Loweruka
‘Menya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro’—Yuda 3
M’MAWA
9:20 Kuonera Vidiyo ya Nyimbo
9:30 Nyimbo Na. 57 ndi Pemphero
9:40 NKHANI YOSIYIRANA: Anthu Opanda Chikhulupiriro Akhoza Kusintha N’kukhala ndi Chikhulupiriro
• Anthu a ku Nineve (Yona 3:5)
• Abale Ake a Yesu (1 Akorinto 15:7)
• Anthu Otchuka (Afilipi 3:7, 8)
• Anthu Osapembedza (Aroma 10:13-15; 1 Akorinto 9:22)
10:30 Muzilimbitsa Chikhulupiriro Chanu Pogwiritsa Ntchito Buku Lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale (Yohane 17:3)
10:50 Nyimbo Na. 67 ndi Zilengezo
11:00 NKHANI YOSIYIRANA: Anthu Omwe Apambana pa Nkhondo Yachikhulupiriro
• Amene Ali pa Banja Ndi Munthu Wosakhulupirira (Afilipi 3:17)
• Amene Akuleredwa Ndi Kholo Limodzi (2 Timoteyo 1:5)
• Akhristu Omwe Sali pa Banja (1 Akorinto 12:25)
11:45 NKHANI YA UBATIZO: Kukhala Ndi Chikhulupiriro N’kofunika Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha (Mateyu 17:20; Yohane 3:16; Aheberi 11:6)
12:15 Nyimbo Na. 79 ndi Kupuma
MASANA
1:35 Kuonera Vidiyo ya Nyimbo
1:45 Nyimbo Na. 24
1:50 NKHANI YOSIYIRANA: Mmene Abale Athu Akusonyezera Chikhulupiriro ku . . .
• Africa
• Asia
• Europe
• North America
• Oceania
• South America
2:15 NKHANI YOSIYIRANA: Lowani pa Khomo la Utumiki Mwachikhulupiriro
• Phunzirani Chilankhulo China (1 Akorinto 16:9)
• Samukirani Kumene Kukufunika Olalikira Ufumu Ambiri (Aheberi 11:8-10)
• Funsirani Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu (1 Akorinto 4:17)
• Thandizani pa Ntchito Yazomangamanga (Nehemiya 1:2, 3; 2:5)
• ‘Muziika Kenakake Pambali’ Kothandizira pa Ntchito ya Yehova (1 Akorinto 16:2)
3:15 Nyimbo Na. 84 ndi Zilengezo
3:20 VIDIYO: Danieli Anali Munthu Wachikhulupiriro Cholimba— Mbali Yoyamba (Danieli 1:1–2:49; 4:1-33)
4:20 ‘Menya Mwamphamvu Nkhondo Yachikhulupiriro’ (Yuda 3; Miyambo 14:15; Aroma 16:17)
4:55 Nyimbo Na. 38 ndi Pemphero Lomaliza