Kuwopa Mulungu Kodi Kungakupindulitseni?
“Opani Mulungu wowona, ndi kusunga malamulo ake. Pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—MLALIKI 12:13, NW.
1, 2. (a) Ndi pa chiyani pamene kulambira kwathu Mulungu kuyenera kuzikidwa? (b) Nchiyani chinanso, ngakhale kuli tero, chimene Mulungu amafuna? (Deuteronomo 10:12)
KODI mawu akuti “kuwopa Mulungu” amamveka achilendo kwa inu? Ambiri angadzimve kuti ngati iwo amakondadi Mulungu, iwo sayeneranso kumuwopa iye. Kodi ndithudi tiyenera kuchita zonse ziŵiri? Ngati ndi tero, ndimotani mmene kuwopa Mulungu kumatipindulitsira ife?
2 Malemba amasonyeza kuti kulambira kwathu ndi utumiki kwa Mulungu ziyenera kuzikidwa pa chikondi. Yesu anachimveketsa bwino ichi pamene anatiuza ife kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo, maganizo, ndi mphamvu. (Marko 12:30) Koma kufunika kwa kuwopa Mulungu kukugogomezeredwanso m’Mawu ake. Mwachindunji kwambiri, tikuuzidwa pa Mlaliki 12:13, NW: “Opani Mulungu wowona ndi kusunga malamulo ake. Pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” Kodi Yehova ali wosalinganizika m’kutifunsa ife kumuwopa ndi kumkonda iye panthaŵi imodzimodziyo?
3. Ponena za kuwopa, nchiyani chimene chiyenera kusungidwa m’maganizo?
3 Osati kwenikweni—ngati ife tisunga m’maganizo kuti pali mitundu yosiyanasiyana ya kuwopa. Pamene anthu alingalira za kuwopa, iwo kaŵirikaŵiri amakhala ndi kudzimva kwa mantha m’malingaliro omwe amawononga chiyembekezo ndi kutipangitsa ife kudzimva okhumudwitsidwa. Mwachiwonekere, Yehova sangatifune ife kudzimva m’njira yoteroyo ponena za iye! Atate wathu wa kumwamba amatifuna ife kubwera kwa iye monga mmene mwana angapitire kwa atate wake, wokhala ndi chidaliro chachikondi cha atate wake ndipo komabe pa nthaŵi imodzimodziyo akumawopa kusawakondweretsa iwo. Mantha oterowo adzatithandiza ife kukhalabe omvera kwa Atate wathu wa kumwamba pamene tiyesedwa kuchita cholakwa. Awa ndi “mantha aumulungu” oyenera amene Akristu ayenera kukhala nawo.—Ahebri 5:7; 11:7.
4. Ndi mtundu wotani wa mantha umene chikondi chidzathetsa?
4 Yehova sali monga woweruza wopanda malingaliro yemwe amangolanga atumiki ake nthaŵi iriyonse pamene alakwa. M’malomwake, iye amawakonda iwo ndi kuwafuna iwo kuti apambane. Chotero ngati tipanga chophophonya kapena kuchita chimo, kuwopa Yehova sikuyenera kutiletsa ife kulankhula kwa iye ponena za icho. (1 Yohane 1:9; 2:1) Kuwopa kwathu Yehova kwa ulemu sikuli kuwopa kwa kutsutsidwa kapena kukanidwa. Monga mmene tikuŵerengera pa 1 Yohane 4:18: “Mulibe mantha m’chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango.” “Chikondi changwiro,” ngakhale kuli tero, sichidzachotsa ulemu wokulira ndi mantha oyenerera amene tiyenera kukhala nawo kaamba ka Yehova monga Mlengi wathu ndi Mpatsi wa Moyo.—Masalmo 25:14.
Lingalirani Mapindu
5. (a) Ndimotani kokha mmene nzeru ingapezedwere? (b) Nchiyani chimene chinafulumiza munthu yemwe kale anali womwerekera ku anamgoneka kusintha njira yake yopanda nzeru m’moyo?
