeko yotsatirika.
Ngati mukulankhula kwa anthu kapena munthu amene ayenera kuganizira mosamala zotsatira za chinthu china chimene akuchita kapena chimene akufuna kuchita, njira imeneyi ingakhale yogwira mtima. Pa Miyambo chaputala 7 timapezapo chitsanzo chabwino kwambiri cha njira imeneyi. Pamenepo akufotokoza momvekera bwino mmene mnyamata “wopanda nzeru” (chofesa chake) akukopedwera ndi mkazi wachiwerewere kenako n’kugwera m’tsoka lomvetsa chisoni (zimene anatuta).—Miy. 7:7.
Pofuna kutsindika mfundo, mungafotokoze zotsatira zoipa zimene zimagwera okana kuyenda m’njira za Yehova, ndi zotsatira zabwino zimene zimafika kwa amene amamvera Yehova. Polimbikitsidwa ndi mzimu wa Yehova, Mose anasonyeza kusiyana kwa zotsatirazo polankhula ndi mtundu wa Aisrayeli asanakaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa.—Deut., chap. 28.
Nthaŵi zina, ndi bwino kuyamba nkhani yanu mwa kusonyeza kuti munthu akachita zakutizakuti (kufesa), zimene zimamuonekera n’zakutizakuti (zimene amatuta). Njira imeneyi kaŵirikaŵiri imasonyeza vuto ndi njira yothetsera vutolo.
Kusonyeza vuto ndi njira yothetsera vutolo. Mu utumiki wa kumunda, pamene mufotokoza vuto lina limene limakhudza anthu ambiri ndi kusonyeza njira yokhutiritsa yothetsera vutolo, zingalimbikitse munthuyo kuti amvetsere. Vutolo lingakhale limene inuyo mwalitchula kapena lingatchulidwe ndi munthu winayo.
Vuto limenelo lingakhale mfundo yakuti anthu amakalamba ndi kufa, kuchuluka kwa zaupandu, kapena kusoŵa chilungamo kofala. Vuto limeneli n’lachidziŵikire, moti simungachite kufotokoza zambiri. Tangoyambani mwa kutchula vutolo, kenako perekani njira yolithetsera yochokera m’Baibulo.
Koma nthaŵi zina vutolo lingakhale lokhudza munthu payekha, mwina ndi vuto la kulera ana kwa kholo limodzi, kuda nkhaŵa kwambiri chifukwa chodwala matenda aakulu, kapena nkhanza zimene munthu wina akum’chitira. Kuti mukhale wothandiza kwambiri, muyenera kukhala womvetsera bwino. Baibulo limapereka njira zothetsera mavuto onseŵa. Koma tikayenera kuligwiritsa ntchito mwanzeru. Kuti kukambirana kwanu kum’thandizedi munthuyo, muyenera kulankhula zenizeni. Nenani momvekera bwino kuti mukunena njira yothetsera vuto kwa nthaŵi yonse, kapena mpumulo wa pakanthaŵi, kapena mmene angathanire ndi mkhalidwe umene sudzasintha m’dziko lino. Kunena kwina, onetsetsani kuti zifukwa za m’Malemba zimene mukutchula zikupereka umboni wokwanira wa mfundo yanu. Kulephera kutero kungachititse munthuyo kusakhulupirira njira yothetsera vuto imene mukuinenayo.
Kufotokoza zochitika m’ndondomeko ya nthaŵi. Nkhani zina zimafuna kufotokoza zochitika motsatira nthaŵi pamene zinachitika. Mwachitsanzo, m’buku la Eksodo, Miliri Khumi amaifotokoza motsatira ndondomeko ya mmene inachitikira. Pa Ahebri chaputala 11, mtumwi Paulo anandandalika amuna ndi akazi amene anapereka chitsanzo chabwino cha chikhulupiriro motsatira nthaŵi imene anakhalako.
