Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • T-36 tsamba 1-4
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?
    Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?
  • Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?
    Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?
  • Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?
    Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?
  • Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?
    Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?
Onani Zambiri
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
T-36 tsamba 1-4
Anthu amitundu yosiyanasiyana akupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi mungayankhe kuti ndi . . .

  • chinachake chimene chimakhala mu mtima mwa munthu aliyense?

  • mawu ongophiphiritsira?

  • boma limene lili kumwamba?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.”—Danieli 2:44, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Ife tapatsidwa mwana wamwamuna, ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.”—Yesaya 9:6.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

  • Kudzakhala boma lolungama limene mudzasangalale nalo.—Yesaya 48:17, 18.

  • M’dziko latsopano anthu adzakhala angwiro, ndiponso osangalala.—Chivumbulutso 21:3, 4.

Anthu akulima ndipo akusangalala m’paradaiso padziko lapansi pomwe Ufumu wa Mulungu ukulamulira

KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?

Inde tingazikhulupirire pa zifukwa ziwiri izi:

  • Yesu anasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere komanso kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Yesu anasonyeza mmene Mulungu adzayankhire pemphero limeneli.

    Pamene Yesu anali padziko lapansi anadyetsa anthu anjala, kuchiritsa odwala ndiponso kuukitsa akufa. (Mateyu 15:29-38; Yohane 11:38-44) Zimene anachitazi zinasonyeza zimene Ufumuwo udzachitire anthu Yesu akadzayamba kulamulira dziko lapansili monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 11:15.

  • Zimene zikuchitika m’dzikoli zikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Yesu ananeneratu kuti Ufumu wa Mulungu usanabweretse mtendere padziko lapansi, m’dzikoli mudzakhala nkhondo, njala komanso zivomezi.—Mateyu 24:3, 7.

    Zimenezi ndi zomwe zikuchitika masiku ano. Choncho sitikukayikira kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uthetsa mavuto onsewa.

GANIZIRANI MFUNDO IYI

Mu Ufumu wa Mulungu dziko lapansi lidzakhala lokongola

Kodi moyo udzakhala wotani mu Ufumu wa Mulungu?

Baibulo limayankha funso limeneli pa SALIMO 37:29 ndi pa YESAYA 65:21-23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena