GAWO 2
Dziwani Yehova Ndipo Mutumikireni
Kodi m’mabuku 12 a aneneri muli uthenga wotani, womwe ukutichititsa kuti tizifunitsitsa kumudziwa bwino kwambiri Yehova? N’chifukwa chiyani mauthenga a Yehova, omwe aneneriwa ankalengeza ali ofunika kwambiri masiku ano? Pamene mukuphunzira Mutu 4 mpaka 7 m’buku lino, mupeza malangizo okuthandizani kulambira Mulungu m’njira yoyenera. Komanso mupeza mfundo zokuthandizani kudziwa mmene mungagwiritsire ntchito mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, mudziwa zimene Mulungu amafuna kuti muzichita posonyeza kuti ndinu wachilungamo. Zoonadi, mabuku 12 aulosiwa, akuthandizani kuti mukhale ndi moyo wabwino masiku ano.