Khalani ndi Mtima Woopa Yehova
“Ha! mwenzi akadakhala nawo mtima wotere wakundiopa ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse.”—DEUTERONOMO 5:29.
1. Kodi tingatsimikize bwanji kuti tsiku lina anthu sadzachita mantha?
ANTHU avutika ndi mantha kwa zaka zambirimbiri. Anthu miyandamiyanda akhala ndi nkhaŵa yosatha chifukwa choopa njala, matenda, upandu, kapena nkhondo. N’chifukwa chake, mawu oyamba m’chikalata cha mfundo za ufulu wachibadwidwe cha Universal Declaration of Human Rights amanena kuti akufuna kubweretsa dziko limene anthu onse sadzachita mantha.a N’zosangalatsa kuti Mulungu akutitsimikizira kuti dziko lotero lidzafika—ngakhale kuti si anthu amene adzalibweretse. Yehova akutilonjeza kudzera mwa mneneri wake Mika kuti m’dziko lake latsopano la chilungamo, ‘palibe amene adzaopseza anthu ake.’—Mika 4:4.
2. (a) Kodi Malemba amatilimbikitsa motani kuopa Mulungu? (b) Kodi pangakhale mafunso otani pamene tikulingalira za udindo wathu woopa Mulungu?
2 Komabe, mantha angakhalenso othandiza. Malemba akulimbikitsa atumiki a Mulungu mobwerezabwereza kuti aziopa Yehova. Mose anawauza Aisrayeli kuti: “Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira iyeyu.” (Deuteronomo 6:13) Patapita zaka mazana angapo Solomo analemba kuti: “Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” (Mlaliki 12:13) Ifenso timalimbikitsa anthu ‘kuopa Mulungu ndi kum’patsa ulemerero’ kudzera m’ntchito yathu yolalikira imene angelo akutiyang’anira. (Chivumbulutso 14:6, 7) Kuphatikiza pa kuopa Yehova, Akristu afunika kum’konda ndi mtima wonse. (Mateyu 22:37, 38) Kodi tingakonde bwanji Mulungu pomwenso tikumuopa? N’chifukwa chiyani n’koyenera kuopa Mulungu wachikondi? Kodi tingapindule chiyani ngati tiopa Mulungu? Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, choyamba tidziŵe tanthauzo la kuopa Mulungu ndi kuona mmene mantha ameneŵa alili maziko a ubale wathu ndi Yehova.
Ulemu Waukulu ndi Mantha
3. Kodi kuopa Mulungu kumatanthauzanji?
3 Akristu ayenera kuopa Mulungu, Mlengi wawo. Tanthauzo lina la mantha ameneŵa ndilo “kuopa ndi kupereka ulemu waukulu kwa Mlengi ndi kusafuna kumukhumudwitsa.” Motero, kuopa Mulungu kumakhudza mbali ziŵiri zofunika kwambiri pa moyo wathu. Mbali zimenezi ndizo mmene timaonera Mulungu ndi mmene timaonera makhalidwe amene iye amadana nawo. Mwachidziŵikire, mbali zonse ziŵirizi n’zofunika kwambiri ndipo n’zoyenera kuzilingalira mosamalitsa. Malinga ndi kunena kwa buku lakuti Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words, kwa Akristu mantha a ulemu ameneŵa ndi amene ‘amatsogolera moyo wawo, pankhani zauzimu kapena zamakhalidwe.’
4. Kodi tingatani kuti timuope ndi kum’lemekeza kwambiri Mlengi wathu?
4 Kodi tingatani kuti tikhale ndi mantha ndi kulemekeza kwambiri Mlengi wathu? Timasoŵa chonena tikamaona kukongola kwa mapiri, zigwa, mitsinje komanso poona mathithi ochititsa kaso kapena kuloŵa kwa dzuŵa kochititsa chidwi. Malingaliro ameneŵa amakula tikazindikira ndi maso a chikhulupiriro kuti ndi Mulungu amene analenga zinthu zimenezi. Ndiponso, timazindikira monga anachitira Mfumu Davide kuti ndife opanda pake poyerekeza ndi zinthu zochititsa mantha zimene Yehova analenga. “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mum’kumbukira?” (Salmo 8:3, 4) Mantha aakulu ameneŵa amatichititsa kulemekeza kwambiri Yehova, zimene zimatipangitsa kum’thokoza ndi kum’tamanda chifukwa cha zonse zimene amatichitira. Davide analembanso kuti: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.”—Salmo 139:14.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuopa Yehova, ndipo tili ndi chitsanzo chabwino chotani pankhani imeneyi?
5 Kukhala ndi mantha ndi ulemu waukulu kumatichititsa kuopa ndi kulemekeza mphamvu za Mulungu monga Mlengi ndiponso udindo wake monga woyenera kulamulira chilengedwe chonse. M’masomphenya amene mtumwi Yohane anaona, “iwo amene anachilaka chilombocho, ndi fano lake,” omwe ndi otsatira Kristu odzozedwa m’malo awo a kumwamba, analengeza kuti: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu n’zolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye?” (Chivumbulutso 15:2-4) Kuopa Mulungu chifukwa cha kulemekeza kwambiri ulemerero wake kumachititsa olamulira anzake a Kristu mu Ufumu wa kumwamba ameneŵa kulemekeza Mulungu monga wolamulira wamkulu. Kodi sitipeza chifukwa choyenera choopera Yehova tikamalingalira zonse zimene wachita ndi mmene amayendetsera chilengedwe chonse mwachilungamo?—Salmo 2:11; Yeremiya 10:7.
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuopa kumukhumudwitsa Yehova?
6 Komabe, kuwonjezera pa mantha ndi ulemu waukulu, kuopa Mulungu kuyenera kuphatikizapo kupeŵa kumukhumudwitsa kapena kusamumvera. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti, ngakhale kuti Yehova ndi “wolekereza, [“wosakwiya msanga,” NW] ndi wa ukoma mtima wochuluka,” tizikumbukira kuti iye ndi “wosamasula wopalamula.” (Eksodo 34:6, 7) Ngakhale kuti Yehova ndi wachikondi ndiponso wachifundo, salekerera zosalungama ndi machimo adala. (Salmo 5:4, 5; Habakuku 1:13) Anthu amene amachita dala zinthu zimene Yehova amaziona kuti ndi zoipa komanso salapa ndiponso amene amatsutsana naye, adzawalanga. Monga mmene mtumwi Paulo ananenera, “kugwa m’manja a Mulungu wamoyo n’koopsa.” Kuopa kugwa m’manja a Mulungu kumatiteteza kwambiri.—Ahebri 10:31.
‘M’mamatireni’
7. Kodi tili ndi zifukwa zotani zokhulupirira mphamvu zopulumutsa za Yehova?
7 Kuopa Mulungu kom’patsa ulemu ndi kuzindikira mphamvu zake zochititsa mantha ndizo zinthu zofunika kwambiri kuti tikhulupirire ndi kudalira Yehova. Timatetezeka ndi kukhala ndi chidaliro tikakhala m’manja a Yehova otitsogolera monga mmene mwana amaonera kuti ndi wotetezeka bambo ake akakhala pafupi. Taonani mmene Aisrayeli anachitira Yehova atawatulutsa mu Igupto: “Ndipo Israyeli anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aigupto, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova.” (Eksodo 14:31) Zimene zinam’chitikira Elisa zikuperekanso umboni wakuti “mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.” (Salmo 34:7; 2 Mafumu 6:15-17) Mbiri yamakono ya anthu a Yehova ndiponso zimene ife patokha takumana nazo zikutsimikizira kuti Mulungu amasonyeza mphamvu zake m’malo mwa anthu amene amamutumikira. (2 Mbiri 16:9) Motero timafika pozindikira kuti “wakuopa Yehova akhulupirira kolimba.” (Miyambo 14:26)
8. (a) N’chifukwa chiyani kuopa Mulungu kumatichititsa kuyenda m’njira zake? (b) Fotokozani mmene ‘tingamamatirire’ kwa Yehova.
8 Kuopa Mulungu kumatichititsa kumukhulupirira ndi kumudalira ndiponso kumatilimbikitsa kutsatira njira zake. Pamene Solomo anali kupatulira kachisi, anapemphera kwa Yehova kuti: “[Israyeli] aope Inu, kuyenda m’njira zanu masiku onse akukhala iwo m’dziko limene munapatsa makolo athu.” (2 Mbiri 6:31) M’mbuyomo, Mose anali atauza Aisrayeli kuti: “Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mawu ake, ndi kum’tumikira iye, ndi kum’mamatira.” (Deuteronomo 13:4) Monga mmene mavesiŵa akusonyezera, kufuna kuyenda m’njira za Yehova ndi “kum’mamatira” kumachitika ngati tikukhulupirira ndi kudalira Mulungu. Inde, kuopa Mulungu kumatichititsa kumvera Yehova, kum’tumikira, ndi kum’mamatira, monga mmene mwana angamamatirire bambo ake amene amawakhulupirira ndi kuwadalira kotheratu.—Salmo 63:8; Yesaya 41:13.
Kukonda Mulungu Ndiko Kumuopa
9. Kodi kukonda Mulungu ndi kumuopa n’zogwirizana bwanji?
9 Malinga ndi Malemba, kuopa Yehova sikulepheretsa kumukonda. N’chifukwa chake Aisrayeli anawalangiza kuti ‘aziopa Yehova, kuyenda m’njira zake zonse, ndi kumukonda.’ (Deuteronomo 10:12) Motero, kuopa Mulungu ndi kumukonda n’zogwirizana kwambiri. Kuopa Mulungu kumatichititsa kuyenda m’njira zake, ndipo kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timamukonda. (1 Yohane 5:3) Zimenezi n’zomveka chifukwa ngati tikumukonda munthu, timaopa kumukhumudwitsa. Aisrayeli anamukhumudwitsa Yehova mwa kum’pandukira m’chipululu. Ndithudi, sitingafune kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse Atate wathu wakumwamba. (Salmo 78:40, 41) Mosiyana ndi zimenezo, popeza “Yehova akondwera nawo akumuopa Iye,” kumvera ndi kukhulupirika kwathu kumasangalatsa mtima wake. (Salmo 147:11; Miyambo 27:11) Kukonda Mulungu kumatichititsa kum’sangalatsa, ndipo kumuopa kumatithandiza kupeŵa kumukhumudwitsa. Kukonda Mulungu ndi kumuopa n’zogwirizana osati zotsutsana.
10. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali wokondwa kuopa Yehova?
10 Moyo wa Yesu Kristu umasonyeza mmene tingakondere Mulungu kwinaku tikumamuopa. Mneneri Yesaya analemba za Yesu kuti: “Mzimu wa Yehova udzam’balira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziŵa ndi wakuopa Yehova; ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova.” (Yesaya 11:2, 3) Malinga ndi ulosi umenewu, mzimu wa Mulungu unam’chititsa Yesu kuopa Atate wake wakumwamba. Ndiponso, tikuona kuti kuopa kumeneku sikunafanane ndi mtolo. M’malo mwake kunam’chititsa kukhala wokhutira. Yesu anali wokondwa kuchita zimene Mulungu ankafuna ndipo ankam’sangalatsa, ngakhale nthaŵi imene zinthu zinafika povuta kwambiri. Atatsala pang’ono kuti amugwire kukamupha pa mtengo wozunzirapo, iye anauza Yehova kuti: “Si monga ndifuna Ine, koma Inu.” (Mateyu 26:39) Chifukwa cha kuopa Mulungu kumeneku, Yehova anamvera pempho la Mwana wakeyo ndipo anam’limbikitsa ndi kum’pulumutsa ku imfa.—Ahebri 5:7.
Kuphunzira Kuopa Yehova
11, 12. (a) N’chifukwa chiyani tifunika kuphunzira kuopa Mulungu? (b) Kodi Yesu amatiphunzitsa bwanji kuopa Yehova?
11 Kuopa Mulungu sikumangobwera kokha monga mmene amachitira mantha achibadwa amene timakhala nawo poona mphamvu ndi ulemerero wa chilengedwe. N’chifukwa chake Davide Wamkulu yemwe ndi Yesu Kristu, akutiitana molosera kuti: “Idzani ananu ndimvereni ine: ndidzakulangizani za kumuopa Yehova.” (Salmo 34:11) Kodi Yesu angatiphunzitse bwanji kuopa Yehova?
12 Yesu amatiphunzitsa kuopa Yehova mwa kutithandiza kudziŵa makhalidwe abwino a Atate wathu wakumwamba. (Yohane 1:18) Popeza Yesu anasonyeza bwino umunthu wa Atate wake, chitsanzo chake chimavumbula mmene Mulungu amaganizira ndi mmene amachitira zinthu kwa ena. (Yohane 14:9, 10) Ndiponso, kudzera mu nsembe ya Yesu, timapeza mwayi wolankhula ndi Yehova pamene tim’pempha kuti atikhululukire machimo athu. Chifundo chachikulu cha Mulungu chimenechi ndi chifukwa champhamvu chomuopera. Wamasalmo analemba kuti: “Kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.”—Salmo 130:4.
13. Kodi ndi njira ziti zimene azifotokoza m’buku la Miyambo zimene zingatithandize kuopa Yehova?
13 Buku la Miyambo linafotokoza mwatsatanetsatane njira zimene zingatithandize kuopa Mulungu. “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire . . . pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu.” (Miyambo 2:1-5) Motero, kuti tiope Mulungu tifunika kuphunzira Mawu ake, kuyesetsa moona mtima kumvetsa malangizo ake, ndi kusamalitsa uphungu wake.
14. Kodi tingatsatire bwanji uphungu umene anawapatsa mafumu a Israyeli?
14 Mfumu iliyonse ya Israyeli wakale anailangiza kukopera Chilamulo m’buku lake ‘n’kumaŵerenga masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mawu onse a chilamulocho ndi malemba amenewo.’ (Deuteronomo 17:18, 19) Kwa ifenso, kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo n’kofunika kwambiri ngati tikufuna kuphunzira kuopa Yehova. Tikamagwiritsa ntchito mfundo za chikhalidwe za m’Baibulo m’moyo wathu, pang’onopang’ono timapeza nzeru za Mulungu ndi kum’dziŵa kwambiri. Timafika ‘pozindikira kuopa Yehova’ chifukwa timaona zotsatira zabwino zomwe timapeza m’moyo wathu chifukwa chochita zimenezi. Ndiponso ubale wathu ndi Mulungu timauona kukhala wamtengo wapatali. Kuwonjezera apa, ana ndi achikulire omwe angamvetsere zimene Mulungu akuphunzitsa, kuphunzira kumuopa ndiponso kuyenda m’njira zake mwa kusonkhana ndi okhulupirira anzathu.—Deuteronomo 31:12.
Wodala Yense Wakuopa Yehova
15. Kodi kuopa Mulungu kukugwirizana motani ndi kumulambira kwathu?
15 Malinga ndi zimene tafotokozazi, tingaone kuti kuopa Mulungu ndi khalidwe lofunika limene tonsefe tifunika kukhala nalo, chifukwa ndi mbali yofunika ya kulambira kwathu Yehova. Kumatichititsa kumudalira kotheratu, kuyenda m’njira zake, ndi kum’mamatira. Monga mmene anachitira Yesu Kristu, kuopa Mulungu kungatithandizenso kukwaniritsa lumbiro lathu la kudzipatulira nthaŵi ino komanso kwamuyaya.
16. N’chifukwa chiyani Yehova amatilimbikitsa kuti tizimuopa?
16 Kuopa Mulungu sikufuna zimene sitingathe kapena kuumitsa zinthu mopambanitsa. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m’njira zake.” (Salmo 128:1) Yehova amatilimbikitsa kumuopa chifukwa akudziŵa kuti khalidwe limeneli lidzatiteteza. Tikuona kutidera nkhaŵa ndi kutikonda kwake m’zimene anauza Mose kuti: “Ha! mwenzi [Aisrayeli] akadakhala nawo mtima wotere wakundiopa ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana awo nthaŵi zonse!”—Deuteronomo 5:29.
17. (a) Kodi timapindula chiyani ngati tiopa Mulungu? (b) Kodi ndi mbali ziti za kuopa Mulungu zimene tipende m’nkhani yotsatirayi?
17 N’chimodzimodzinso kuti ngati titakhala ndi mtima woopa Mulungu, zidzatiyendera bwino. Motani? Choyamba, kuchita zimenezo kudzasangalatsa Mulungu ndipo kudzatichititsa kumuyandikira kwambiri. Davide anadziŵa kuchokera m’zimene anaona kuti “[Mulungu] adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwawo, nadzawapulumutsa.” (Salmo 145:19) Chachiŵiri, tidzapindula ngati tiopa Mulungu chifukwa kudzakhudza mmene timaonera zinthu zoipa. (Miyambo 3:7) Nkhani yotsatirayi ipenda mmene mantha ameneŵa amatitetezera ku ngozi zauzimu, ndipo ipendanso zitsanzo zina za m’Malemba za anthu amene anaopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.
[Mawu a M’munsi]
a Pa msonkhano waukulu wa General Assembly wa bungwe la United Nations anagwirizana kutsatira mfundo za m’chikalata cha ufulu wachibadwidwe Universal Declaration of Human Rights pa December 10, 1948.
Kodi Mungayankhe Mafunso Aŵa?
• Kodi kuopa Mulungu kumatanthauzanji, ndipo kumatikhudza bwanji?
• Kodi kuopa Mulungu kukugwirizana motani ndi kuyenda ndi Mulungu?
• Kodi chitsanzo cha Yesu chikusonyeza motani kuti kuopa Mulungu n’kogwirizana ndi kum’konda?
• Kodi tingatani kuti tikhale ndi mtima woopa Yehova?
[Chithunzi patsamba 17]
Mafumu a Israyeli anawalamula kukopera Chilamulo m’buku lawo ndi kumaŵerenga tsiku ndi tsiku
[Chithunzi patsamba 18]
Kuopa Yehova kumatichititsa kum’dalira monga mmene mwana amadalirira bambo ake
[Mawu a Chithunzi patsamba 15]
Nyenyezi: Chithunzi chojambulidwa ndi Malin, © IAC/RGO 1991