Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 3/1 tsamba 15
  • Wazaka Zisanu Zakubadwa Adzutsa Chikondwerero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wazaka Zisanu Zakubadwa Adzutsa Chikondwerero
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Wachichepere Alemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kudya Opanda Mafoloko ndi Mipeni
    Galamukani!—2003
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kuchitira Umboni Kubala Zipatso Panyumba ndi Kusukulu
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 3/1 tsamba 15

Ripoti la Olengeza Ufumu

Wazaka Zisanu Zakubadwa Adzutsa Chikondwerero

PAKATI pa Mboni za Yehova zoposa 40,000 mu Venezuela pali mnyamata wazaka zisanu zakubadwa yemwe anakhala ndi chokumana nacho chosangalatsa. Iye anamvetsera mosamalitsa ku nkhani za Baibulo zozikidwa pa bukhu lakuti Life​—How Did It Get Here?​—By Evolution or by Creation? ndi kukambitsirana kwa banja kwa pambuyo pake kwa bukhu limeneli. Wazaka zisanu zakubadwayo, yemwe anali wam’banja lateokratiki, anamvetsetsa kuti chisinthiko chimati munthu anakhalako kuchokera ku “nsuzi.” Chimodzi cha zigawo za bukhulo chimafotokoza chiphunzitso chachisinthiko kuti moyo unasinthika kuchokera ku nsuzi wa zinthu za organic [zomera kapena zamoyo zakufa].

Kwa zaka 14, banja la m’nyumba yoyandikana (mwamuna, mkazi, anyamata aŵiri azaka zapakati pa 13 ndi 19, ndi mwana wamkazi wazaka zisanu ndi ziŵiri) sanasonyeze chikondwerero ku mapempho a banja la Mbonilo kuti asanthule Baibulo ndi kuziitano zawo kupita nawo ku Nyumba Yaufumu.

Tsiku lina pamene mkazi wa Mboniyo ankatsuka mbale, anamva kukambitsirana kosangalatsa pakati pa mwana wake wamwamuna ndi mtsikana wachichepere wa pa anansipo, chapafupi ndi mpanda wogaŵa nyumbazo. Mnyamata wachichepereyo adati: “Udziŵa chiyani iwe! Anthu akudziko amati munthu anachokera ku nsuzi!” Mtsikana wachichepereyo anayankha, monga momwe ankachitira nthaŵi zonse nati: “Kodi wachita misala?” Mnyamata wachichepereyo anayankha kuti: “Ayi, sindinachite misala. Anthu akudziko amanena kuti munthu anachokera ku nsuzi; komabe Yehova analenga munthu.” Mnyamatayo anaseka lingalirolo, akumaganiza kuti unali nsuzi weniweni wakudya, umene sankaukonda. Kenaka anapitirizabe kuuza mtsikana wachichepereyo kuti: “Atate anga ayenera kupatsa atate ako bukhu la Creation kotero kuti awone kuti Mulungu analenga munthu.” Komabe, mtsikana wachichepereyo anati iwo anali Akatolika, ndi kuimitsa kukambitsiranako.

Pamene mwamuna wa mlongoyo, yemwe ali mkulu, anabwera kunyumba kuchokera ku ntchito, mlongoyo anamsimbira za kukambitsirana kumene anamvetserako. Ngakhale kuti chochitika cha pakati pa anawo chinawaseketsa, mbaleyo analingalira kuti mwinamwake Yehova anafuna kuti iye achitirenso umboni kwa mwamuna woyandikana nayeyo. Chotero pambuyo pa masiku ochepa, iye anafikira mnansi wake ndi kusimba kukambitsirana kwa ana kuja. Iye anati m’malo mwa mwana wake wamwamuna, anafuna kumpatsa kope la bukhu la Creation. Mboniyo inalangiza mnansiyo kuliŵerenga popanda kunyada, popeza likasonyeza chiyambi cha moyo.

Chomdabwitsa mbaleyo chinali chakuti, patapita masiku angapo okwatirana ameneŵa, amene sanasonyeze chikondwerero ku chowonadi kwa nthaŵi yaitali, anadzipereka okha ku nyumba ya mbaleyo kudzalongosola chisoni chawo kaamba ka mkhalidwe umene anausonyeza kwa zaka zambiri. Iwo anati anazizwa ndi phindu lodabwitsa la bukhu la Creation.

Chotulukapo chinali chakuti phunziro la Baibulo linayambidwa ndi banja limeneli. Iwo anayamba kupezeka ku misonkhano mokhazikika ndipo mwamsanga anakhala ofalitsa a mbiri yabwino. Mwamunayo, mkazi wake, ndi ana aamuna aŵiri azaka zapakati pa 13 ndi 19 anabatizidwa pa msonkhano wachigawo, ndipo mtsikanayonso ngwofalitsa wa Ufumu. Mkaziyo anayamba utumiki wa upainiya wothandizira mwamsanga pambuyo pa ubatizo wake.

Yesu Kristu amadziŵa awo amene mitima yawo iri yabwino, ndipo iye angakhoze ndipo amagwiritsiradi ntchito achichepere kuifikira mitima yabwino yoteroyo.​—Yohane 10:14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena