NYIMBO 37
Kutumikira Yehova Ndi Moyo Wonse
Losindikizidwa
1. Yehova Wamphamvuyonse
Ineyo ndimakukondani.
Ndikufuna n’kutumikireni
Ndi mtima wanga wonse.
Ndizimvera mawu anu ndi
Kuchita zofuna zanu.
(KOLASI)
Inu Yehova ndinu woyenera
Kutumikiridwa.
2. Atate zomwe munalenga
Zimakulemekezani.
Ndidzalengeza za inu
Kwa ena mokhulupirika.
Yehova muzindithandiza
Kuti ndikhulupirike.
(KOLASI)
Inu Yehova ndinu woyenera
Kutumikiridwa.
(Onaninso Deut. 6:15; Sal. 40:8; 113:1-3; Mlal. 5:4; Yoh. 4:34.)