Ngati mufotokoza zochitika zakale motsatira nthaŵi, mungathandize omvera anu kumvetsa mmene zinthu zina zinachitikira. Njira imeneyi imathandiza pofotokoza zochitika za m’mbiri yamakono komanso zochitika za m’mbiri ya m’Baibulo. Choncho mukhoza kumaphatikiza njira yofotokoza zochitika motsatira ndondomeko ya nthaŵi komanso njira yofotokoza zimene munthu angafese ndi zotuta zake. Ngati mukufuna kufotokoza zochitika za m’tsogolo zimene Baibulo limanena kuti zidzachitika, njira ya kakambidwe imene omvera anu angaitsatire ndi kukumbukira mosavuta ingakhale yofotokoza zochitika motsatira ndondomeko ya nthaŵi.
Kufotokoza zochitika m’ndondomeko ya nthaŵi sikutanthauza kuti nthaŵi zonse muyenera kuyamba ndi zoyambirira. Nthaŵi zina, mungachite bwino kuyamba mwa kufotokoza chimake cha nkhaniyo. Mwachitsanzo, pofotokoza chokumana nacho cha munthu, mungayambe mwa kufotokoza nthaŵi pamene chikhulupiriro cha munthuyo kwa Mulungu chinali chitayesedwa kwambiri. Pokhala mutadzutsa chidwi ndi mbali imeneyo, mukhoza tsopano kulongosola ndondomeko ya zochitika zimene zinam’fikitsa ku chokumana nacho chimenecho.
Kugwiritsa Ntchito Mfundo Zoyenerera Zokha. Mulimonse mmene mungayalire mfundo zanu, onetsetsani kuti mukugwiritsa ntchito mfundo zoyenerera zokha. Sankhani mfundo malinga ndi mutu wa nkhani yanu. Ganiziraninso mtundu wa omvera anu. Mfundo ina ikhoza kukhala yofunika kwambiri kwa omvera ena, koma ikhoza kukhalanso yosafunikira kwenikweni kwa omvera ena. Tsimikizaninso kuti mfundo zanu zonse zikathandiza kukwaniritsa cholinga chanu. Kupanda kutero, kakambidwe kanu kadzakhala kopanda phindu lenileni, ngakhale katakhala kosangalatsa.
Pofufuza nkhani, mungapeze mfundo zosangalatsa zambiri zokhudza nkhani yanu. Kodi muyenera kugwiritsa ntchito zochuluka motani? Ngati omvera anu muwapanikiza ndi mfundo zambirimbiri, mukhoza kuwononga cholinga chanu. Omvera anu akhoza kukumbukira mosavuta mfundo zazikulu zochepa chabe zofotokozedwa bwino kusiyana ndi mfundo zambirimbiri zofotokozedwa mothamanga. Apa sitikutanthauza kuti mfundo zina za pambali zosangalatsa simungaziphatikizepo ayi. Koma samalani kuti zisaphimbe cholinga cha nkhani yanu. Onani mmene mfundo zoterozo anaziphatikizira mosamala m’Baibulo pa Marko 7:3, 4 ndi Yohane 4:1-3, 7-9.
Pamene mukuchoka pa mfundo ina kupita pa ina, samalani kuti musachokepo mwadzidzidzi moti omvera anu n’kutaya njira ya malingaliro anu. Kuti malingaliro azilumikizana bwino, mungafunikire kuyala ulalo wochokera pa lingaliro lina kupita pa lina. Ulalowo ungakhale mawu ochepa kapena sentensi yonse yosonyeza mgwirizano wa malingaliro. M’zinenero zambiri, mawu olumikizira maganizo angagwiritsidwe ntchito posonyeza mgwirizano pakati pa lingaliro latsopano ndi limene langochokapo kumene.
Kugwiritsa ntchito mfundo zoyenerera zokha ndi kuziyala m’ndondomeko yotsatirika kudzakuthandizani kukwaniritsa cholinga chanu.