GAWO 1
Mulungu Angakuthandizeni Kukonzekera Tsiku Lake Lalikulu
Mneneri winawake wa Mulungu anati: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.” (Zefaniya 1:14) Tsiku limeneli latsala pang’ono kwambiri kufika, ndipo tiyenera kumakumbukira mfundo imeneyi tsiku ndi tsiku. Koma kodi mukudziwa kuti mabuku ang’onoang’ono a aneneri, oyambira pa Hoseya mpaka Malaki, ali ndi uthenga wofunika kwambiri kwa inu wokhudza tsiku lalikululi? Mutu 1 mpaka 3 wa buku lino ukuthandizani kuti muwadziwe bwino aneneri 12 amenewa komanso kuti mudziwe mfundo zikuluzikulu za uthenga wa m’mabuku awo. Choncho mungapindule ndi zimene iwo analemba chifukwa mungapeze mfundo zothandiza pa moyo wanu.