Maufumu Athira Nkhondo Dziko Lolonjezedwa
SAMARIYA, likulu la ufumu wakumpoto wa Israyeli, anagonjetsedwa ndi Asuri m’chaka cha 740 B.C.E. Pamenepo Aisrayeli anayamba kulamulidwa ndi ufumu wankhanzawo. Asuri anali kukhala kumpoto chakumapeto kwa zigwa za Mesopotamiya, kufupi ndi Tigirisi, umodzi wa mitsinje yaikulu m’dera la Fertile Crescent. Nimrode anakhazikitsa midzi ya Nineve ndi Kala yomwe inali yofunika kwambiri kwa Asuri. (Gen. 10:8-12) M’nthaŵi ya ulamuliro wa Salimanezere Wachitatu, Asuri anafalikira chakumadzulo mpaka kudera la madzi ochuluka ndiponso zigawo zachonde kwambiri za Suriya ndi kumpoto kwa Israyeli.
Mu ulamuliro wa Mfumu Tiligati Pilesere Wachitatu (Puli), yotchulidwa m’Baibulo, Asuri anayamba kupondereza Israyeli. Asilikali ake anafikanso kum’mwera kwa Yuda. (2 Maf. 15:19; 16:5-18) M’kupita kwa nthaŵi, Asuri analoŵa mu Yuda ngati “madzi” osefukira, nafika ku likulu lake ku Yerusalemu.—Yes. 8:5-8.
Mfumu ya Asuri Sanakeribu inaloŵerera Yuda m’chaka cha 732 B.C.E. (2 Maf. 18:13, 14) Inalanda midzi 46 ya Yuda kuphatikizapo Lakisi, umene unali pamalo abwino kwambiri pa zankhondo opezeka kuchidikha cha Shefela. Monga mmene mapu akusonyezera, asilikali ake anadzera kum’mwera chakumadzulo kwa Yerusalemu, nazungulira likulu la Yudayo. M’mabuku amene analembamo mbiri yake, Sanakeribu anadzitama kuti anasunga Hezekiya “ngati mbalame m’chikwere,” pamene m’mbiri yawo ya Asuri sanatchulemo n’komwe kuphedwa kwa asilikali a Sanakeribu ndi mngelo wa Mulungu.—2 Maf. 18:17-36; 19:35-37.
Ufumu wa Asuri masiku ake anauthera. Amedi, amene anali kukhala m’dera la mapiri limene panopa ndi Iran, anayamba kumenyana ndi asilikali a Asuri otsalawo. Zimenezi zinapangitsa kuti Asuri aiwale madera ake akumadzulo, amenenso anayamba kumuukira. Panthaŵi imeneyi n’kuti Ababulo atayamba kupeza mphamvu moti analanda mudzi wa Ashuri. M’chaka cha 632 B.C.E., Nineve—“mudzi wa mwazi”—unagonjetsedwa ndi mitundu yogwirizana ya Ababulo, Amedi, ndi Asikuti, omwe anali anthu okonda nkhondo ochokera kumpoto kwa Nyanja Yakuda. Zimenezi zinakwaniritsa maulosi a Nahumu ndi Zefaniya.—Nah. 3:1; Zef. 2:13.
Ufumu wa Asuri unathera ku Harana. Ataukiridwa ndi asilikali amphamvu a Ababulo, Asuri anayesetsa kulimba nayo nkhondo akumayembekezera thandizo lochokera ku Igupto. Komabe paulendo wake wopita kumpoto, Farao-neko anachedwa ku Megido polimbana ndi Yosiya, Mfumu ya Yuda. (2 Maf. 23:29) Mmene Neko amafika ku Harana, munali m’mbuyo mwa alendo, moti anapeza Ufumu wa Asuri utagonjetsedwa kale.
Ufumu wa Babulo
Kodi ndi mudzi uti umene umafika m’maganizo mwanu mukamva mawu akuti “minda yolenjekeka ya maluŵa”? Ndi Babulo, likulu la ulamuliro wamphamvu padziko lonse wodziŵika ndi dzina lomweli umene m’maulosi umaimiridwa ndi mkango wamapiko. (Dan. 7:4) Mudzi umenewu unkadziŵika kwambiri chifukwa cha chuma chake, malonda ake, ndiponso kuthandiza kwake pa kufalikira kwa chipembedzo ndi zokhulupirira nyenyezi. Ufumuwo unali m’madambo a kum’mwera kwa Mesopotamiya pakati pa mitsinje ya Tigirisi ndi Firate. Mtsinje wa Firate unadutsa pakati penipeni pa mudziwu, ndipo chifukwa cha makoma ake zimaoneka zosatheka kuloŵa m’mudziwu.
Ababulo anayambitsa njira zamalonda zodutsa m’chipululu chamiyalacha kumpoto kwa Arabiya. Panthaŵi ina yake, Mfumu Nabonidasi anakakhala ku Tema, atasiya Belisazara akulamulira Babulo.
Babulo anaukira Kanani maulendo atatu. Pambuyo poti Nebukadinezara wagonjetsa Aigupto ku Karikemisi m’chaka cha 625 B.C.E., Ababulo analunjika kum’mwera ku Hamati, kumene anagonjetsanso Aigupto amene anali kubwerera kwawo. Kenako Ababulo anasesa dera lonse lakugombe mpaka kuchigwa cha Igupto, ndipo anagonjetsa Asikeloni mmene amapita kum’mwerako. (2 Maf. 24:7; Yer. 47:5-7) Paulendo umenewu, Yuda anayamba kulamulidwa ndi Babulo.—2 Maf. 24:1.
Mfumu Yehoyakimu ya Yuda inapanduka m’chaka cha 618 B.C.E. Ndiyeno Babulo anatumiza asilikali a mitundu yoyandikana ndi Yuda kuti aononge Yudayo koma asilikali a Babuloyo anazinga ndi kugonjetsa Yerusalemu. Patangopita nthaŵi pang’ono chichitikireni zimenezi, Mfumu Zedekiya inagwirizana ndi ufumu wa Igupto ndipo inaputa Ababulo koopsa moti mkwiyo wawo unayakira Yuda. Kachiŵirinso iwo anaukira Yudayo ndipo anayamba kuwononga midzi yake yonse. (Yer. 34:7) Pamapeto pake, Nebukadinezara anatsogolera asilikali ake ku Yerusalemu, ndipo anagonjetsa mzindawo m’chaka cha 607 B.C.E.—2 Mbiri 36:17-21; Yer. 39:10.
[Bokosi patsamba 23]
MABUKU A M’BAIBULO OLEMBEDWA NTHAŴIYI:
Hoseya
Yesaya
Mika
Miyambo (mbali yake ina)
Zefaniya
Nahumu
Habakuku
Maliro
Obadiya
Ezekieli
1 ndi 2 Mafumu
Yeremiya
[Mapu patsamba 23]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Maufumu a Babulo ndi Asuri
Ufumu wa Asuri
B4 Mofi (Nofi)
B4 Zoani
B5 IGUPTO
C2 KUPRO (KITIMU)
C3 Sidoni
C3 Turo
C3 Megido
C3 Samariya
C4 Yerusalemu
C4 Asikeloni
C4 Lakisi
D2 Harana
D2 Karikemesi
D2 Aripadi
D2 Hamati
D3 Ribala
D3 ASURI
D3 Damasiko
E2 Gozani
E2 MESOPOTAMIYA
F2 MINI
F2 ASURI
F2 Khorsabad
F2 Nineve
F2 Kala
F2 Ashuri
F3 BABULO
F3 Babulo
F4 KALDAYO
F4 Ereke
F4 Uri
G3 Susani
G4 ELAMU
Ufumu wa Babulo
C3 Sidoni
C3 Turo
C3 Megido
C3 Samariya
C4 Yerusalemu
C4 Asikeloni
C4 Lakisi
D2 Harana
D2 Karikemesi
D2 Aripadi
D2 Hamati
D3 Ribala
D3 ASURI
D3 Damasiko
D5 Tema
E2 Gozani
E2 MESOPOTAMIYA
E4 ARABIYA
F2 MINI
F2 ASURI
F2 Khorsabad
F2 Nineve
F2 Calah
F2 Ashuri
F3 BABULO
F3 BABULO
F4 KALDAYO
F4 Ereke
F4 Uri
G3 Susani
G4 ELAMU
[Malo ena]
G2 MEDIYA
Njira Zazikulu (Onani m’kabuku kenikeni)
[Nyanja]
B3 Nyanja ya Mediterranean (Nyanja Yaikulu)
C5 Nyanja Yofiira
H1 Nyanja ya Caspian
H5 Nyanja ya Perisiya
[Mitsinje]
B5 Nile
E2 Firate
F3 Tigirisi
[Chithunzi patsamba 22]
Chitunda cha Lakisi
[Chithunzi patsamba 22]
Chifanizo cha Megido wakale
[Chithunzi patsamba 23]
Chithunzi chongoyerekezera minda yolenjekeka ya maluŵa ku Babulo