Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • T-35 tsamba 1-4
  • Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?
  • Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?
    Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?
  • Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?
    Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?
  • Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?
    Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Onani Zambiri
Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?
T-35 tsamba 1-4
Makolo akuyang’anitsitsa zithunzi za mwana wawo wamkazi amene anamwalira

Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?

Kodi mungayankhe kuti . . .

  • inde?

  • ayi?

  • mwinamwake?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Kudzakhala kuuka.”—Machitidwe 24:15, Baibulo la Dziko Latsopano.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

Zingatilimbikitse pamene wachibale wathu wamwalira.—2 Akorinto 1:3, 4.

Sitingaopenso imfa.—Aheberi 2:15.

Tidzaonananso ndi achibale athu amene anamwalira.—Yohane 5:28, 29.

Banja komanso mayi wamasiye akulimbikitsidwa ndi chiyembekezo chakuti akufa adzauka

KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?

Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa zitatu izi:

  • Mulungu ndi amene analenga moyo. Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu ndiye “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9; Machitidwe 17:24, 25) Popeza kuti Mulungu ndi amene anapereka moyo kwa chinthu chilichonse chamoyo, sitingakayikire zoti angathe kuukitsa anthu amene anamwalira.

  • M’mbuyomu Mulungu anaukitsapo anthu. Baibulo limafotokoza nkhani za anthu 8 amene anaukitsidwa. Pa gulu la anthu amenewa panali achinyamata, achikulire, amuna ndiponso akazi. Ena mwa anthuwa anaukitsidwa pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anamwalira, koma mmodzi anaukitsidwa patatha masiku anayi ali m’manda.—Yohane 11:39-44.

  • Mulungu akufunitsitsa kuchitanso zimenezi. Yehova amadana ndi imfa, moti amaiona kuti ndi mdani. (1 Akorinto 15:26) Mulungu ‘akulakalaka’ kugonjetsa mdani ameneyu mwa kuukitsa akufa. Iye akukumbukira anthu onse amene ali m’manda ndipo akufunitsitsa kuwaonanso ali ndi moyo padziko lapansili.—Yobu 14:14, 15.

GANIZIRANI MFUNDO IYI

Mnyamata wamng’ono amakula n’kukhala bambo wachikulire

N’chifukwa chiyani timakalamba n’kufa?

Baibulo limayankha funso limeneli pa GENESIS 3:17-19 ndi pa AROMA 5:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena