Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 7/15 tsamba 15-20
  • Mapemphero Amafunikira Zintchito

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapemphero Amafunikira Zintchito
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chimene Mapemphero Amafunikira Ntchito
  • Zitsanzo Zina Zamakedzana
  • Chitsanzo cha Yesu
  • Kugwiritsira Ntchito Prinsipulo
  • Pemphero ndi Umboni Wathu
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Mapemphero Amene Amayankhidwa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mmene Mungapezere Chithandizo Kupyolera mwa Pemphero
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 7/15 tsamba 15-20

Mapemphero Amafunikira Zintchito

Yehova atalikira oipa; Koma pemphero la Olungama alimvera.”​—MIYAMBO15:29

1. Kodi ndi mkhalidwe umodzi uti umene uyenera kufikiridwa ngati Mulungu ayenera kuyankha mapemphero athu?

ZIFUNO zonse za Yehova ndi zanzeru, zolungama, ndi za chikondi. Izo siziri zolemetsa. (1 Yohane 5:3) Icho chimaphatikizapo zifuno zake ponena za pemphero, chimodzi cha izo chiri chakuti tiyenera kutsogoza miyoyo yathu m’chigwirizano ndi mapemphero athu. Njira yathu ya kachitidwe iyenera kukondweretsa Yehova Mulungu. Kupanda apo, kodi ndimotani mmene tingamuyembekezerere kulingalira mapemphero athu ndi mapembedzero ndi chiyanjo?

2, 3. Kodi nchifukwa ninji Yehova sanayankhe mapemphero a Aisrayeli, monga chawonedwera m’mawu a Yesaya, Yeremiya, ndi Mika?

2 Iyi ndi mbali ya pemphero imene imanyalanyazidwa ndi ambiri a awo amene ali m’Dziko la Chipembedzo, monga momwe inanyalanyazidwira ndi Aisrayeli ampatuko m’tsiku la Yesaya. Chimenecho ndicho chifukwa chake Yehova anapangitsa mneneri wake kumuimira iye akumati: “Pochulukitsa mapemphero anu inu sindidzamva . . . sambani dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa; phunzirani kuchita zabwino.” (Yesaya 1:15-17) Inde, ngati Aisrayeli anafuna chiyanjo cha Mulungu, iwo anayenera kuchita m’njira imene imamkondweretsa. Monga mmene chanenedwera bwino: “Ngati mufuna kuti Mulungu akumveni inu pamene mupemphera, muyenera kumumva iye pamene akulankhula.”

3 M’chenicheni, Yehova Mulungu mobwerezabwereza anachipeza icho kukhala choyenera kukumbutsa anthu ake Aisrayeli za chowonadi chimenechi. Chotero timawerenga: “Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake liri lonyansa” kwa Mulungu. “Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.” (Miyambo 28:9; 15:29) Chifukwa cha mkhalidwe umenewu, Yeremiya analira: “Inu [Yehova] mwadzikuta ndi mtambo kuti pemphero lathu lisapyolemo.” (Maliro 3:44) Zowonadi, chenjezo limene Mika anauuziridwa kupereka linakwaniritsidwa: “Adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsya machitidwe awo.”​—Mika 3:4; Miyambo 1:28-32.

4. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti ngakhale pakati pa anthu a Yehova ena samayamikira kufunika kwa ntchito zogwirizana ndi mapemphero awo?

4 Chotero chiri choyenerera kukhala m’chigwirizano ndi mapemphero athu. Kodi chiri chofunika kugogomezera nsonga imeneyo lerolino? Inde icho chiridi, osati kokha chifukwa chamkhalidwe m’Dziko la Chipembedzo komanso chifukwa cha mkhalidwe wina wa anthu odzipereka a Yehova. Pa ofalitsa oposa 3, 000, 000 a mbiri yabwino chaka chatha, chiwerengero choposa 37, 000 chinachotsedwa chifukwa cha mkhalidwe wosayenera Akristu. Icho chimafika ku kuwerengera kwa munthu m’modzi pa anthu 80 alionse. Moyenerera, ambiri a anthu awa anali kupemphera chifupifupi pano ndi apo. Koma kodi iwo anali kuchita mogwirizana ndi mapemphero awo? Kutalitali! Ngakhale akulu ena amene anali mu utumiki wanthawi zonse kwa zaka makumi angapo anali pakati pa awo opatsidwa chilango mu njira imodzi kapena inzake. Chiri chomvetsa chisoni motani nanga! Zowonadi, “Lolani iwo akuyesa kuti ali chiriri adziyang’anire kuti angagwe,” kuti iye sakuchita m’njira imene ingapangitse mapemphero ake kukhala osalandiridwa kwa Mlengi wake.​—1 Akorinto 10:12.

Chifukwa Chimene Mapemphero Amafunikira Ntchito

5. Kuti Yehova ayankhe mapemphero athu, kodi ndimotani mmene tingatsimikizirire kuwona mtima kwathu?

5 Kuti mapemphero athu amvedwe ndi Yehova Mulungu, sitiyenera kokha kukhala oyera mwa makhalidwe ndi mwauzimu koma tiyenera kutsimikizira kufunitsitsa kwa mapemphero athu mwakugwirira ntchito pa zimene tipempherera. Pemphero lokha siliri choloŵa m’malo chakuwonamtima, kuyesetsa kwanzeru. Yehova sangachite kaamba ka ife, chimene tingathe kuchichita ife eni mwakufunitsitsa kugwiritsira ntchito uphungu wa Mawu ake ndi kutsatira chitsogozo cha mzimu wake woreyera. Tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita zo nse zimene tingathe m’njira imeneyi kotero kuti iye akhale ndi maziko akuyankhira mapemphero athu. , Chotero, ife ‘sitiyenera kupempha zoposa zimene. tin ofuna kugwirirapo ntchito,’ monga mmene wina wake achiikira bwino ichi

6. Ndi kaamba ka zifukwa ziWiri ziti zimene tiyenera kupempherera?

6 Komabe, funso lingafunsidwe: ‘Nchifukwa ninji tiyenera kupemphera ngati tikayenera kugwirira ntchito pa zimene tapempherera? Tiyenera kupemphera makamaka kaamba ka zifukwa ziŵiri zabwino. Choyamba, mwa ma pemphero athu timatsimikizira kuti zinthu zonse zabwino zimabwera kuchokera kwa Mulungu. lye ali Mpatsi wa mphatso yonse yabwino ndi yangwiro​—kuwala kwa dzuwa, mvula, nyengo zopatsa zipatso, ndizina zambiri! (Mateyu 5:45; Machitidwe 14:16, 17; Yakobo l:17) Chachiwiri, kaya zoyesayesa zathu ziri ndi chipambano kapena ayi zimadalira pa dalitso la Yehova. Monga momwe timaŵerengerapa Masalmo 127:1: ‘’Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mudzi Yehova, mlonda adikira chabe.” Kupanga nsonga yofananayo ali mawu awa a mtumwi Paulo pa 1 Akorinto 3: 6, 7: “Ndinawoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wowokayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.”

Zitsanzo Zina Zamakedzana

7, 8. (a) Kodi ndi chochitika chotani m’moyo wa . Yakobo chimene chikusonyeza kuti iye anayamikira kuti zintchito ziyenera kutsagana ndi mapemphero? (b) Kodi ndi chitsanzo chotani chimene Mfumu Davide anapereka m’chigwirizano ndi ichi?

7 Malemba amasimba zochitika zambiri kusonyeza kuti atumiki okhulupirika a Yehova anagwirira ntchito pa zimene iwo anapempherera. Tiyeni tilingalire zitsanzo zoimira zochepa Chifukwa chakuti mdzukulu wa Abrahamu Yakobo anapeza dalitso laukulu, mbale wake wamkulu Esau anamuda ndi chidani chachikulu. (Genesis 27:41) Zaka zina 20 pambuyo pake, pamene Yakobo anali kubwerera kuchokera ku Padanaramu kupita ku dziko lake lobadwira ndi banja lalikulu ndi zambiri za zoweta zake, iye anamva kuti Esau anali kubwera kukumana naye. Kukumbukira udani wa Esau, Yakobo anapemphera mofunitsitsa kwa Yehova kaamba ka chitetezero kuchokera ku mkwiyo wa mbale Wake. Koma kodi iye anachilola kuthera pomwepo? Ndithudi, ayi. Iye anatumiza mphatso zaulere patsogolo pake akumapereka chifukwa: “Ndimusangalatse iye ndi mphatso zotumizidwa patsogolo panga.” Ndipo chotero zinakhalira momwemo, popeza pamene abale aŵiriwa anakumana, Esau anafungatira Yakobo ndi kumpsompsona iye.​—Genesis, mitu 32, 33.

8 Davide anapereka chitsanzo china cha kugwirira ntchito pa zomwe timapempherera. Pamene mwana wake Abisalomu analanda mpandowake wachifumu, phungu wa Davide Ahitofeli anachita maere ndi Abisalomu. , Chotero Davide anapembedzera mofunitsitsa ku, ti uphungu wa Ahitofeli usokonezedwe. Kodi Davide anangopemphera kokha kaamba ka chifukwa chimenecho? Ayi, iye analangiza phungu wake womvera. Husai kugwirizana ndi Abisalomu kotero kuti uphungu Wa Ahitofeli usakhazikike. Ndipo mmenemo ndi mmene zinthu zinaChitikira. Abisalomu anachita mogwirizana ndi Uphungu woipa wopatsidwa kwa iye ndi Husai, kukana uphungu Wa Ahitofeli.​—2 Samueli 15:31-37; 17:1-14; 18:6-8.

9. Kodi ndimotani mmene Nehemiva anasonyezera kuti iye anayamikira prinaipulo lakuti mapemphero amafunikira zintchito?

9 Komabe uphungu wina womwe tingautenge kaamba ka chenjezo lathu uli uja wa Nehemiya. Iye anali ndi ntchito yaikulu yoyenera kuti aichite​—kumanganso malinga a Yerusalemu. Komabe, adani ambiri anali kum’chitira chiwembu iye. Nehemiya ponse pawiri anapemphera ndi kugwira ntchito, monga mmene timawerengera: “Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, chifukwa cha iwowa.” Kuyambira pamenepo kupita mtsogolo, theka la amuna achichepere a Nehemiya anaimirira okonzekera kuchinjiriza theka lina, awo amene anali kumanga linga.​—Nehemiya 4:9, 16.

Chitsanzo cha Yesu

10, 11. Kodi ndi zitsanzo ziti zoperekedwa ndi Yesu zimene zimasonyeza kuti iye anachita mogwirizana ndi mapemphero ake?

10 Yesu Kristu anakhazikitsa chitsanzo chabwino cha kugwirira ntchito pa zimene tipempherera. Iye anatiphunzitsa ife kupemphera: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Koma Yesu anachitanso chirichonse chimene akanatha kotero kuti amvetseri ake ayeretse dzina la Atate wake. Mofananamo, Yesu sanadziikire malire iyemwini ku kupemphera kuti: “Atate, yeretsani dzina lanu.” (Yohane 12:28) Ayi, iye anachita zomwe akanatha kuyeretsa dzina la Atate wake ndi kupangitsa ena kuchita chimodzimodzi.​—Luka 5:23-26; 17:12-15; Yohane 17:4.

11 Kuwona kusoweka kwakukulu kwauzimu kumene anthu anali nako, Yesu ananena kwa ophunzira ake: “Zotuta zichulukadi, koma otuta ali ochepa. Chomwecho, funsani mwini kututa [Yehova Mulungu] kutumiza antchito ambiri ku kututa kwake.” (Mateyu 9:37, 38) Kodi Yesu analola zinthu kuthera pomwepo? Kutalitali! Mwamsanga pambuyo pa icho, iye anatumiza atumwi ake 12 awiri awiri paulendo wolalikira, kapena ‘kututa.’ Pambuyo pake, Yesu anatumiza alaliki 70 kukachita ntchito imodzimodziyo.​—Mateyu 10:1-10; Luka 10: 1-9.

Kugwiritsira Ntchito Prinsipulo

12. Kodi ndi chotulukapo chotani chimene ntchito iri nayo pa mapemphero athu akuti Mulungu atipatse ife chakudya chathu cha lero?

