NYIMBO 131
“Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”
Losindikizidwa
1. Chingwe cholimbadi
Chamangidwa lero.
Mulungu ndi anthufe
Tamva malumbiro.
(KOLASI 1)
Mwamuna walumbira
Kukonda mkaziyu.
“Chomwe M’lungu wamanga,
Musalekanitse.”
2. Onse afufuza
M’Mawu a Mulungu,
Kuti akwaniritse
Zomwe alumbira.
(KOLASI 2)
Mkazinso walumbira
Kukonda mwamuna.
“Chomwe M’lungu wamanga,
Musalekanitse.”
(Onaninso Gen. 2:24; Mla. 4:12; Aef. 5:22-33.)