Anthu a Mulungu Abwerera Kudziko Lawo
DZIKO lamakono la Iran linazunguliridwa ndi mitandadza ya mapiri akuluakulu aŵiri. Mapiriwo ndi Elburz (kum’mwera kwa Nyanja ya Caspian) ndi Zagros (kum’mwera chakum’maŵa kwake kufupi ndi Nyanja ya Perisiya). Pakati pa mapiriŵa pali zigwa zitalizitali zachonde, ndiponso pali mitsetse yomwe ili ndi mitengo yambiri. M’zigwamu simutentha kapena kuzizira kwambiri, koma madera okwera kwambiri, omwe ndi ouma ndipo amaomba mphepo yambiri, ndi amene amazizira kwadzaoneni m’nyengo yachisanu. Kufupi ndi zigwazi kuli chipululu china komwe sikukhala anthu ambiri. Uku, komwe ndi kum’maŵa kwa Mesopotamiya, n’kumene kunabadwira Ufumu wa Mediya ndi Perisiya.
Amedi ankakhala kumpoto m’mapiriŵa, ngakhale kuti anadzayamba kufalikira ku Armenia ndi ku Kilikiya. Koma Aperisi ankakhala kum’mwera chakumadzulo kwake, kum’maŵa kwa Chigwa cha Tigirisi. Mu ulamuliro wa Koresi, cham’katikati mwa zaka za m’ma 500 B.C.E., maufumu aŵiriŵa anagwirizana n’kupanga ufumu wamphamvu padziko lonse wa Mediya ndi Perisiya.
Koresi analanda Babulo mu 539 B.C.E. Kum’maŵa ufumu wake unafika mpaka ku Indiya. Kumadzulo kwake, ufumuwu unaphatikiza dziko la Igupto ndiponso dziko lomwe tsopano ndi Turkey. Danieli anaufotokoza bwino Ufumu wa Mediya ndi Perisiya poutcha kuti ndi “chimbalangondo” chomwe ‘chinalusira nyama zambiri.’ (Dan. 7:5) Koresi anakhazikitsa ulamuliro woganizira anthu, wololera maganizo awo. Iye anagaŵa ufumuwo m’zigawozigawo. Chigawo chilichonse chinkalamulidwa ndi kalonga yemwe nthaŵi zambiri ankakhala Mperisiya, komano pansi pa kalongayo pankakhala mtsogoleri wa m’deralo amene ankakhala ndi mphamvu ndithu. Mitundu yosiyanasiyana imene inali mu ufumuwo ankailimbikitsa kusunga miyambo yawo ndiponso kupitiriza zipembedzo zawo.
Potsatira mfundo imeneyi, Koresi analola Ayuda kubwerera kwawo kukabwezeretsa kulambira koona ndi kukamanganso Yerusalemu, malinga n’kufotokoza kwa Ezara ndi Nehemiya. Kodi mukuganiza kuti chigulu cha anthu chimenechi chinabwerera podutsa njira yomwe Abrahamu anadutsa yotsata Firate kuloŵera cha ku Karikemisi, kapena mwina anadutsa njira yaifupiko yodutsa ku Tadimori ndi ku Damasiko? Baibulo silinenapo chilichonse. (Onani masamba 6-7.) Patapita nthaŵi ndithu, Ayuda anakakhalanso kumadera ena a ufumuwo, monga ku Matsiriro a Nile ndiponso kumadera ena a kum’mwera kwambiri kwa ufumuwo. Ayuda ambiri ndithu anakhalabe ku Babulo, ndipo mwina n’chifukwa chake mtumwi Petro anadzapita kumeneko patatha zaka mazana ambiri. (1 Pet. 5:13) Inde, Ufumu wa Mediya ndi Perisiya ndiwo unachititsa kuti Ayuda azipezeka m’madera ambiri a maufumu otsatira a Girisi ndi Roma.
Atagonjetsa Babulo, Amedi ndi Aperisi anagwiritsa ntchito mudziwu, umene unali kutentha kwambiri m’chilimwe, monga likulu la boma. Mudzi wa Susani, likulu lakale la Aelamu, unali umodzi mwa midzi yachifumu. Patapita nthaŵi, kumeneku n’komwe Mfumu ya Perisiya, Ahaswero (yemwe mosakayikira anali Sasta Woyamba), inatenga Estere kukhala mkazi wake ndi kulepheretsa chiwembu chofuna kupha anthu a Mulungu mu ufumu wonse waukuluwo. Malikulu ena aŵiri a Amedi ndi Aperisi anali Ecbatana (womwe unali pamalo okwera kwambiri, mamita 1,900 ndipo nyengo yake inali yabwino kwambiri m’chilimwe) ndi Pasagade (womwenso unali pamalo okwera mofanana ndi Ecbatana, ndipo unali makilomita pafupifupi 650 kum’mwera chakum’maŵa kwa Ecbatana).
Kodi ulamuliro wamphamvu padziko lonse umenewu unatha motani? Ufumuwu utafika pachimake penipeni, Amedi ndi Aperisi anafuna kuthetsa kugalukira kumene Agiriki anayambitsa kumalire ake a kumpoto chakumadzulo. Panthaŵiyi n’kuti Girisi ali ndi mizinda yokhala ndi maboma akeake ndipo inkathirana nkhondo kwambiri. Koma mizindayi inagwirizana pofuna kugonjetsa asilikali a Aperisi pankhondo zoopsa zomwe anamenyera ku Maratoni ndi ku Salami. Izi zinayala maziko oti Girisi, monga mtundu umodzi wogwirizana, adzagonjetse Amedi ndi Aperisi.
[Bokosi patsamba 25]
Motsogozedwa ndi Zerubabele, amuna achiisrayeli pafupifupi 50,000 anayenda ulendo wobwerera ku Yerusalemu wa makilomita pakati pa 800 mpaka 1,600 (malinga ndi njira yomwe anadutsa). Iwo anakumana ndi vuto lalikulu la zachuma. Dziko lawo linakhala bwinja kwa zaka 70. Anthu obwererawo anayamba kubwezeretsa kulambira koona mwa kumanganso guwa la nsembe ndi kupereka nsembe kwa Yehova. M’nyengo ya phukutho chaka cha 537 B.C.E., anachita Madyerero a Misasa. (Yer. 25:11; 29:10) Kenako obwererawo anayala maziko a nyumba ya Yehova.
[Bokosi patsamba 25]
MABUKU A M’BAIBULO OLEMBEDWA NTHAŴIYI:
Danieli
Hagai
Zekariya
Estere
Masalmo (mbali yake ina)
1 ndi 2 Mbiri
Ezara
Nehemiya
Malaki
[Mapu patsamba 24]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Ufumu wa Mediya ndi Perisiya
A2 MAKEDONIYA
A2 THIRESI
A4 Kurene
A4 LIBIYA
B2 Bezantiyamu
B2 LIDIYA
B3 Sarde
B4 Mofi (Nofi)
B4 IGUPTO
B5 No-Amoni (Thebesi)
B5 Sevene
C3 KILIKIYA
C3 Tariso
C3 Isase
C3 Karikemesi
C3 Tadimori
C3 ASURI
C3 Sidoni
C3 Damasiko
C3 Turo
C4 Yerusalemu
D2 Phasis
D2 ARMENIA
D3 SURIYA
D3 Nineve
D4 Babulo
E3 MEDIYA
E3 Akimeta (Ecbatana)
E3 HYRCANIA
E4 Susani (Susa)
E4 ELAMU
E4 Pasagade
E4 Pesepoli
E4 PERISIYA
F3 PARTHIA
F4 DRANGIANA
G2 Maracanda (Samarkand)
G3 SOGDIANA
G3 BACTRIA
G3 ARIA
G4 ARACHOSIA
G4 GEDROSIA
H5 INDIYA
[Malo ena]
A2 GIRISI
A3 Maratoni
A3 Atene
A3 Salami
C1 SIKUTI
C4 Elati (Eloti)
C4 Tema
D4 ARABIYA
[Mapiri]
E3 MAPIRI A ELBURZ
E4 MAPIRI A ZAGROS
[Nyanja]
B3 Nyanja ya Mediterranean (Nyanja Yaikulu)
C2 Nyanja Yakuda
C5 Nyanja Yofiira
E2 Nyanja ya Caspian
E4 Nyanja ya Perisiya
[Mitsinje]
B4 Nile
C3 Firate
D3 Tigirisi
H4 Indase
[Chithunzi patsamba 24]
Asilikali a Koresi anadutsa m’Mapiri a Zagros kuti afike ku Babulo
[Chithunzi patsamba 25]
Pamwamba: Chipata cha Mitundu Yonse, ku Pesepoli
[Chithunzi patsamba 25]
Chithunzi Chaching’ono: Manda a Koresi ku Pasagade