MUTU 28
Bulu wa Balamu Analankhula
Aisiraeli atakhala m’chipululu zaka pafupifupi 40, anagonjetsa mizinda yambiri yamphamvu. Kenako anamanga misasa yawo m’chipululu cha Mowabu cha kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano. Nthawi yoti alowe m’dziko lolonjezedwa inali itakwana. Ndiyeno mfumu ya Mowabu dzina lake Balaki anaopa kwambiri podziwa kuti dziko lake ligonjetsedwa. Choncho anaitanitsa munthu wina dzina lake Balamu kuti adzatemberere Aisiraeli.
Koma Yehova anauza Balamu kuti: ‘Aisiraeliwo usawatemberere.’ Choncho Balamu anakana kupita ku Mowabu. Mfumu ija inamuitananso kachiwiri n’kumulonjeza kuti imupatsa chilichonse chimene angafune. Koma Balamu anakanabe. Kenako Mulungu anamuuza kuti: ‘Ukhoza kupita, koma ukalankhule mawu okhawo amene ndikakuuze.’
Ndiyeno Balamu ananyamuka pa bulu wake kupita ku Mowabu. Mumtima mwake ankafuna kukatembereradi Aisiraeli ngakhale kuti Yehova anamuuza kuti asakachite zimenezo. Mngelo wa Yehova anakumana naye katatu panjira imene anadutsayo. Balamu sankaona mngeloyu koma bulu wake ankamuona. Poyamba, buluyo anapatuka n’kudutsa m’munda. Kachiwiri buluyo anapatukanso n’kudutsa pafupi ndi mpanda moti anakanikizira phazi la Balamu kukhoma. Kachitatu, buluyo anangogona pakati pa msewu. Maulendo onsewa Balamu ankamenya buluyo ndi ndodo.
Ulendo wachitatuwu, Yehova anachititsa kuti buluyo alankhule. Buluyo anafunsa Balamu kuti: ‘Kodi iwe ukundimenyeranji?’ Balamu anamuyankha kuti: ‘Chifukwa wandipusitsa, moti ndikanakhala ndi lupanga bwenzi pano nʼtakupha.’ Buluyo anati: ‘Ndakhala ndikuyenda nawe kwa zaka zambiri. Kodi ndinayamba ndachitapo zimenezi?’
Kenako Yehova anachititsa kuti Balamu aone mngeloyo. Ndiyeno mngeloyo anati: ‘Kodi Yehova sanakuuze kuti usakatemberere Aisiraeli?’ Balamu anayankha kuti: ‘Pepani ndalakwa. Ndibwerera.’ Mngeloyo anati: ‘Pita ku Mowabu koma ukanene zokhazo zimene Yehova angakuuze.’
Kodi Balamu anaphunzirapo chilichonse? Ayi. Pambuyo pake Balamu anayesa kutemberera Aisiraeli maulendo atatu. Koma Yehova anamuchititsa kuti awadalitse m’malo mowatemberera. Kenako, Aisiraeli anagonjetsa dziko la Mowabu ndipo Balamu anaphedwa. Iye akanamvera Yehova, zinthu zikanamuyendera bwino.
“Khalani maso ndipo chenjerani ndi dyera lamtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera mʼzinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15