5 Tiyeni tilingalire ena a mapindu omwe amabwera kuchokera ku “kuwopa Yehova”. Mwachitsanzo, kumatsogolera ku kupeza kwathu nzeru yowona. Anthu ayesera m’njira zambiri, sanasunge kuyesetsa kulikonse, kuti apeze nzeru yotero, koma iwo alephera chifukwa chakuti amanyalanyaza prinsipulo loyambirira: “Kuwopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.” (Masalmo 111:10; Miyambo 9:10) Lingalirani mmene kuwopa koteroko kunathandizira munthu yemwe poyamba anali womwerekera ku anamgoneka kuchita mwanzeru. Iye akulongosola kuti: “Pamene ndinatenga chidziŵitso cha Mulungu, ndinakulitsanso kuwopa kumkhumudwitsa kapena kusamsangalatsa iye. Ndinadziŵa kuti iye anali kundiwona, ndipo ndinali ndi chikhumbo chakukhala wovomerezedwa pamaso pake. Chinandisonkhezera ine kuwononga anamgoneka omwe ndinali nawo mwakuwagwejemulira m’chimbudzi.” Mwamuna ameneyu anagonjetsa machitachita ake oipa, kupereka moyo wake kwa Yehova, ndipo tsopano ali mtumiki mu Johannesburg, South Africa.
6. Ndimotani mmene “kuwopa Yehova” kudzatichinjirizira ife motsutsana ndi zinthu zoipa, ndipo ndi kuti kumene iko kudzatitsogolera?
6 Kodi mungakonde kupewa chimene chiri choipa? “Kuwopa Yehova ndiko kuda zoipa.” (Miyambo 8:13) Inde, kuwopa koyenerera kumeneku kungakuletseni kuchita zizoloŵezi zoipa zambiri zimene Mulungu amatsutsa, monga ngati kusuta fodya, kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka, kuledzera, ndi mkhalidwe woipa wa chisembwere. Pambali pa kusangalatsa Yehova, mukudzichinjiriza kuchokera ku zinthu zambiri zoipa zomwe zimachitika kwa anthu, kuphatikizapo matenda ochititsa mantha ku amene amadzivumbulutsira iwo eni. (Aroma 1:26, 27; 12:1, 2; 1 Akorinto 6:9, 10; 1 Atesalonika 4:3-8) Kuwopa Mulungu sikudzangokuthandizani kokha kudzichinjiriza motsutsana ndi chimene chiri choipa ndi zosayeruzika komanso kudzakutsogozani ku chimene chiri choyera ndi changwiro, popeza tikuuzidwa kuti “kuwopa Yehova kuli mbe.”—Masalmo 19:9.
7, 8. (a) Ndimotani mmene mtsikana wachichepere mmodzi anapezera kuti “kuwopa Yehova” kumatsogolera ku chimwemwe? (b) Tchulani mapindu owonjezereka omwe amabwera kwa awo amene amawopa Yehova.
7 Chimwemwe chiri chonulirapo china chofunidwa ndi anthu ambiri. Ndimotani mmene mungapezere icho? Mawu a Mulungu akuti: “Wodala munthu wakuwopa Yehova.” (Masalmo 112:1; 128:1) Chokumana nacho cha mtsikana wa zaka za uchichepere chikutsimikizira ichi. Iye anadzilowetsa m’mitundu yonse ya mikhalidwe yosavomerezeka ya kugonana, limodzinso ndi kukhulupirira mizimu ndi kuba. Iye kenaka anayamba kuphunzira Baibulo ndi kuwona chifuno cha kumvetsera kwa Yehova ndi kumuwopa. Iye akunena kuti: “Kudziŵa Yehova chiri chinthu chabwino koposa chomwe chachitika kwa ine. Yehova wandithandiza kwambiri m’kupeza chowonadi ndi chimwemwe. Ndikudzimva kuti ndiri wa mangawa mokulira kwa iye chifukwa iye watsegula maso anga ndi kundipatsa mwaŵi ndithudi wa kulingalira ndi kumpeza iye. Tsopano ndikufuna kuthandiza anthu ena kupeza chimwemwe chimenechi.”
8 Yehova amalonjezanso kuti iye adzafupa ‘awo owopa dzina lake.’ (Chivumbulutso 11:18) Kuwonjezerapo, “kuwopa Yehova kupatsa moyo; wokhala nako adzakhala wokhuta; zoipa sizidzamgwera.” (Miyambo 19:23) Ndithudi, kuli “kuwopa Yehova” kumene kudzabweretsa kwa ife ziri zonse zimene tidzazifuna. Kutagwirizana ndi kudzichepetsa, chotulukapo chiri “chuma ndi ulemu ndi moyo.”—Miyambo 22:4; 10:27.
9. Nchifukwa ninji “kuwopa Yehova” kumatsogolera ku njira yokha ya moyo imene imasonyeza nzeru? (Yobu 28:28; Mika 6:9)
9 Kodi ichi sichimatipatsa ife chilimbikitso chirichonse cha kuwopa Mulungu wowona ameneyo? Ndithudi, “kuwopa Yehova” kuli kosangalatsa koposa. Kumatsogolera ku zinthu zonse zimene zidzatibweretsera ife chikhutiritso chenicheni—chokumana nacho chosawonekawoneka lerolino. Ali olimbikitsa chotani nanga mawu ouziridwa awa: “Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziŵitsadi kuti omwe awopa Mulungu nawopa pamaso pake adzapeza bwino, koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa sawona pamaso pa Mulungu”! (Mlaliki 8:12, 13) Ndi munthu uti amene sakhumba zinthu “kukhala bwino” kwa iye? Chokumana nacho cha chimwemwe chimenechi chidzasangalalidwa kokha ndi awo amene amawopa Mulungu.—Masalmo 145:19.
10. Nziti zimene ziri zifukwa zina zofunika koposa zomwe ziyenera kutisonkhezera ife kuwopa Mulungu?
10 Kodi ichi sichiyenera kutipanga ife kutsimikiza mtima kukhala ndi mantha enieni kwa Atate wathu wa kumwamba Yehova, inde, kumuwopa iye? Ndithudi, tiyenera kukhala ndi mantha owona mtima a kusamsangalatsa iye. Ife mozama timayamikira kukoma mtima konse ndi ubwino umene iye wasonyeza kwa ife. Chirichonse chimene tiri nacho chimachokera kwa iye. (Chivumbulutso 4:11) Ndiponso, iye ali Woweruza Wamkulu, Wamphamvuyonse, wokhala ndi mphamvu yakupha awo amene samvera iye. “Gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira,” akufulumiza tero mtumwi Paulo.—Afilipi 2:12; Hoseya 3:5; Luka 12:4, 5.
11. (a) Ndi mkhalidwe wotani umene uyenera kupewedwa ndi Akristu m’masiku ano otsiriza? (b) Ndi mzimu wotani umene uyenera kukulitsidwa?
11 Palibe chisonyezero pano chonena kuti tingapeze chipulumutso mwa kutsanzira mkhalidwe wopanda umoyo, kumachita zochepera monga mmene kungathekere ndi kuyembekezera kuti mwanjira inayake zinthu zidzatembenukira kukhala bwino. Uwu simkhalidwe umene uyenera kusonyezedwa ndi Akristu amene masiku ano otsiriza akukalamira kusunga unansi ndi Mmodzi amene angawone bwino mkati mwa mitima yawo ndi amene amadziŵa malingaliro awo a mkatikati ndi zolinga. (Yeremiya 17:10) Kokha awo amene ali ndi kuzindikira koyenera kwa Yehova adzazindikiridwa ndi iye. Iye akunena kuti: “Koma ndidzayang’anira munthu uyu amene ali waumphaŵi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mawu anga.”—Yesaya 66:2.
Tiyenera Kuphunzira Kuwopa Yehova
12. (a) Ndi mwanjira yotani mmene mtundu wa Israyeli unayanjidwira kuposa mitundu ina yonse? (b) Nchiyani chimene Yehova anayembekezera m’kubwezera?
12 Kulingalira zochita za Yehova ndi Israyeli kungasindikize mowonjezereka m’maganizo athu kufunika kwa kumuwopa iye. Palibe mtundu wina uliwonse umene unakumana ndi chisamaliro choterocho ndi chilabadiro kuchokera kwa Wolamulira wa chilengedwe. (Deuteronomo 4:7, 8, 32-36; 1 Samueli 12:24) Ndi maso awo Aisrayeli anawona chimene Yehova anachita kwa Aigupto, amene, popanda kumuwopa iye, anaika ukapolo ndi kutsendereza anthu ake. Nchiyani chimene anayembekezera mkubwezera? “Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana ang’ono, ndi mlendo wokhala m’midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuwopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mawu onse a chilamulo ichi, ndi kuti ana awo osadziŵa amve, naphunzire kuwopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordano kulilandira likhale lanu lanu.”—Deuteronomo 31:12, 13; 14:23.
13. Nchiyani chimene chiyenera kukhala chodera nkhaŵa choyamba cha makolo ponena za ana awo?
13 Mofanana ndi Aisrayeli, atumiki amakono a Mulungu “ayenera kuphunzira kuwopa Yehova.” Ndi thayo lotani nanga limene ichi chimaika pa tonsefe—makamaka makolo! Makolo, dzifunseni inu eni: ‘Ndimotani mmene ndingathandizire ana anga kupeza mtima wowopa Yehova?’ Tsiku lina pamene iwo adzakula ndi kuchoka panyumba, nchiyani chimene chidzapereka chitetezero chabwino kwa ana anu, mwauzimu, mwamaganizo, kapena mwa kuthupi, kuposa chimenecho? Yehova iyemwini amagogomezera kufunika kwa ichi pamene amachonderera kuti: “Ha! mwenzi akadakhala nawo mtima wotere wakundiwopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana awo nthaŵi zonse!”—Deuteronomo 5:29; 4:10.
14. Tchulani nsonga imodzi imene makolo ayenera kusunga m’maganizo pa kuphunzitsa ana awo kukhala owopa Yehova, ndipo longosolani mmene iyi ingagwiritsidwire ntchito.
14 Mkristu aliyense amene akusamalira banja adzavomereza mwamsanga kuti ichi sichiri thayo lopepuka. Mosasamala kanthu za chimenecho, Mawu ouziridwa a Mulungu amabweretsa nsonga zambiri zofunika ku chisamaliro cha makolo. Imodzi iri yakuti iye ayenera kuyamba pamene ana ali ang’ono. Wamng’ono motani? Pamene Aisrayeli anakumana kuti alandire malangizo kuchokera kwa Yehova, “a ang’ono” anaphatikizidwapo. (Deuteronomo 29:10-13; 31:12, 13) Mwachiwonekere, akazi a Chiisrayeli anabwera ndi makanda awo pa zochitika zoterozo, popeza onse anafunikira kupezekapo. “Kuyambira ku ubwana,” ana awo a amuna ndi akazi anaphunzira kufunika kwa kukhala chete ndi kumvetsera pa misonkhano yoteroyo. (2 Timoteo 3:15) Chotero bweretsani “achichepere anu” limodzi nanu ku misonkhano. Ndiponso, aloŵetseni iwo mu utumiki wa m’munda mwamsanga pamene ali okhoza kugawanamo. Achichepere ambiri aphunzira kugawira magazini kapena trakiti ngakhale asanayambe kupezeka ku sukulu. Yambani mwamsanga kuphunzitsa “achichepere” anu, m’njira zochepera, “kuwopa Yehova”.
15. Ndi iti yomwe iri nsonga yachiŵiri, ndipo ndimotani mmene makolo angaikwaniritsire iyo?
15 Nsonga ina iri kukhala wokhazikika. Ichi chingachitidwe ngati nthaŵi zonse timamatira ku Mawu a Mulungu pophunzitsa, kulanga, ndi kuwongolera kumene timapereka kwa ana athu. Ngakhale pamene chibwera ku kupumula kapena zosangulutsa, khalani okhazikika mwa kulola maprinsipulo a Baibulo kulamulira zimene zidzaloledwa pa zochitika zoterozo. (Aefeso 6:4) Ichi chidzafunikira kuyesetsa, monga mmene Mawu a Mulungu momvekera bwino akusonyezera pamene akunena kuti: “Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pa mtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi powuka inu.” (Deuteronomo 6:4-9; 4:9; 11:18-21) Kukhazikika koteroko mkati mwa zaka kudzachita zambiri kuthandiza ana anu kukulitsa mtima wowopa Yehova.
16. (a) Ndi iti yomwe iri nsonga yachitatu, ndipo nchifukwa ninji iyi iri yofunika koposa chotero? (b) Ndi mafunso otani amene makolo ayenera kudzifunsa iwo eni?
16 Makolo ayeneranso kukalamira kusindikiza m’maganizo ndi mitima ya ana awo kuti iwo eni, monga makolo, ali “owopa Yehova.” (Masalmo 22:23) Njira imodzi mu imene iwo angachitire ichi iri mwa kugwiritsira ntchito uphungu wa teokratiki m’kuphunzitsa ndi kulanga ana awo. Iyi iri mbali yachitatu yomwe idzalingaliridwa. Dzifunseni inu eni: ‘Kodi ine mokhazikika ndimakhala ndi phunziro la Baibulo ndi ana anga?’ ‘Kodi ndimagwiritsira ntchito mokulira kwambiri kwa ana anga achichepere zothandizira zonga ngati Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndi Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuluyo?’ ‘Pamene iwo akukula, kodi ndimagwiritsira ntchito bukhu la Your Youth—Getting the Best out of It ndi nkhani za mu Galamukani! zakuti “Achichepere Akufunsa Kuti”?’ ‘Kodi ndimakonzekera kaamba ka maseŵera abwino ndi zosangulutsa zomwe sizikhala ndi chiyambukiro choipa pa ana anga?’ ‘Kodi ndavomereza zimene zanenedwa ndi gulu la Yehova ponena za maphunziro apamwamba?’ ‘Kodi ndikulangiza ana anga mofananamo? Kodi zonulirapo zimene ndakhazikitsa kaamba ka ana anga ziri zimene zidzawathandiza iwo kukhala ndi “mantha aumulungu”?’—Ahebri 5:7, NW.
17. Ndani amene amapindula pamene ana aphunzira kuwopa Yehova? Chitirani chitsanzo.
17 Mapindu ndi chisangalalo zidzabwera osati kokha kwa ana anu komanso kwa inu kaamba ka kuchita zonse zimene mungathe kuwalangiza iwo “kuwopa Yehova”. Mwachitsanzo, Mboni imene pamapeto pa tsiku, imadzimva, monga mmene mlongoyo akunenera, “wotoperatu” amalingalira chirichonse kukhala chabwino pamene amva mwana wake wamkazi wa zaka zisanu ndi ziŵiri akupemphera kwa Yehova. Misozi imabwera m’maso mwake ndipo amatsamwidwa ndi chisangalalo pamene amvetsera ku pemphero la mwana wake wamkazi: “Yehova wachikondi, ndikuthokozani kaamba ka zinthu zabwino zonse zimene mwachita kwa ine lerolino. Ndipo ndikuthokozani kaamba ka chakudya changa. Thandizani abale onse m’ndende ndi m’ndende za chibalo kupeza chakudya, Yehova, ndi abale ndi alongo onse owonda m’maiko ena. Athandizeninso iwo kupeza chakudya chokwanira, Yehova. Ndipo awo amene akudwala, athandizeni iwo kupeza bwino kotero kuti angapite ku misonkhano. Chonde lolani kuti angelo andiyang’anire ine pamene ndigona usiku, Yehova, ndi amayi anga ndi atate, ndi mbale wanga, ndi agogo anga akazi ndi agogo amuna, ndi abale ndi alongo onse m’chowonadi. Kupyolera mwa Mwana wanu Yesu, Amen.”
18. Ndimotani mmene timayambukirirana wina ndi mnzake m’nkhani iyi ya kuwopa Yehova?
18 M’nkhaniyi ya kuwopa Yehova, tiyenera kukumbukira kuti timayambukirana wina ndi mnzake ndi chitsanzo chimene timasonyeza. Makolo amayambukira ana awo. Akulu ndi atumiki otumikira amayambukira mipingo yawo. Oyang’anira omayendayenda amayambukira awo amene amawatumikira. Mwachiwonekere, ichi ndi chifukwa chake mafumu mu Israyeli analangizidwa kuŵerenga Lamulo la Mulungu masiku onse a moyo wawo kotero kuti “aphunzire kuwopa Yehova.” (Deuteronomo 17:18-20) Chitsanzo chimene mfumu ikakhazikitsa mwa kuwopa Yehova chikayambukira mtundu wonse.
19. Nkuchiyani kumene mbiri yakale imatsimikizira ponena za Israyeli?
19 Mbiri yakale imatsimikizira ku nsonga yakuti Israyeli monga mtundu, anataya kuwopa kwawo Yehova. Iwo analingalira kuti mwa kukhala ndi kachisi mu Yerusalemu chikatumikira monga chitetezero kwa iwo, monga mtundu wa chithumwa cha “mwaŵi”, mosasamala kanthu zakuti kaya iwo anamvera malamulo ake kapena ayi. (Yeremiya 7:1-4; Mika 3:11, 12) Koma iwo anali olakwa. Yerusalemu ndi kachisi wake zinawonongedwa. Pambuyo pake, pamene iwo anakhazikitsidwanso monga mtundu, iwo kachiŵirinso analephera kusonyeza kuwopa Yehova koyenera. (Malaki 1:6) Pali zambiri zimene tingaphunzire kuchokera ku chokumana nacho chimenechi, chomwe chidzakwaniritsidwa m’nkhani yotsatira.
20. Ndimotani mmene tingafupikitsire chifukwa chimene tiyenera kuwopera Yehova?
20 Kumbukirani, chotero, kuti kuwopa Yehova sikumafooketsa chikondi chathu kaamba ka iye; m’malomwake, kumalimbikitsa ndi kulimbitsa icho. Kumvera ku malamulo ake onse kudzatsimikizira osati kokha kuti timawopa Yehova komanso kuti timamkonda iye. Zonse ziŵiri ziri zofunika koposa. Chiri chosatheka kukhala ndi chimodzi popanda chinzake. Ndi chofunika chotani nanga kwa makolo kuti azamitse kuwopa Yehova kwaumulungu ndi kumkonda kumeneku mwa ana awo! Ndipo ndi chimwemwe chachikulu chotani nanga chimene ichi chimabweretsa ponse paŵiri kwa achikulire ndi achichepere! Lolani ife, chotero, timve njira yofanana monga mmene anachitira wamasalmo pamene iye ananena kuti: “Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu.”—Masalmo 86:11.
Nsonga za Kusinkhasinkhapo
◻ Ndimotani mmene ife ponse paŵiri tingakondere ndi kuwopa Yehova?
◻ Ndi ati omwe ali ena amapindu a kuwopa Yehova?
◻ Ndi nsonga zitatu ziti zimene zingathandize makolo kuthandiza ana awo kukulitsa mtima womwe umawopa Yehova?
◻ Ndimotani mmene timayambukirirana wina ndi mnzake m’nkhani ya kuwopa Yehova?
[Chithunzi patsamba 12]
Kuwopa Yehova kudzathandiza achichepere kukana ziyeso za kuchita zolakwa
[Chithunzi patsamba 14]
Makolo ayenera kuthandiza ana awo kukulitsa kuwopa Yehova kwenikweni
[Chithunzi patsamba 15]
“Chidzakhala bwino kwa awo owopa Mulungu wowona.”—Mlaliki 8:12, NW
[Mawu a Chithunzi]
By courtesy of Hartebeespoort Snake and Animal Park