Kodi Mungapeze Chipembedzo Chabwino?
RONALD—wotchulidwa m’nkhani yapitayo—analingalira kuti ayenera kusiiratu kufunafuna kwake kaamba ka chipembedzo chomwe chingamupatse iye thandizo logwira ntchito ndi chitsogozo. Koma iye analingalira kudzipatsa iyemwini mwaŵi womalizira. “Ngati ndithudi panali Mulungu, ndinafuna kuti iye adziŵe kuti ndiri mowona mtima kumfunafuna iye,” iye anatero. Chotero usiku umodzi Ronald anapemphera kuti: “Ngati inudi muli Mulungu wachikondi, mundipeze ine popeza kuti kwa zaka zambiri ndakhala ndikukufunafunani ndipo sindinapeze chirichonse.”
Masiku ochepa pambuyo pake ku ntchito kwake, Ronald anagawiridwa kugwira ntchito pa gawo lake ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye anayamba kufunsa mafunso ponena za Baibulo. Mayankhowo anatokosa kufunitsitsa kwake. Mwamsanga anayamba phunziro la Baibulo lokhazikika. Iye anapitanso ku misonkhano ya mpingo wa kumaloko wa Mboni za Yehova.
Miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pake Ronald anali wokhutiritsidwa kuti anapeza chipembedzo chimene chinamupatsa iye chisonkhezero cha kukonzanso moyo wake m’njira yokhoza kugwira ntchito koposa. Pambuyo pa zaka zitatu akugwirizana ndi Mboni za Yehova, iye analongosola m’kalata yake ku magazini ya Nsanja ya Olonda mapindu ena amene anapeza kuchokera mkusonkhana kumeneku.
“Chibadwa Chakupha” Chachotsedwa
Ronald akulemba kuti: “Phindu loyamba la kuphunzira chowonadi [kuphunzitsa kwa Baibulo] linali kukhala wokhoza kulamulira mkwiyo wanga. Kwanthaŵi yaitali ndinali wogwirizanitsidwa m’machitachita a kudzitetezera. . . . Ndinali kuphunzira kwa maora asanu ndi limodzi kufika ku asanu ndi atatu pa tsiku, ndipo nthaŵi zonse chinakhazikika m’maganizo anga kukulitsa chibadwa chakupha.”
Kumenya ndi kupha siziri njira zokhutiritsa zakuthetsera kusemphana kwa munthu mmodzi ndi m’nzake. Chotero, chipembedzo chothandiza chiri mphamvu ya mtendere. Baibulo limanena pa Aroma 12:18: “Khalani pa mtendere ndi anthu onse.” Mboni za Yehova sizimaphunzitsa matupi awo kaamba ka kumenyana, ndiponso sizimafunafuna kudzichinjiriza izo zokha mwa kuphunzira mmene angagwirire mfuti. Iwo amadziŵika kuzungulira padziko lonse ponena za kaimidwe kawo ka mtendere, ka uchete mkati mwa nthaŵi za nkhondo.
Kuwona mphamvu yokhoza kugwirirapo ntchito kapena kuthekera kwa chipembedzo chotero, virigo wa Roma Katolika analemba m’magazini ya tchalitchi ya Chiitaliyano: “Dziko likanakhala losiyana chotani nanga ngati tonse tikanadzuka m’mawa umodzi molimba mtima kulingalira kuti sitikatenganso zida, . . . monga ngati Mboni za Yehova!”
Kawonedwe ka mtendere kameneka pakati pa Mboni kagawirako ku kupanga ubale wadziko lonse wa anthu oposa mamiliyoni atatu m’maiko 208. Iwo amachita ndi wina ndi mnzake monga mabwenzi owona, mosasamala kanthu za mtundu wawo, fuko, kapena malo amayanjano. Ichi chiri chogwira ntchito kwambiri m’dziko la ukali, makamaka pamene thandizo lifunika. Eva, mkazi wachichepere wa chiSwedish amene ali mmodzi wa Mboni za Yehova, anakumana ndi ichi.
Pamene anali kuchezera ku Greece, Eva anagwidwa ndi meningitis. Atakomoka, ndi ululu wa m’mwazi ndi kukha mwazi kwa mkatikati, iye anatengedwera ku chipatala mwamsanga mu Athens, kumene sanadziŵe aliyense. Atate wake ku Sweden anadziŵitsidwa pa lamya. Iye anaitana mkulu mu mpingo wa Mboni za Yehova wa kumaloko. Mkulu ameneyo anaitana Mboni zimene anali kudziŵa mu Athens. Eva mofulumira anafikiridwa ndi akhulupiriri anzake a chiGreek amene anali asanakumane nawo ndi kalelonse.
Ichi chimaitanira m’maganizo chitsanzo chimene mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito, kusonyeza mmene umodzi ndi kudera nkhaŵa zimayendera limodzi. Iye anati pa 1 Akorinto 12:25, 26: “Kusakhale chisiyano m’thupi . . . koma kuti ziwalo zisamalane china ndi chinzake. Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi.”
Chimenechi ndi chimene Eva anakumana nacho mu Greece. Kwa chifupifupi milungu itatu mabwenzi ake atsopano sanamusiye iye wopanda chisamaliro. Iye anachira ndi kubwerera kumudzi kwake. Iye akunena kuti: “Ndithudi ndinakumana ndi mapindu a ubale wachikondi.”
Osakhumba “Dola Yowonjezereka Imeneyo”
Tiyeni tibwerere m’mbuyo ku kalata ya Ronald. Pambuyo pa kunena mmene chikhulupiriro chake chatsopano chinamthandizira iye kulamulira mkwiyo wake, kuchotsa “chibadwa chakupha” chimenecho, ndi kukhala wa mtendere koposa, iye akunena kuti chiphunzitso cha Baibulo chinamupatsa iye kayang’anidwe kolinganizidwa ka ntchito ndi ndalama. “Ndinali woyendetsa kompyuta wa wondilemba ntchito wanga woyambirira,” akutero Ronald, “ndipo ndinali kuphonya kukhala ndi banja langa ndi mabwenzi kokha kuti ndigwire ntchito yowonjezereka. Ndinali kugwira ntchito usiku kwa zaka zoposa zisanu ndi ziŵiri. Nthaŵi zonse ndinafuna dola yowonjezereka imeneyo.”
Chikhumbo choterocho kaamba ka “dola yowonjezereka imeneyo”, mkupita kwanthaŵi, chingakhale chovulaza, chovulaza mwakupha. “Kwa ena, ndalama zimatanthauza chisungiko. Kwa ena zimatanthauza mphamvu. Kwa ena zimatanthauza kuti akakhala okhoza kugula chikondi, ndipo kwa gulu lachinayi zimatanthauza mpikisano ndi kupambana maseŵera”, akutero katswiri wa odwala maganizo Jay Rohrlich, amene makasitomala ake mokulira ali oyang’anira a ntchito ya ndalama ochokera ku boma la New York Wall Street.
Kuchitira ndemanga pa lingaliro limeneli, ripoti m’magazini ya Science Digest ikunena kuti: “Chikhulupiriro cha kunena kuti ndalama zingatulutse zinthu izi . . . kaŵirikaŵiri chimatsogolera ku kusakhoza kubala, kusowa tulo, matenda a mtima ndiponso mavuto ndi mkazi kapena ana.” Chenjezo la Baibulo liri lakuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma.” Ronald anaphunzira chimenecho ndi kugwiritsira ntchito icho. Iye anapeza icho kukhala chopindulitsa koposa.—Ahebri 13:5.
Kawonedwe Koyenera ka Ntchito
Chikhumbo cha ndalama kaŵirikaŵiri chimasonkhezera anthu kudzikakamiza iwo eni pamwamba pa makwerero a ntchito. Ichi chingapangitse anthu a moyo wabwino koposa kukhala opsyinjika mopambanitsa ndipo kukhala ndi malingaliro owombana—ngakhale ku nsonga ya kudzipha. “Mwamuna mmodzi, amene anafika ku ntchito m’mawa mwina ndi kupeza kuti desiki yake inachotsedwa, anakwera pamwamba pa nyumbayo ndi kudzigwetsera pansi.” Dr. Douglas LaBier ananena chimenecho mu U.S.News & World Report m’kufunsa kochita ndi kugwirizana pakati pa ntchito ndi mavuto a za malingaliro.
“Chimene chikufunika,” akutero Dr. LaBier, “uli moyo wokulitsidwa bwino, umene suli wozikidwa pa ntchito. M’kuwonjezera ku zinthu zonga ngati chakudya chokwanira, kupuma ndi masewera, anthu amene amafuna miyoyo yolinganizika bwino amafunikira kulingalira ponena za kuchita zowonjezereka ndi mabanja awo ndi kukulitsa maluso osakhala a ntchito omwe amawapatsa iwo chisangalalo.”
Mboni za Yehova zaphunzira kuchokera m’Baibulo kukhala zolinganizika ponena za ntchito ndi ndalama. Mlaliki 4:4, 6 amalankhula ponena za kugwira ntchito molimbika komwe kumaphatikizamo “anansi ake kuchitira munthu nsanje” ndipo amanena kuti: “Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja aŵiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.” Ronald anapeza ichi kukhala nzeru yogwira ntchito. Iye anadulako ntchito yake ya kuthupi kotheratu kuti akhale ndi nthaŵi yowonjezereka kaamba zikondwerero zake zauzimu ndi kaamba ka banja lake ndi mabwenzi.
Moyo Wabanja Wachimwemwe Choposa
Ronald kenaka akunena m’kalata yake kuti uphungu wa Baibulo pa ukwati ndi moyo wabanja wamthandiza iye kuchita mwanzerupo ndi mikhalidwe ya banja. Ichi chiri chofunika koposa tsopano pamene moyo wa banja umawoneka kukhala wolekereredwa m’mikhalidwe yambiri. Maiko otukuka amasimba maukwati ochepa, kutha kwa maukwati kokulira, ndi kutsika kwa liŵiro la kubala.
Chikhoterero chimenechi chiri chochititsa mantha chifukwa m’banja ndi mmene zina za zofunika zoyambirira za munthu zimakhutiritsidwa. M’kufufuza, Sydney Morning Herald ya ku Australia inafunsa anthu 2,000 amene zotsatirazi zinawapatsa iwo chikhutiritso chachikulu: ntchito, banja, mabwenzi, machitachita a panthaŵi yapadera, chuma, kapena chipembedzo. Chiŵerengero chachikulu koposa chinapatsa “banja” malo oyambirira.
Mboni za Yehova ziri zosangalatsidwa m’kusunga mabanja awo kukhala amphamvu. Mwachitsanzo, mkati mwa zaka zisanu zokha zapita, magazini awo aŵiri Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! (kugawira kosakaniza kwa makope mamiliyoni 22 m’zinenero zoposa 100) anali ndi nkhani zina zokhoza kugwirirapo ntchito 60 ponena za kusamalira mikhalidwe yosiyanasiyana ya moyo wa m’banja. Mosakaikira, chipembedzo chozikidwa pa Baibulo chomwe chimathandiza anthu kusamalira mabanja awo m’njira yanzeru ndi yachikondi chiri chogwira ntchito.
“Nchifukwa Ninji?” Wamkulu Ayankhidwa
Ronald akumaliza kalata yake mwa kunena kuti: “Pali chinthu chimodzi chimene kaŵirikaŵiri chimabwera m’maganizo pamene ndiŵerenga nyuzipepala, kuwona nyuzi, kukambitsirana ndi ogwira nawo ntchito, kapena kuuza ena ponena za chikhulupiriro changa. Chiri chakuti kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova kunapereka yankho ku limodzi la mafunso ofunsidwa mofala kwambiri m’dziko—‘Nchifukwa Ninji?’ Nchifukwa ninji upandu wonsewu, chiwawa, nkhondo, mkhalidwe woipa, matenda, phokoso, pambali pa mavuto onse a tsiku ndi tsiku? Kudziŵa kuti dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu ndi mavuto ake liri kokha lakanthaŵi kwachotsa cholemetsa chachikulu pa mapewa anga.”
Baibulo limavumbulutsa chimene chiri kumbuyo kwa mikhalidwe ya dziko yochititsa kakasi lerolino. Ilo limalongosola nchifukwa ninji chifuno choyambirira cha Mlengi cha kupanga dziko iri lapansi kukhala nyumba ya paradaiso kaamba ka mtundu wa anthu sichinakwaniritsidwebe. Ilo limalongosola mmene Mulungu adzachotsera zisonkhezero zonse zosokoneza kuchokera padziko lapansi ndi kukhazikitsa paradaiso wokhazikika kaamba ka anthu kusangalala kosatha.—2 Petro 3:9-13.
Kuti chipembedzo chikhale chogwira ntchito mopindulitsa, chiyenera kubala zipatso zabwino. Chiyenera kutulutsa anthu abwinopo. Chiyenera kukhala chokhoza kulongosola nchifukwa ninji zinthu ziri monga mmene ziriri padziko lapansi lerolino. Ndipo chiyenera kukhazikitsa m’malingaliro ndi m’mitima ya anthu chiyembekezo chotsimikizika kaamba ka mtsogolo. Ronald anafunafuna kaamba ka chipembedzo choterocho, ndipo anachipeza. Mwaŵi wofananawo udakali wotseguka kaamba ka inu.—Mateyu 7:17-20.
[Chithunzi patsamba 5]
Akristu owona amachita ndi wina ndi mnzake monga mabwenzi owona