NYIMBO 53
Kukonzekera Kupita Kokalalikira
Losindikizidwa
1. Tsopano
Kunja kwacha
Tikalalikiretu.
Komano mvula
Ikuyamba kugwa,
N’zosavuta kupitiriza
Kugona.
(KOLASI)
Tisafooke tikonzeke.
Tipemphe Yehova
Kuti azitilimbikitsa
Pokonzeka.
Tipezenso woyenda naye
Wotilimbikitsa.
Angelo atitsogolera
Tikwanitsa.
2. Tipeza
Chimwemwedi
Ngati sitifooka.
Ndipo Yehova
Amaona zonse,
Iye saiwala chikondi
Chathuchi.
(KOLASI)
Tisafooke tikonzeke.
Tipemphe Yehova
Kuti azitilimbikitsa
Pokonzeka.
Tipezenso woyenda naye
Wotilimbikitsa.
Angelo atitsogolera
Tikwanitsa.
(Onaninso Mlal. 11:4; Mat. 10:5, 7; Luka 10:1; Tito 2:14.)