12 Mwachiwonekere, Yehova Mulungu amatiyembekezera ife kukhala okhazikika, kuchita mogwirizana ndi mapemphero athu, mwakutero kutsimikizira kuwona mtima kwathu. Yesu anatiuza ife kupemphera: “Tipatseni ife lero chakudya chathu cha lero.” (Mateyu 6: 11) Chotero, moyenerera, otsatira ake onse amapembedzera Mulungu kaamba ka chimenecho. Koma kodi timayembekezera Atate wathu wakumwamba kuyankha pemphero limenelo popanda kuchita kwathu kena kake konena za icho? Ndithudi ayi. Chimenecho ndiye chifukwa chake timawerenga kuti: “Moyo wa waulesi ukhumba”​—mwinamwake ngakhale mwa kupemphera​“koma moyo wake supeza kanthu.” (Miyambo 13:4, NW) Mtumwi Paulo anapanga nsonga yofananayo pa 2 Atesalonika 3:10, akumati: “Ngati munthu safuna kugwira ntchito asadyenso.” Kupemphera kaamba ka chakudya chathu chatsiku ndi tsiku kuyenera kutsagana ndi kufunitsitsa kugwira ntchito. Mosangalatsa Paulo mwanzeru ananena kuti awo amene safuna “kugwira ntchito” sayenera kudya. Ena amene amafuna kugwira ntchito angakhale osalembedwa ntchito, kudwala, kapena kukha la okalamba kwambiri kuti agwire ntchito. Iwo amafuna kugwira ntchito, koma ichi chiri chosatheka mu mikhalidwe yawo. Chotero, iwo moyenerera angapemphere kaamba ka chakudya chawo cha tsiku ndi tsiku ndi kuyembekezera kuchilandira icho.

13. Kuti Yehova ayankhe mapemphero athu kaamba ka mzimu wake woyera, kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita?

13 Yesu anaperekanso uphungu kwa ife wa kufunsa Atate wake wa kumwamba kaamba ka mzimu wake woyera. Monga mmene Yesu anatitsimikizirira ife, Mulungu ali wofunitsitsa kutipatsa ife mzimu woyera kuposa mmene makolo a padziko lapansi amakhalira ofunitsitsa kupereka zinthu zabwino kwa ana awo. (Luka 11:13) Koma kodi tingayembekezere Yehova Mulungu kupereka mzimu wake woyera kwa ife mozizwitsa, mopanda kuyesayesa kumbali yathu? Kutalitali! Tiyenera kuchita chirichonse chimene tingathe kuti tilandire mzimu woyera. Mkuwonjezera pa kupemphera kaamba ka iwo, tiyenera kudya mosamalitsa kuchokera m’Mawu a Mulungu. Nchifukwa ninji? Chifukwa Yehova Mulungu samapereka mzimu wake woyera kuchotsapo kokha Mawu ake ndipo sitingayembekezere kulandira mzimu woyera ngati tikunyalanyaza njira ya padziko lapansi imene Yehova akugwiritsira ntchito lerolino, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” woimiridwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Popanda thandizo lochokera kwa “kapolo” ameneyu, sitingakhale okhoza ku mvetsetsa kufunika kwenikweni kwa zimene timawerenga kapenanso kudziwa mmene tingagwiritsire ntchito zimene timaphunzirazo.​—Mateyu 24:45-47.

14, 15. (a) Kuti Yehova ayankhe mapemphero athu kaamba ka nzeru, kodi ndimotani mmene tiyenera kugwirizanira? (b) Ndimotani mmene ichi chasonyezedwera mu chitsanzo cha Mfumu Solomo?

14 Prinsipulo lakuti pemphero limafunikira ntchito limagwiranso ntchito ku mawu awa a wophunzira Yakobo, mbale wa mimba yina wa Yesu: “Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsaiye.” (Yakobo 1:5; Mateyu 13:55) Koma kodi Mulungu amapereka nzeru imeneyi kwa ife mozizwitsa? Ayi. Choyambirira cha zonse, tiyenera kukhala ndi khalidwe labwino, monga momwe timawerengera: “Adzaphunzitsa ofatsa njira yake.” (Masalmo 25:9) Ndipo kodi ndimotani mmene Mulungu amaphunzitsira “ofatsa”? Kupyolera mu Mawu ake. Kachiwirinso, tiyenera kupanga kuyesayesa kwakumvetsetsa iwo ndi kugwiritsira ntchito iwo, monga kwasonyezedwera pa Miyambo 2:1-6: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutchera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, . . . pompo udzazindikira kuwopa Yehova ndi kumdziwadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru.”

15 Pamene Mfumu Solomo anapempherera kaamba ka nzeru ndipo Mulungu mozizwitsa anayankha pemphero lake, kodi prinsipulo lakuti pemphero limafunikira ntchito linagwiranso ntchito? Inde, linatero, popeza monga mfumu ya Israyeli, Solomo anafunikira kulemba bukhu lake la Lamulo, kuliwerenga ilo tsiku ndi tsiku, ndi kuligwiritsira ntchito ilo m’moyo wake. Koma pamene Solomo anachita mosiyana ndi malangizo ake, monga kuchulukitsa akazi ndi akavalo, ntchito zake sizinali m’chigwirizano ndi mapemphero ake. Monga chotulukapo chake, Solomo anakhala wampatuko ndipo anafa wotero monga “wopanda nzeru.”​—Masalmo 14:1; Deutronomo 17:16-20; 1 Mafumu 10:26; 11:3, 4, 11.

16. Kodi ndi chisonyezero chotani chimene chimasonyeza kuti kuti mapemphero athu alake zofooka zakuthupi ayenera kutsagana ndi zintchito?

16 Prinsipulo lakuti ntchito ziyenera kutsagana ndi mapemphero limagwiranso ntchito pamene tikufunsa thandizo la Mulungu kulaka chizolowezi chadyera, chokhazikika mwa ife. Chotero mlongo wachipainiya anavomereza kukhala womwerekera ku kuwonera programu yosatsa malonda, kuyambira 11:00 a. m. mpaka 3:30 p. m. tsiku lirilonse. Kuphunzira kuchokera ku nkhani ya pa msonkhano wa chigawo kuti ndi movulaza chotani mmene maprogramu oipa amenewo aliri, iye anaitenga nkhaniyo kwa Mulungu m’pemphero. Koma chinatenga nthawi kwa iye kuti alake chizolowezicho. Chifukwa ninji? Chifukwa, monga momwe iye akunenera: ‘Ndinapemphera kulaka chizolowezicho ndipo kenaka ndi kuwonera maprogramuwo. Chotero ndinaganiza za kukhala mu utumiki wa m’munda tsiku lonse kotero kuti ndisakhale ndi chiyeso. Pomalizira ndinafika ku nsonga ya kutseka TV m’mawa ndi kuisiya iyo kukhala yotseka tsiku lonse. Inde, kuwonjezera ku pemphero lakuti alake chofooka chake, iye anayenera kugwirirapo ntchito kuti achilake icho.

Pemphero ndi Umboni Wathu

17-19. (a) Kodi ndi nsonga zotani zimene zimasonyeza kuti Mboni za Yehova zakhala zikugwirira ntchito mogwirizana ndi mapemphero awo? (b) Kodi ndi chitsanzo chaumwini chiti chimene chikupereka nsonga yofananayo?

17 Kulibe kwina kuli konse kumene prinsipulo lakuti pemphero limafunikira ntchito liri lowona mokulira kuposa m’ntchito yolalikira Ufumu. Chotero, Mboni zonse za Yehova sizimapemphera kokha kaamba ka kuwonjezeka kwa otuta komanso zimadzigwiritsira ntchito izo zeni kuntchitoyo. Monga chotulukapo chake, izo zawona chiwonjezeko chowonekera m’dziko limodzi pambuyo pa linzake. Kungosonyeza chitsanzo chimodzi chokha: “Mu 1930 munali Mboni ya Yehova imodzi yokha yolalikira mu Chile. Lerolino, Mboni imodzi imeneyo yakhala osati kokha chikwi koma 30, 000. (Yesaya 60:22) Kodi ichi chinali kokha monga chotulukapo chapemphero? Ayi, ntchito inalowetsedwamo. Nkulekeranji, popeza mu 1986 mokha, Mboni za Yehova mu Chile zinapereka maora oposa 6, 492, 000 ku ntchito yolalikira!

18 Chofananacho chiri chowona pamene ntchito yolalikira yatsekedwa. Mboni sizimapemphera kokha kaamba ka kuwonjezeka komanso zimapita mobisira ndi kupitiriza kulalikira. Mosasamala kanthu za chiletso chalamulo chotero, kuwonjezeka kumachitika m’maiko amenewo. Chotero, m’maiko 33 kumene Mboni za Yehova zimakumana ndi chitsutso chalamulo chimenecho, mkati mwa chaka chautumiki cha 1986 izo zinapereka maora oposa 32,600,000 ku ntchito yawo yolalikira ndipo zinasangalala ndi chiwonjezeko cha 4.6-peresenti!

19 Ndithudi, prinsipulo lakuti mapemphero amafunikira zintchito limagwiranso ntchito kwa aliyense payekha. Tingapemphere kwa Yehova kuti tikhale ndi phunziro la Baibulo la panyumba komanso sitingakhale tikuchita chirichonse chomwe tingathe kuti tipeze limodzi. Chimenecho chinali chokumana nacho champainiya m’modzi. Pokhala anali ndi phunziro la Baibulo limodzi lokha, iye anapemphera kuti akhale nawo ochuluka. Kodi iye analeka zinthu kuthera pomwepo? Ayi, koma mosamalitsa anasamalira ponena za utumiki wake ndipo anapeza kuti pa maulendo obwereza iye sanali kubweretsa nsonga ya kukhala ndi phunziro la Baibulo la panyumba. Akumapitirira m’mzerawo, iye mwamsanga anapeza maphunziro awiri a Baibulo owonjezereka.

20. Kodi ndimotani mmene prinsipulo lakuti mapemphero amafunikira zintchito lingafupikitsidwire?

20 Zitsanzo zina zambiri zingaperekedwe kutsimikizira kuti mapemphero amafunikira zintchito. Mwachitsanzo, pali awo ogwirizana ndi maunansi aumwini mu banja kapena mpingo. Koma zitsanzo zotchulidwazi ziyenera kukhala zokwanira kuchipangitsa icho kukhala chomvekera bwino kuti mapemphero amafunikira zintchito. Ichi chiri chanzeru, popeza sitingayembekezere Yehova Mulungu kupereka lingaliro la chiyanjo ku kupembedzera kwathu ngati timamuchimwira iye ndi khalidwe lathu lenilenilo. Chimatsatiranso kuti tiyenera kuchita chiri chonse chimene tingathe m’chigwirizano ndi mapemphero athu ngati tikuyembekezera Yehova kutichitira ife zimene sitingathe kudzichitira ife eni. Zowonadi, maprinsipulo a Yehova ali anzeru ndi olungama. Iwo amapanga lingaliro, ndipo chiri kaamba ka phindu lathu kuti tichite mogwirizana ndi iwo.

Kodi Mumakumbukira?

◻ Kodi ndi chofunikira chotani chogwirizana ndi pemphero chimene chinanyalanyazidwa ndi ambiri mu Israyeii wakale?

◻ Kodi nchifukwa ninji Mulungu sali wosalingalira m’kufuna kuti tiyenera kugwira ntchito limodzi ndi kupemphera kaamba ka zimene timakhumba?

◻ Kodi ndi zitsanzo zakale ziti zimene zimasonyeza kuti atumiki a Yehova anagwirira ntchito pa zimene anapempherera?

◻ Kuti Mulungu ayankhe mapemphero athu kaamba ka mzimu wake woyera ndi nzeru, kodi nchiyani chimene tiyenera kumachita?

◻ Kodi ndimotani mmene prinsipulo lakuti mapemphero amafunikira zintchito limagwirira ntchito ku utumiki wathu wa m’munda?

[Chithunzi patsamba 17]

Yesu anafulumiza ophunzira ake kupemphera kaamba ka otuta ambiri. Koma iye anawatumizanso iwo ku ntchito yolalikira, kapena”kututa”

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi mumapemphera kaamba ka thandizo kuletsa kuwonera kwanu wailesi ya kanema? Chotero gwiritsirani ntchito prinsipulo lakuti mapemphero amafunikira zintchito mwakutseka TV yanu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena