Kodi Chipembedzo Chamakono Chiri Chogwira Ntchito Motani?
“NDINATAYA Baibulo m’chipinda chapadera pa ulendo wanga wopita ku chipinda changa chogona. Ndinaganiza kuti sindidzalinyamulanso ilo kapena kupezekanso pa tchalitchi china. Ndinakhala ndikufufuzafufuza kwa chifupifupi zaka zisanu ndi chimodzi. Komabe sindinapeze thandizo.”
Ronald, woyendetsa kompyuta wa zaka 26, anali atapyola m’mavuto a akulu ndipo anawopa kuti moyo wake ungasweke pakati. Chipembedzo chinawonekera kukhala chosagwira ntchito m’njira yopindulitsa kwa iye. “Ndathana nacho,” iye anatero.
Anthu ambiri, monga Ronald, ali okhumudwitsidwa ndi chipembedzo. Bwanji ponena za inu? Kodi mumaganiza kuti chipembedzo chapereka kwa anthu thandizo lokhoza kugwirirapo ntchito ndi chitsogozo ku kukhala ogwira nawo ntchito abwino, anansi, amuna, akazi, makolo, kapena ana? Kodi chipembedzo chiri ndi mphamvu ya mtendere ndi kugwirizana pakati pa anthu? Kodi icho chawathandiza iwo kumvetsetsa cholinga cha moyo? Kodi icho chakhazikitsa m’maganizo mwawo ndi m’mitima yawo chiyembekezo chotsimikizirika kaamba ka mtsogolo?
Chitsogozo Chogwira Ntchito Chikusoweka
M’dziko iri locholowanacholowana, anthu amafuna nzeru, chitsogozo chomvekera bwino. Kodi iwo angayembekezere icho kuchokera kwa atsogoleri auzimu? M’kalata kwa olemba nkhani mu danga la magazini, mkazi anadandaula kuti:
“Zonse zimene timamva tsopano m’tchalitchi chathu . . . kwakanthaŵi tsopano chiri chikondi, chikondi, chikondi. . . . Sindidziŵa chimene chinachitika ku ‘Musachite chakuti’—‘Musaphe. Musabe,’ ndi zina zonse? Timafunikira kukumbutsidwa kaŵirikaŵiri kuti zinthu zina ziri zoletsedwa. . . . Koma sitimva nkomwe liwu lakuti ‘Chimo’ ndi pang’ono pomwe. Chiri monga ngati kuti iwo amalikana ngati kuti liri liwu lakuda la zilembo zinayi.”
Mwachiwonekere, ena amadzimva kuti aphungu a chipembedzo chawo akhala osasatitsa kwambiri, olekelera koposa. Atsogoleri auzimu oterowo ali ofooka. Iwo ali monga dokotala amene amalemba matenda abodza pa vuto la wodwala ndi kulemba mankhwala osungunulidwa. Ndi ziti zomwe ziri zifukwa zina za kulephera koteroko?
Chiitano cha Chipembedzo chiri M’mavuto
Munthu amene ali wolemetsedwa ndi mavuto ake aumwini sangakhale wokhoza kuwononga nthaŵi yambiri ndi zoyesayesa kuthandiza ena. Maripoti a panyumba zowulutsira mawu akusonyeza kuti chiŵerengero chowonjezereka cha atsogoleri achipembedzo ali okutidwa mozama ndi mavuto awo a chiitano cha chipembedzo ndi aumwini. Pano pali zitsanzo zina:
“Pamene kupsyinjika ndi kuwawidwa ziri zofala m’ntchito zambiri lerolino, palibe kwina kulikonse kumene ziri zoipirapo koposa pakati pa atsogoleri achipembedzo a Chiyuda,” anatero katswiri wa za maganizo pa chipatala chaching’ono Dr. Leslie R. Freedman pambuyo pa kuphunzira kwa zaka zinayi pa yuniversiti ya atsogoleri a chipembedzo a Chiyuda.
“Ngati ndinali ndi mwana wamwamuna, kodi ndikanamufuna iye kukhala wansembe? Mwachisoni, yankho langa liyenera kukhala ayi,” akudandaula wansembe, William Wells, mu ripoti la pa mavuto a atsogoleri a chipembedzo. Nchifukwa ninji? Iye akunena kuti sangalimbikitse mwamuna wachichepere kulingalira chiitano cha chipembedzo chodzazidwa ndi “kutsutsana, chiwawa, ndi kusatsimikizirika monga mmene unsembe wa Roma Katolika uliri lerolino.”
Ansembe m’tchalitchi cha Lutheran chochirikizidwa ndi boma cha mu Sweden alinso m’mavuto. Nyuzipepala ya tsiku ndi tsiku ya mu Sweden inanena kuti: “Ansembe ali ndi mavuto a malingaliro, omwe m’mikhalidwe yoipa kwambiri amatsogolera ku kudzipha. . . . Chiitano cha chipembedzo cha utsogoleri wa chipembedzo chiri m’vuto.”
Kusagwirizana Kosokoneza
M’maiko amenewo kumene atsogoleri a chipembedzo ali odzilowetsa m’nkhondo zotopetsa ndi zosankha, iwo ali opatutsidwa kuchokera ku kupereka chiyang’aniro chosamalitsa ku zosowa zauzimu za anthu. Iwonso ayenera kugawanamo mu thayo la kutaika kwamphamvu ya anthu ndi ndalama zomwe zikanagwiritsiridwa ntchito kaamba ka ubwino wa kuthupi wa anthu.
Pali awo m’mbali zonse za dziko lapansi omwe ataya chidaliro chawo m’chipembedzo ndipo akhala mwachipembedzo osiyanako. Kutaika m’ziwalo ndi kutsika kwa anthu opita ku tchalitchi kukusimbidwa kuchokera ku malo oterowo monga ngati Sweden, Finland, Germany, Britain, Italy, Canada, ndi United States.
Kodi muli pakati pa awo, onga Ronald, amene amaganiza kuti athana nacho chipembedzo? Ndipo komabe, kodi pangakhale chipembedzo chomwe chatsimikizira kukhala chogwira ntchito mwa mtengo wapatali kwa ambiri? Nkhani yotsatirayi idzalongosola chimenechi.