Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 55 tsamba 132
  • Mngelo wa Yehova Anateteza Hezekiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mngelo wa Yehova Anateteza Hezekiya
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • “Usaope Ndidzakuthandiza”
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Hezekiya Anadalitsidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 55 tsamba 132
Mngelo akupha asilikali pamsasa wa Asuri

MUTU 55

Mngelo wa Yehova Anateteza Hezekiya

Senakeribu yemwe anali mfumu ya Asuri anagonjetsa ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10. Ndiyeno ankafunanso kugonjetsa ufumu wa Yuda wa mafuko awiri. Iye anayamba kugonjetsa mizinda ya Yuda. Mzinda umene ankaufunitsitsa unali wa Yerusalemu. Koma Senakeribu sankadziwa kuti Yehova ankateteza mzindawu.

Hezekiya, yemwe anali mfumu ya Yuda, anapereka ndalama zambiri kwa Senakeribu kuti asalande mzinda wa Yerusalemu. Senakeribu analandira ndalamazo, komabe anatumiza gulu la asilikali ake kuti akagonjetse Yerusalemu. Anthu a mumzindawo atamva kuti asilikaliwo atsala pang’ono kufika, anachita mantha kwambiri. Koma Hezekiya anawauza kuti: ‘Musachite mantha. N’zoona kuti Asuri ndi amphamvu, komabe Yehova atithandiza.’

Senakeribu anatumiza Rabisake kuti apite ku Yerusalemu kukalankhula ndi Ayuda. Rabisake anaima panja pa mzindawu n’kukuwa kuti: ‘Inutu Hezekiya asakupusitseni. Yehova sangakuthandizeni. Palibe mulungu amene angatilepheretse kukugonjetsani!’

Hezekiya anapempha Yehova kuti amuthandize kudziwa zoyenera kuchita. Yehova anayankha kuti: ‘Musaope zimene Rabisake akunenazo. Senakeribu sangagonjetse Yerusalemu.’ Kenako Hezekiya analandira makalata ochokera kwa Senakeribu. M’makalatawo munali mawu akuti: ‘Tangonenani kuti mwagonja. Yehovatu sakupulumutsani.’ Zitatero Hezekiya anapemphera kuti: ‘Chonde Yehova tipulumutseni kuti aliyense adziwe kuti inu nokha ndinu Mulungu woona.’ Yehova anamuuza kuti: ‘Mfumu ya Asuri sifika ku Yerusalemu. Ineyo nditeteza mzinda wangawu.’

Senakeribu ankaona kuti agonjetsa Yerusalemu basi. Koma usiku wina, Yehova anatumiza mngelo kumalo amene asilikali a Asuri ankagona. Mngeloyo anapha asilikali 185,000. Asilikali onse amphamvu a Senakeribu anathera pomwepo. Zitatero Senakeribu anadziwa kuti wagonja ndipo anangouyamba ulendo wobwerera kwawo. Apa ndiye kuti Yehova anakwaniritsa lonjezo lake loti adzateteza Hezekiya komanso mzinda wa Yerusalemu. Kodi iweyo ukanakhala ku Yerusalemu, ukanadalira Yehova?

“Mngelo wa Yehova amamanga msasa kuzungulira anthu onse amene amaopa Mulungu, ndipo amawapulumutsa.”​—Salimo 34:7

Mafunso: Kodi Yehova anateteza bwanji Yerusalemu? Kodi iweyo umakhulupirira zoti Yehova angakuteteze?

2 Mafumu 17:1-6; 18:13-37; 19:1-37; 2 Mbiri 32:1-23

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena