Kodi Zonsezi Zikutanthauzanji?
YESU KRISTU anati ‘mathedwe a nthaŵi ya pansi pano’ adzadziŵika ndi nkhondo, kupereŵera kwa zakudya, miliri, ndi zivomezi.—Mateyu 24:1-8; Luka 21:10, 11.
Chiyambire 1914, moyo waipa kwambiri chifukwa cha nkhondo pakati pa mayiko ndiponso pakati pa mafuko, zomwe nthaŵi zambiri zimayamba chifukwa cha kuloŵerera m’zandale kwa atsogoleri achipembedzo, ndiponso masiku ano chifukwa cha kufala kwa uchigawenga.
Ngakhale kuti masiku ano kuli njira zamakono zamalimidwe, anthu ambiri padziko lonse lapansi alibe chakudya chokwanira. Chaka chilichonse anthu ambiri amafa chifukwa cha kupereŵera kwa zakudya.
Miliri kapena kuti matenda opatsirana amene amagwira anthu ambiri, ndi mbali inanso ya chizindikiro chimene Yesu anapereka. Nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha, mliri wa fuluwenza unapha anthu opitirira 21,000,000. Mosiyana ndi miliri ina ya m’mbuyomo imene inkakhudza dera lochepa chabe, mliri umenewu unakhudza dziko lonse lapansi, ndi zisumbu zakutali zomwe. Masiku ano Edzi ikutha anthu ambiri padziko lonse lapansi, ndipo matenda monga TB, malungo, tayifodi, ndi kolera zikuvutitsabe m’mayiko amene akungotukuka kumene.
Akuti chaka chilichonse kumakhala zivomezi zikwi zambiri zosiyanasiyana mphamvu zake. Ngakhale kuti masiku ano kuli zida ndi njira zamakono zodziŵiratu kuti kukubwera zivomezi, nkhani zokhudza ngozi zochitika m’madera okhala anthu ambiri chifukwa cha zivomezi zikumveka pafupipafupi.
Baibulo linaneneratunso kuti: “Zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.”—2 Timoteo 3:1-5.
Kodi simukuvomereza kuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa”?
Kodi mwaona kuti anthu ndi odzikonda okha, okonda ndalama, ndiponso odzikuza kwambiri?
Ndani angatsutse zoti anthu ambiri m’dzikoli ndi aliuma, osayamika, osayanjanitsika, ndiponso osayera mtima?
Kodi mukudziŵa zoti kusamvera makolo limodzi ndi kupanda chikondi chachibadwidwe kochititsa mantha kwawonjezeka kwambiri, osati m’madera ochepa okha koma padziko lonse lapansi?
Mosakayikira mukudziŵa kuti tikukhala m’dziko lodzala ndi anthu okonda zosangalatsa munthu koma osakonda zabwino. Mmenemo ndi mmene Baibulo limafotokozera mtima umene anthu adzakhale nawo mu “masiku otsiriza.”
Kodi pakufunika umboni wina wowonjezera kuti tidziŵe nthaŵi imene tikukhala? Yesu ananeneratunso kuti panthaŵi yomweyo, uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14) Kodi zimenezo zikuchitika?
Nsanja ya Olonda, magazini yofotokoza za m’Baibulo yomwe cholinga chake chachikulu ndicho kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Yehova, imafalitsidwa nthaŵi zonse m’zinenero zambiri kuposa magazini ina iliyonse yotulutsidwa nthaŵi ndi nthaŵi.
Chaka chilichonse Mboni za Yehova zimathera maola opitirira biliyoni imodzi zikulalikira kwa anthu ena za Ufumu wa Mulungu.
Mboni za Yehova zikufalitsa mabuku ofotokoza Baibulo panopa m’zinenero pafupifupi 400, ngakhale zinenero zimene amalankhula ndi anthu ochepa chabe okhala ku madera akutali. Mboni za Yehova zalalikira uthenga wabwino kwa mitundu yonse ya anthu, ndipo zalalikiranso m’zisumbu ndi madera ang’onoang’ono kwambiri amene sadziŵika n’komwe kwa anthu andale. M’mayiko ambiri, zimaphunzitsa Baibulo nthaŵi zonse.
Zoonadi, uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa padziko lonse lapansi, osati kuti anthu onse atembenuke, koma kuti ukhale umboni. Anthu kulikonse akupatsidwa mwayi woti asonyeze ngati ali ndi chidwi ndi amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndiponso ngati adzalemekeza malamulo ake n’kusonyeza kuti amakonda anthu anzawo.—Luka 10:25-27; Chivumbulutso 4:11.
Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu udzachotsa oipa onse padziko lapansi n’kulipanga kukhala paradaiso.—Luka 23:43.
[Bokosi patsamba 6]
Masiku Otsiriza a Chiyani?
Osati masiku otsiriza a kukhalapo kwa anthu onse. Baibulo likulonjeza kuti anthu amene amachita zimene Mulungu amafuna ali ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha.—Yohane 3:16, 36; 1 Yohane 2:17.
Osati masiku otsiriza a dziko lapansili. Mawu a Mulungu amalonjeza kuti dziko lapansi limene anthu akukhalamoli lidzakhalako mpaka kalekale.—Salmo 37:29; 104:5; Yesaya 45:18.
M’malo mwake, ameneŵa ndi masiku otsiriza a dongosolo la zinthu lachiwawa ndi lopanda chikondi lino ndiponso ndi masiku otsiriza a anthu amene akutsatirabe njira za dongosololi.—Miyambo 2:21, 22.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]
Kodi Baibulo Ndi Mawudi a Mulungu?
Mobwerezabwereza, aneneri a m’Baibulo analemba kuti: “Atero Yehova.” (Yesaya 43:14; Yeremiya 2:2) Ngakhale Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, anagogomezera kuti ‘sanalankhule za iye yekha.’ (Yohane 14:10) Baibulo lenilenilo limanena momveka bwino kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu.”—2 Timoteo 3:16.
Palibe buku lina limene lafalitsidwa m’zinenero zambiri kuposa Baibulo. Malinga n’kunena kwa bungwe la United Bible Societies, Baibulo lafalitsidwa m’zinenero zoposa 2,200. Palibe buku lina limene lasindikizidwa kwambiri kuposa Baibulo; mabaibulo oposa mabiliyoni anayi asindikizidwa. Kodi simukuona kuti mmenemu ndi mmene uthenga wochokera kwa Mulungu wopita kwa anthu onse uyenera kukhalira?
Kuti mumve umboni watsatanetsatane wosonyeza kuti Baibulo n’louziridwa ndi Mulungu, onani buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Ngati muŵerenga Baibulo mozindikira kuti lilidi Mawu a Mulungu, mudzapindula kwambiri.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 8]
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Ndi boma lapadera limene Mulungu woona, Yehova, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi wakhazikitsa.—Yeremiya 10:10, 12.
Baibulo limasonyeza kuti Yesu Kristu ndi amene Mulungu wamuika kukhala wolamulira boma limenelo. (Chivumbulutso 11:15) Pamene anali padziko lapansi, Yesu anasonyeza kuti anali kale ndi mphamvu zazikulu zolamulira zochokera kwa Mulungu. Mphamvu zimenezo zinamuthandiza kulamulira mphepo ndi nyanja, kuchiza matenda osiyanasiyana, ndipo ngakhale kuukitsa akufa. (Mateyu 9:2-8; Marko 4:37-41; Yohane 11:11-44) Ulosi wa m’Baibulo wouziridwa unaneneratu kuti Mulungu adzamupatsanso “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, am’tumikire.” (Danieli 7:13, 14) Boma limenelo limatchedwa Ufumu wa kumwamba, ndipo panopa Yesu Kristu akulamulira kuchokera kumwamba.
[Zithunzi patsamba 7]
Kulalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi