Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/15 tsamba 21-23
  • Thandizo M’kupanga Zosankha za Nzeru

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizo M’kupanga Zosankha za Nzeru
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Phunzirani Kuchokera ku Zochitika Kale
  • Kuyang’anizana ndi Chosankha
  • Kupindula Kuchokera ku Uphungu Wanzeru
  • Musakhale Osadziwa Machenjera a Satana
  • Kodi Umodzi wa Akristu Umalira Kuchita Chilichonse Mofanana?
    Galamukani!—2003
  • “Muzindikire Otere”
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Mpingo Uyenera Kulimbikitsidwa
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Mpingo Ungatsanzire Bwanji Maganizo a Yehova pa Nkhani ya Anthu Ochimwa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/15 tsamba 21-23

Thandizo M’kupanga Zosankha za Nzeru

ALICE anapanga chosankha chopanda nzeru chomwe chinafikira ku mapeto osakaza. “Ndinadzilekanitsa inemwini kuchokera kwa Yehova ndi gulu lake,” iye akuvomereza. Ngakhale kuti iye pomalizira anabwerera, chinamutengera iye zaka zoposa 13 kuchita tero​- “zaka za chisoni” iye akuzitcha izo.

Mkristu sayenera kupeputsa kuopsya kwa kupanga zosankha zopanda nzeru m’chigwirizano ndi utumiki wake kwa Mulungu. Sichiri chakuti zosankha zoipa zimapangidwa mwadala pambuyo pa kulingalira nsonga zoyenerera. Nthaŵi zina izo zimapangidwa kokha pa maziko akugwira ntchito kwa maganizo a chibadwa. Pamene malingaliro apambana mkuphimba nkhani ndipo mtima wopanda ungwiro upereka chilimbikitso chosayenera pa kuthekera kwa kulingalira, mtundu uliwonse wakusakaza ndi chisoni ungatulukepo.

Indedi, “mtima ndiwo wonyenga koposa.”(Yeremiya 17:9) Baibulo, ngakhale kuli tero, limatiuza ife mmene tingadzichinjirizire ife eni. “Pakuti nzeru idzalowa m’mtima mwako,” ilo likutero, “kulingalira kudzakudikira.” (Miyambo 2:10, 11) Koma kodi ndimotani mmene tingapangire nzeru kulowa m’mtima mwathu?

Phunzirani Kuchokera ku Zochitika Kale

Yesani ichi. Dziikeni inumwini m’mkhalidwe wa atumiki oyambirira a Mulungu omwe anayang’anizana ndi mikhalidwe yoyesa yofanana ndi yanu. Talingalirani, mwachitsanzo, kuti mkhalidwe mkati mwa mpingo Wachikristu wa kumaloko ukukupangitsani inu kudera nkhaŵa. Yesani kulingalira za mkhalidwe wofananawo wotchulidwa mu Baibulo.

Bwanji ponena za mpingo Wachikristu wa mu zana loyamba ku Korinto? Talingalirani kuti inu mmi chiwalo cha mpingo wa Korinto. Mwakhala muli Mkristu kwa zaka ziŵiri kapena zitatu. Chinali chimwemwe chotani nanga kufika ku chidziŵitso cha chowonadi mkati mwa kukhalako kwa miyezi 18 kwa Paulo kumeneko! Koma tsopano, zinthu zikuwoneka moipa.

Chikhoterero cha kupanga timagulu ndi magulu a dyera akupangitsa kusagwirizana mkawonedwe ka zinthu pa mpingo, kuopsyeza umodzi wake. (1 Akorinto 1:10, 11) Kulekelera kwa mkhalidwe woipa wa chisembwere kukuika pangozi mzimu wake. (1 Akorinto 5:1-5 Kuwonetsera kwa pabwalo kwa kusiyana pakati pa ziwalo za mpingo pamaso pa mabwalo amilandu alamulo a dziko kukuwononga mkhalidwe wake wabwino.​—1 Akorinto 6:1-8.

Mukudzilingalirabe inumwini muli mu Korinto wakale, muli wodera nkhawa kuti ziwalo zina za mpingo nthawi zonse zimakangana pa nkhani zomwe ziri zosafunika kwenikweni. (Yerekezani ndi 1 Akorinto 8:1-13. ) Muli womvetsedwa chisoni ndi chotetana, kaduka, mikwiyo, ndi kusagwirizana kumene mukuwona. (2 Akorinto 12:20) Indedi, muli wovutitsidwa ndi odzikuza ochepa amene akupanga kukhala kwa Chikristu kukhala kovutitsitsa. (1 Akorinto 4:6-8) Muli woipidwa mtima kumva kuti ena akukaikira ngakhale malo a mtumwi Paulo ndi ulamuliro, kumapanga zinenezo zabodza, ndipo kumamuseka chifukwa cha kusoweka kwake kwa kufotokoza monga mlankhuli. (2 Akorinto 10:10; 12:16) Muli wodera nkhawa kwenikweni kuti mwina awo amene mwapoyera amapititsa patsogolo malingaliro aumwini angapepukitse chikhulupiriro cha mpingo mu chiphunzitso choyambirira.​—1 Akorinto 15:12.

Kuyang’anizana ndi Chosankha

Ichi kokha sichiyenera kukhala tero,’ mukuusa moyo. ‘Nchifukwa ninji akulu sakuwongolera zinthu? China chake chalakwika kwambiri.’

Kodi mudzachokamo mu mpingo wa Korinto, muli kumamaliza kuti mungakhale bwino mukumatumikira Mulungu kwina kwake? Kapena kodi inu mwinamwake mungaganize kuti chiri chabwino kwambiri kusiya kuyanjana ndi Akristu anzanu? Kodi inu mudzalola mavuto amenewa kuchepetsa chimwemwe chanu ndi chidaliro chanu kuti Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ali oyang’anira a zinthu? Kodi mudzakulitsa mzimu wosuliza, wodandaula, kupangitsa inu kukaikira zolinga za Akristu anzanu? Kodi inu mudzafooka mu ntchito ya kulalikira, mukumalingalira kuti pali nsonga yochepa ya kutsogozera okondwerera ku mpingo umenewo?

Kuyang’ana mkhalidwewo mosasonkhezeredwa ndi wina wake kuchokera kukawonedwe ka lerolino, mungachipeze icho kukhala chapafupi kunena kuti chosankha chanu chingakhale mokhulupirika kukhala kufupi ndi mpingo wa Mulungu, mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwake. Koma ngati mutayang’anizana ndi mkhalidwe wofananawo lerolino, kodi mudzakhala okhoza kupitirizabe kusunga kawonedwe kabwino ndi mtima wofatsa? Kodi mudzalingalira lerolino monga mmene mukuganizira kuti mukanalingalirira ngati mukanakhalako nthawi imeneyo?

Kupindula Kuchokera ku Uphungu Wanzeru

Akristu a ku Korinto amene anapanga chosankha chanzeru anali awo amene anakhala kufupi ndi mpingo. Iwo anadzimva monga mmene anachitira Petro zaka zingapo poyambirira. Pamene ena a ophunzira anasiya kuyanjana ndi Yesu, Petro anati: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha, ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.” (Yohane 6:68 , 69) Mwachiwonekere, kokha mwakukhala pafupi ndi gulu la Mulungu tingapindule kuchokera ku uphungu wake.

M’mipingo yatsopano, monga uja wa mu Korinto, sichiri chachilendo ponena za kupanda ungwiro kwa anthu kuyambitsa mavuto omwe angafunikire kupereka uphungu wamphamvu. Koma mkupereka uphungu kwa Akristu a ku Korinto, Paulo anakumbukira kuti ambiri a iwo anali “okondedwa.” (1 Akorinto 10:14; 2 Akorinto 7:1; 12:19) Iye sanaiwale kuti Yehova amapereka chisomo ndi chikhululukiro kwa awo amene amavomereza ku chitsogozo chake.​—Masalmo 130:3, 4.

Komabe, popeza mpingo Wachikristu umakopa mitundu yonse ya anthu, ena amatenga nthawi yaitali kuvomereza ku chitsogozo chimenechi kusiyana ndi ena. Ichi chiri chowona kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana. Masinthidwe ena ali ovuta kwambiri kuwapanga kusiyana ndi ena. Ndiponso, munthu aliyense pa yekha ali wosiyana mkapangidwe ka kuthupi ndi m’maganizo, malo otizinga, mayambidwe, ndi mikhalidwe. Chotero chiri chanzeru chotani nanga kupewa kukhala wosuliza wopambanitsa ndi kukumbukira kuti “chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo”! (1 Petro 4:8) Ndiponso, ngati Yehova ndi Mwana wake ali ofunitsitsa kuchita nako kupanda ungwiro kwa munthu ndi kusakula msinkhu mu mpingo wawo, kodi ife sitiyenera kusonyeza mzimu wofananawo?—1 Akorinto 13:4-8; Aefeso 4:1, 2.

Ngati inu munalimo mu mpingo wa Korinto wakale, kumvetsera ku uphungu wachikondi koma wamphamvu wa Paulo kukanakukumbutsani inu kuti Kristu, monga mutu wa mpingo Wachikristu, ali mowonadi wosangalatsidwa mu ubwino wake. (Mateyu 28:20) Iwo ukanamangirira chidaliro chanu mu lonjezo la Yesu la kusunga otsatira ake ogwirizana pamene akuvomereza ku thandizo loperekedwa kupyolera mwa wkapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47; Aefeso 4: 11-16) Inde, ndipo mawu a Paulo akanakuthandizani inu kusunga chimwemwe ndi kukhazikika ngakhale pansi pa mikhalidwe yoyesa. Mukakhala ndi chidaliro kuti Mulungu adzakupatsani inu mphamvu kuchita nachochovuta chirichonse chimene iye kwakanthawi angachilole kukhalapo.

Uku sindiko kunena kuti Mkristu sayenera kuchita kanthu ngati mkhalidwe woipa wabuka mu mpingo. Kubwerera m’mbuyo mu Korinto, amuna achikulire monga Stefana, Fortunato, Akayiko, ndi ena ochokera mnyumba ya Kloe, anachitapo kanthu. Iwo mwachidziwikire anachenjeza Paulo za mkhalidwewo. (1 Akorinto 1:11; 5:1; 16:17) Koma pamene anachita tero, iwo mwachidaliro anasiya nkhaniyo m’manja mwake. Changu kaamba ka chilungamo sichinapangitse iwo kutaya chidaliro mu umutu wa Kristu kapena kukhala “odandaula pa Yehova.”​—Miyambo 19:3.

Changu chathu kaamba ka chilungamo lerolino chidzatiletsa ife kuchokera ku kulingalira ngakhale ku chosankha cha kuzilala mu ntchito yathu yopatsidwa ndi Mulungu ya kulalikira mbiri yabwino. Kuchita tero kudzasonyeza kusoweka kwa kudera nkhawa kaamba ka ubwino wa ena ndipo kungakhale kulephera kuchita zimene Kristu akufuna kuti tichite. “Chifukwa chake abale anga okondedwa,” Paulo akupereka uphungu, “khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.”​—1 Akorinto 15:58.

Musakhale Osadziwa Machenjera a Satana

Mavuto a mpingo monga ngati awo amene anapezeka mu Korinto nthawi zina angakhale ovuta kwambiri kuwasamalira kuposa chizunzo. Satana amatengera mwawi mikhalidwe yoteroyo mu kuyesa kwake kutipangitsa ife kupanga zosankha zolakwa zomwe zidzatikokera ife kutali ndi Yehova. Koma ‘sitikhala osadziwa machenjero ake.’​—2 Akorinto 2:11.

Paulo anauza Akristu a ku Korinto kuti iwo angapindule kuchokera kukusanthula mbiri ya atumiki oyambirira a Mulungu. “Koma izi zinachitika kwa iwowa monga [zitsanzo, NW],” iye ananena za Aisrayeli, “ndipo zina lembedwa kutichenjeza ife amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.”(1 Akorinto 10:11) Mofananamo, ife lerolino tingapindule kuchokera kukusanthula kosamalitsa mbiri ya Akristu oyambirira. Mwachitsanzo, tingalingalire nchiyani chimene chinachitika mu Korinto. Kusinkhasinkha ponena za ndimotani mmene tikanapangira zosankha zabwino nthawiyo kungatithandize ife kupewa kupanga zosankha zolakwa tsopano.

Pambuyo pa “zaka 13 za chisoni” za kusakhalako, Alice akunena za msonkhano wake woyamba mu Nyumba ya Ufumu: “Ndinachita mantha kulankhula kuwopera kuti ndingalire. Ndinali kunyumba​—kunyumba kwenikweni. Sindikanakhulupirira icho.” Chotero khalani otsimikizira, mosasamala kanthu za mavuto omwe angabuke, kumamatira kuchosankha chanu chanzeru chakusasiya gulula Yehova! Madalitso anu mkuyanjana ndianthu a Mulungu adzakhala ochuluka. Ndipo iwo adzakhala opanda mapeto.​—Miyambo 2: 10-15, 20, 21

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena