Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 6 tsamba 14-15
  • Kodi Tikuphunzirapo Chiyani pa Zimene Zinachitika Nthawi ya Chigumula?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tikuphunzirapo Chiyani pa Zimene Zinachitika Nthawi ya Chigumula?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Chigawo 6
    Mverani Mulungu
  • Kutengerapo Chenjezo pa Zochitika Zakale
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Chigumula Chisanachitike, Kodi Ndani Anamvera Mulungu Ndipo Ndani Amene Sanamumvere?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Anayanja Nowa? Kodi Ifenso Angatiyanje?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 6 tsamba 14-15

CHIGAWO 6

Kodi Tikuphunzirapo Chiyani pa Zimene Zinachitika Nthawi ya Chigumula?

Mulungu anawononga anthu oipa koma anapulumutsa Nowa ndi banja lake. Genesis 7:11, 12, 23

Chingalawa chikuyandama, anthu oipa akumira ndipo angelo oipa akusiya matupi amene anavala

Mvula inagwa kwa masiku 40 usana ndi usiku ndipo madzi anadzaza dziko lonse lapansi. Anthu onse oipa anafa.

Angelo amene anagalukira Mulungu aja anavula matupi awo n’kuvalanso matupi auzimu ndipo anakhala ziwanda.

Nowa ndi banja lake akutuluka m’chingalawa limodzi ndi zinyama ndipo utawaleza ukuoneka

Anthu amene anali m’chingalawa aja anapulumuka. Ngakhale kuti patapita nthawi Nowa ndi anthu onse a m’banja lake anamwalira, Mulungu adzawaukitsa ndipo adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha.

Mulungu adzawononganso anthu oipa ndi kupulumutsa anthu abwino. Mateyu 24:37-39

Satana ndi ziwanda zake amasocheretsa anthu m’njira zosiyanasiyana

Satana ndi ziwanda akupitiriza kusocheretsa anthu.

Monga mmene zinalili m’nthawi ya Nowa, masiku ano anthu ambiri safuna kutsatira malangizo amene Yehova akupereka mwachikondi. Posachedwapa Yehova awononga anthu onse oipa.​—2 Petulo 2:5, 6.

A Mboni za Yehova akugwiritsa ntchito Baibulo polalikira; munthu akuwerenga Baibulo

Anthu ena ali ngati Nowa. Iwo amamvetsera ndi kuchita zimene Mulungu akunena. Anthu amenewa ndi Mboni za Yehova.

  • Sankhani njira ya kumoyo wosatha.​—Mateyu 7:13, 14.

  • Anthu oipa adzawonongedwa, koma ofatsa adzasangalala ndi mtendere wochuluka.​—Salimo 37:10, 11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena