Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 16 tsamba 44-tsamba 45 ndime 4
  • Kodi Yobu Anali Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yobu Anali Ndani?
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yobu Analemekeza Dzina la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Yembekezera Yehova”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Yobu Anapirira—Nafenso Tingatero!
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mwamuna Wachitsanzo Chabwino Amene Anavomera Kum’langiza
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 16 tsamba 44-tsamba 45 ndime 4
Yobu ali ndi zilonda thupi lonse ndipo anthu atatu apita kukamuona

MUTU 16

Kodi Yobu Anali Ndani?

Kudziko lina lotchedwa Uzi kunali munthu wina amene ankalambira Yehova. Dzina lake anali Yobu. Iye anali ndi banja lalikulu ndipo anali wolemera kwambiri. Yobu anali wokoma mtima ndipo ankathandiza anthu osauka, azimayi amasiye komanso ana amasiye. Koma kodi iye sakanakumana ndi mavuto chifukwa choti anali munthu wabwino? Ayi.

Satana Mdyerekezi

Satana Mdyerekezi ankaona zonse zimene Yobu ankachita, ngakhale kuti Yobuyo sankadziwa zimenezi. Yehova anauza Satana kuti: ‘Kodi waona mtumiki wanga Yobu? Padziko lapansi palibe munthu wolungama ngati iyeyu. Iye amandimvera komanso amachita zoyenera.’ Satana anayankha kuti: ‘N’zoona kuti Yobu amakumverani. Koma n’chifukwa choti mumamuteteza komanso kumudalitsa. Mwamupatsa malo abwino komanso ziweto. Koma mutamulanda zinthu zimenezi akhoza kusiya kukulambirani.’ Yehova anati: ‘Ndakulola kuti umuyese, koma usamuphe.’ N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti Satana ayese Yobu? N’chifukwa choti ankadziwa kuti Yobu akhalabe wokhulupirika.

Satana anayamba kuyesa Yobu pomubweretsera mavuto osiyanasiyana. Choyamba anachititsa kuti anthu otchedwa Asabeya abe ng’ombe ndi abulu a Yobu. Kenako moto unatentha nkhosa zake. Ndiye panabweranso anthu otchedwa Akasidi amene anadzaba ngamila zake zonse. Komanso antchito amene ankayang’anira ziweto za Yobu anaphedwa. Komatu si zokhazi. Tsiku lina ana onse a Yobu anali m’nyumba ina n’kumachita phwando. Koma mwadzidzidzi nyumbayo inagwa n’kupha onsewo. Yobu anamva chisoni kwambiri ndi zonsezi komabe sanasiye kulambira Yehova.

Satana anaganiza kuti Yobu akhoza kusiya kumvera Mulungu atakumana ndi mavuto enanso. Choncho anachititsa kuti Yobu atuluke zilonda zowawa kwambiri thupi lonse. Yobu anali pa ululu woopsa. Iye sankadziwa chimene chinkachititsa zonsezi koma anapitiriza kulambira Yehova. Mulungu ankaona zonsezi ndipo anasangalala kwambiri kuona kuti Yobu anakhalabe wokhulupirika.

Kenako Satana anatumiza azibambo atatu kuti akayese Yobu. Iwo anauza Yobu kuti: ‘Uyenera kuti unachimwira Mulungu ndipo unabisa. Ndiye Mulungu akukulanga chifukwa cha zimenezo.’ Yobu anati: ‘Palibe chilichonse cholakwika chimene ndinachita.’ Koma zitatere Yobu anayamba kuganiza kuti Yehova ndi amene akuchititsa mavuto ake ndipo sakuchita chilungamo.

Munthu wina wamng’ono kuposa azibambo atatu aja, dzina lake Elihu, ankangomvetsera pamene anthuwa ankakambirana. Koma kenako anayankha kuti: ‘Zimene nonsenu mukunena si zoona. Yehova ndi wapamwamba kwambiri ndipo anthufe sitingathe kumvetsa zochita zake zonse. Iye sangachite zinthu zoipa. Amaona zonse ndipo anthu akamavutika amawathandiza.’

Yobu ndi mkazi wake ali ndi mwana

Ndiyeno Yehova analankhula ndi Yobu kuti: ‘Kodi unali kuti pamene ndinkalenga kumwamba ndi dziko lapansi? N’chifukwa chiyani ukunena kuti ndikuchita zinthu zopanda chilungamo? Ukungolankhulatu zinthu zimene sukuzidziwa.’ Yobu anazindikira kuti ankaganiza molakwika ndipo anati: ‘Pepani ndalakwa. Ndinkangomva za inu, koma panopa ndakudziwani. Palibe chimene simungathe kuchita. Mundikhululukire chifukwa cha zomwe ndinanena.’

Kenako mayesero a Yobu anatha ndipo Yehova anamuchiritsa. Anamupatsanso zinthu zambiri kuposa zomwe anali nazo poyamba. Yobu anakhala ndi moyo wosangalala komanso wautali. Yehova anamudalitsa chifukwa choti ankamumvera ngakhale pa mavuto. Kodi iwenso ungakhale ngati Yobu n’kumalambira Yehova zivute zitani?

“Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mukudziwa madalitso amene Yehova anamupatsa.”​—Yakobo 5:11

Mafunso: Kodi Satana anachititsa kuti Yobu akumane ndi mayesero ati? Kodi Yehova anadalitsa bwanji Yobu?

Yobu 1:1–3:26; 4:7; 32:1-5; 34:5, 21; 35:2; 36:15, 26; 38:1-7; 40:8; 42:1-17

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena