Wachichepere Alemekeza Yehova
MWAWl wokulira wakuchitira umboni uli wotseguka kwa achichepere pamene iwo ali ndi chikhumbo champhamvu cha kutumikira Yehova. Ichi chinawoneka mu chokumana nacho cha mnyamata wa zaka zisanu wa ku madzulo mu Kenya.—Mlaliki 12:1.
Mayi wake anamufunsa iye: ‘‘Kodi nchiyani chimene ufuna kudzakhala pamene wakula?”Mnyamatayo anali atawonapo mpainiya wapadera mu mpingo ndipo anayankha: “Ndikufuna kudzakhala mpainiya wapadera monga Mbale F——.” Mayi anayankha: “Koma ichi nchosatheka; sungakhale ngakhale mpainiya wokhazikika chifukwa ulibe phunziro la Baibulo.” Mnyamatayo anafunsa kuti: “Kodi nchiyani chimene ndingachite tsopano?“ Mayi wake analingalira kwa iye kuyesa kuphunzitsa osewera nawo anzake kuchokera mu kope lake la Bukhu Langa la Nkhaniza Baibulo.
Mnyamata wa zaka zisanuyo anatenga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndi kupita kuitanira pa mabwenzi ake, kuwaitana iwo kuphunzira Baibulo ndi iye. Chotulukapo chake?
lye anapanga gulu la khumi lomwe akanaphunzira nalo. lye anapanga kugwiritsira ntchito kwabwino kwa zithunzi, anafunsa mafunso achitokoso ambiri, ndi kufunsa mafunso obwereramo pamapeto pa phunziro. Ngati iwo sanakumbukire, iye anabwereramo mu nkhaniyi ndi iwo kachiwirinso. Mayiyo analongosola kuti chinalidi chimwemwe chenicheni kuwona achichepere onsewo atakhala pansi kutsogolo kwa nyumba yake kuphunzira limodzi! Pamenepo panali mwana wake wamwamuna wa zaka zisanu akufunsa mafunso, ndipo kenaka manja onse anapita pamwamba kuti ayankhe.
Chinali chimwemwe chowonjezereka kwa mayiwo, limodzinso ndi mpingo, kuwona asanu ndi atatu a ana amenewa akupezeka pa misonkhano ya mpingo. Ena awiriwo anali a ang’ono kwambiri. Zonsezo zinachitika chifukwa cha wa zaka zisanu yemwe anafuna kulemekeza Yehova ndi kuthandiza ena.