Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yc phunziro 14 tsamba 30-31
  • Ufumu Umene Udzalamulira Dziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufumu Umene Udzalamulira Dziko Lonse
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Yofanana
  • “Iwe Udzakhala ndi Ine m’Paradaiso”
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Kodi Ndani Adzauka kwa Akufa? Nanga Adzakhala Kuti?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Phunzitsani Ana Anu
yc phunziro 14 tsamba 30-31
Yesu Khristu akulamulira monga Mfumu m’paradaiso padziko lapansi

PHUNZIRO 14

Ufumu Umene Udzalamulire Dziko Lonse

Kodi ukuganiza kuti ufumu umenewu ndi uti?— Inde, ndi Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu udzasintha dzikoli kuti likhale Paradaiso. Kodi ungakonde kudziwa zambiri za Ufumuwu?—

Ufumu uliwonse umakhala ndi mfumu. Ndipo mfumuyo imalamulira anthu omwe ali m’dziko lake. Kodi ukudziwa amene ali Mfumu ya Ufumu wa Mulungu?— Ndi Yesu Khristu. Panopa Yesu ali kumwamba koma posachedwapa iye adzalamulira aliyense padziko lapansi. Kodi ukuganiza kuti tidzakhala osangalala Yesu akadzakhala Mfumu padziko lapansi?—

Kodi iweyo ukufuna kudzaona chiyani m’Paradaiso?

Tonse tidzakhala osangalala kwambiri. M’Paradaiso palibe amene azidzamenyana kapena kupita ku nkhondo. Anthu onse azidzakondana. Palibe amene azidzadwala kapena kumwalira. Anthu osaona adzayamba kuona, osamva adzayamba kumva ndipo anthu amene satha kuyenda adzayamba kuyenda bwinobwino komanso kudumpha. Aliyense adzakhala ndi chakudya chambiri. Zinyama sizizidzapwetekana komanso kupweteka anthu. Anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Anthu onse amene atchulidwa m’bukuli monga Rabeka, Rahabi, Davide ndi Eliya adzakhalanso ndi moyo. Kodi ukufuna kudzakumana nawo?—

Yehova amakukonda kwambiri ndipo amafuna kuti uzisangalala. Ngati utapitiriza kuphunzira za Yehova komanso kumumvera, udzakhala ndi moyo m’paradaiso mpaka kalekale. Kodi iweyo ukufuna kudzakhala ndi moyo m’paradaiso?—

WERENGANI MAVESI AWA

  • Yesaya 2:4; 11:6-9; 25:8; 33:24; 35:5, 6

  • Yohane 5:28, 29; 17:3

MAFUNSO:

  • Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndi ndani?

  • Kodi Yesu azidzalamulira ndani?

  • Kodi zinthu zidzakhala bwanji Yesu akadzayamba kulamulira dziko lapansi?

  • Ngati ukufuna kudzakhala ndi moyo m’paradaiso, kodi uyenera kuchita chiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena