Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 86 tsamba 200-tsamba 201 ndime 1
  • Yesu Anaukitsa Lazaro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anaukitsa Lazaro
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Munthu Amene Anali Wakufa Masiku Anai
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Yesu Sanapite Mofulumira?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Chimachitika ndi Chiyani Tikamwalira?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • “Ndimakhulupirira”
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 86 tsamba 200-tsamba 201 ndime 1
Lazaro waukitsidwa ndipo ali ndi azichemwali ake, Mariya ndi Malita

MUTU 86

Yesu Anaukitsa Lazaro

Yesu anali ndi anzake atatu apamtima amene ankakhala ku Betaniya. Anzakewo anali Lazaro ndi azichemwali ake awiri, Mariya ndi Marita. Tsiku lina, Yesu ali kutsidya lina la Yorodano, Mariya ndi Marita anamutumizira uthenga wakuti: ‘Lazaro akudwala mwakayakaya. Chonde mubwere mwamsanga.’ Koma Yesu sanapite nthawi yomweyo. Anakhalabe masiku awiri kenako anauza ophunzira ake kuti: ‘Tiyeni ku Betaniya. Lazaro akugona ndiye ndikufuna ndikamudzutse.’ Atumwiwo ananena kuti: ‘Ngati Lazaroyo akugona zimuthandiza kuti apeze bwino mwamsanga.’ Apa tsopano Yesu anawauza kuti: ‘Lazaro wamwalira.’

Pamene Yesu ankafika ku Betaniya n’kuti Lazaro atakhala m’manda masiku 4. Kunali anthu ambiri amene anabwera kudzatonthoza Marita ndi Mariya. Marita atamva kuti Yesu akubwera, anapita kukamuchingamira ndipo atakumana naye anati: ‘Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wanga sakanamwalira.’ Yesu anamuyankha kuti: ‘Mchimwene wako auka. Ukukhulupirira zimenezi Marita?’ Iye ananena kuti: ‘Eya, ndikukhulupirira kuti adzauka pa tsiku lomaliza.’ Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: ‘Ine ndine kuuka ndi moyo.’

Kenako Marita anapita kukauza Mariya kuti: ‘Yesu wabwera.’ Mariya anathamangira kwa Yesu ndipo gulu la anthu linamutsatira. Mariya anagwada pafupi ndi Yesu ndipo ankangolira. Kenako anati: ‘Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wathu sakanamwalira.’ Yesu ataona kuti Mariya ali ndi chisoni kwambiri, nayenso anayamba kulira. Anthu ataona kuti Yesu akugwetsa misozi anati: ‘Taonani, koma ndiyetu Yesu ankamukonda kwambiri Lazaro.’ Koma ena anayamba kufunsa kuti: ‘Ndiye n’chifukwa chiyani sanamuthandize kuti asafe?’ Kodi Yesu anatani?

Yesu ndi anthuwo anapita kumanda ndipo anapeza kuti pamandapo atsekapo ndi chimwala. Iye anauza anthu kuti: ‘Chotsani chimwalachi.’ Koma Marita anati: ‘Wakhalatu m’manda kwa masiku 4. Ayenera kuti wayamba kununkha.’ Koma anthu anachotsabe mwalawo ndipo Yesu anapemphera kuti: ‘Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse, koma ndikupemphera mokweza chonchi kuti anthuwa adziwe zoti inuyo munanditumiza.’ Kenako anafuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Atatero panachitika zodabwitsa. Lazaro uja anatuluka ali wokulungidwa ndi nsalu zamaliro. Yesu anati: “Mʼmasuleni kuti athe kuyenda.”

Anthu ambiri amene anaona zimenezi anakhulupirira Yesu. Koma ena anapita kukauza Afarisi ndipo Afarisiwo anayamba kufuna kupha Lazaro ndi Yesu. Mmodzi mwa atumwi 12 aja dzina lake Yudasi, anazemba n’kupita kwa Afarisi kukawauza kuti: ‘Mundipatsa ndalama zingati ndikakuthandizani kupeza Yesu?’ Anagwirizana naye kuti amupatsa ndalama 30 zasiliva. Choncho Yudasi anayamba kufufuza mpata woti apereke Yesu.

“Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa. Ndipo Yehova Ambuye Wamkulu Koposa amatipulumutsa ku imfa.”—Salimo 68:20

Mafunso: Fotokozani zimene zinachitika kuti Yesu aukitse Lazaro. Kodi Afarisi ankafuna kuchita chiyani atamva kuti Lazaro waukitsidwa?

Mateyu 26:14-16; Yohane 11:1-53; 12:10

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena