Msonkhano Womwe Unawonjezera Kukhulupirira Kwathu Yehova
ATATE wathu wa kumwamba, Yehova Mulungu, amadziŵa kokha chimene timafuna. Ndipo iye amachiika icho m’maganizo a atumiki ake odzipereka omwe akutsogoza ntchito yake pa dziko lapansi kukwaniritsa chosowa chimenecho. Ichi chinganenedwedi tero ponena za Misonkhano ya Chigawo ya “Khulupirirani Yehova”, yomwe inachitidwa kuzungulira pa dziko lonse lapansi kuyambira mu June 1987 kunka mtsogolo. Iyo ndithudi inatumikira kulimbikitsa Akristu motsutsana ndi kusuliza, kukaikira, ndi kusakhulupirira kumene kuli kofala m’dziko.
Mutu wakuti “Khulupirirani Yehova” unamangiriridwa mwaluso mu programu. Iwo unawunikiridwa ndi ndemanga zomwe zinali zamphamvu ndi zachindunji, zomwe zinazindikiritsidwa ndi kumvekera bwino ndi kulunjika. Zonsezi zinalimbikitsa kukhulupirira Yehova kwa amvetseriwo. Iwo ankapita kunyumba zawo ndi mutuwo utasindikizidwa bwino pa mitima yawo ndi maganizo, atagamulapo kuti mwakachitidwe kawo ndi mawu awo iwo ayenera kulengeza kwa onse kuti akukhulupirira kotheratu mwa Yehova.
“Khulupirirani Yehova Anthu Inu”
Mawu amenewo opezeka pa Yesaya 26:4 analongosola mutu wa tsiku loyamba. Moyenerera kwambiri, programu inatsegula ndi nkhani yakuti “Tcherani Khutu Lanu ku Zonena za Mulungu.” Mlankhuli anasonyeza kuti kalongosoledwe kameneka, komwe kamawoneka nthaŵi zambiri m’Mawu a Mulungu, kamatanthauza kupereka chisamaliro chotheratu ponse paŵiri m’maganizo ndi mu mtima ku zimene zimanenedwa, ndi cholinga cha kugwiritsira ntchito zimene zamvedwa. Ichi chimatanthauza kusonyeza kudziletsa ndi kusumika maganizo pa zimene zanenedwa, osalola maganizo kusamukasamuka. Kokha mwakutchera khutu lathu ndi pamene kukhulupirira kwathu Yehova kudzalimbikitsidwa ndi zimene timamva ndipo kenaka tidzasonkhezeredwa kugwirira ntchito pa chimene chanenedwa. Ndipo kodi umenewu suyenera kukhala mkhalidwe wathu nthaŵi iriyonse pamene timamva Mawu a Mulungu akufotokozedwa, monga ngati pa misonkhano yathu ya mpingo?
Tcheyamani wa msonkhano anapereka mutu wotsatira, “Awo Okhulupirira Yehova Ali Achimwemwe Kukhala Pano.” Iye analoza kuti ngati kukhulupirira kwathu Yehova kuli kwakukulu, chimwemwe chathu chimawonjezerekanso. Kukhulupirira Yehova kumatanthauza kuyedzamira kotheratu ndi kotsimikizirika pa iye. Ukulu wa chidziŵitso chathu cha Yehova ndi chikondi chake kaamba ka iye, udzatanthauzanso kulimba kwa kukhulupirira kwathu mwa iye. Mutu wa msonkhanowo sunali kokha kalankhulidwe wamba. Timasonyeza kukhulupirira kwathu Yehova m’njira zambiri, osati yochepa koposa ya izo yomwe iri kusonyeza kudera nkhaŵa kaamba ka ena. Ku chisangalatso cha onse pamapeto a ndemanga zake, tcheyamaniyo anapereka chotulutsidwa choyamba—chida chokongola, chokhoza kugwirirapo ntchito chochitira umboni. Kanali katrakiti kakuti Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo.
Pambuyo pa kukambitsirana zitsanzo zodziŵika za Davide pamene anayang’anizana ndi chimphona Goliati, mlankhuli wotsatira anasonyeza “Mmene Ena Akhulupirira Yehova” m’nthaŵi zamakono. Mwachitsanzo, panali mlongo amene mwamuna wake wosakhulupirira, ali ndi mfuti m’manja, anawopsyeza kumupha iye ngati akapitiriza kupita ku misonkhano. Ena anasonyeza kukhulupirira kwawo Yehova pamene anauzidwa kuti moyo wawo unadalira pa kulandira kupatsidwa mwazi. Achichepere apereka chitsimikiziro cha kukhulupirira kwawo Yehova mwa kutsutsa zitsenderezo za kupita ku maseŵera kapena kusankha maphunziro apamwamba koposa pambuyo pa kumaliza maphunziro a ku sekondale.
Programu ya pa Lachisanu m’mawa inatha ndi nkhani yakuti “Anthu Odzipatula Kuchokera ku Dziko.” Timasonyeza kuti timakhulupirira Yehova mwa kusunga khalidwe lathu ndi anthu osiyana ziwalo kukhala lopanda chitonzo, mwakulola maprinsipulo Achikristu kulamulira zosangulutsa zathu, ndi mwakupewa kavalidwe ndi kapesedwe konse kamene kamaphimba kusiyanitsa pakati pa anthu osiyana ziwalo. Mwakudzipatula kwathu koteroko kuchoka ku dziko, nthaŵi ndi nthaŵi umboni wamphamvu umaperekedwa, ngakhale kutulukapo mu ena kubwera m’chowonadi.
Lachisanu masana, programu inayamba ndi nkhani yakuti “Kuchita Upainiya Kumafulumiza Kukula Kwauzimu.” Ndipo chimenecho chiri chowona motani! Kupyolera m’Mawu a Yehova, mzimu wake woyera, ndi gulu lake, Mulungu akupereka zimene tifunikira kuti tipite patsogolo kufika ku “munthu wachikulire,” koma upainiya umatiika ife m’malo akupanga kugwiritsira ntchito kwabwino ndi kokwanira kwa zopereka zonse zauzimu zimenezi. (Aefeso 4:13) Kupyolera mwa kufunsa mafunso, apainiya analongosola mmene utumiki wa nthaŵi zonse wathandizira iwo kukulitsa mokwanira chipatso cha mzimu wa Mulungu, kusonyeza chikondi chokulira kaamba ka anthu, ndi kukhala okhutiritsa kwambiri mu utumiki, ndi kukhulupirira Yehova ku mlingo wokulira, ndipo chotero kukulitsa ndi unansi wathithithi ndi iye. Zonsezi zafulumiza kukula kwawo kwauzimu.
Kenaka inabwera nkhani yaikulu, “Anthu Okhulupirira Yehova Nthaŵi Zonse.” Nkhani yodzutsa maganizo imeneyi inasonyeza kuti tiri osiyana ndi dziko chifukwa timakhulupirira Yehova kotheratu. Yozikidwa pa malemba osiyanasiyana kuchokera m’bukhu la Yesaya, mlankhuliyo anasonyeza mmene tawonera maulosi olimbikitsa amenewa akukwaniritsidwa mwa Mboni za Yehova chifukwa timakhulupirira Mulungu. Ndi chidaliro, tikuyang’ana kutsogolo ku nthaŵi mtsogolo mwaposachedwapa pamene Yehova adzasonyeza ukali wake kulinga ku mitundu yonse ndipo kenaka kubweretsa Paradaiso.
Osonkhanawo analimbikitsidwa kuti “Falitsani Mbiri Yabwino pa Mwaŵi Uliwonse.” Pambuyo pa kugogomezeredwa kwa kufunika kwa kuchita chimenecho, unyinji wa zitsanzo unasonyeza mmene katrakiti katsopano ka Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo kangagwiritsiridwe ntchito mokhutiritsa ponse paŵiri mu umboni wa nthaŵi zonse ndi wa mwamwaŵi. Ndithudi, nthaŵi zonse timafunikira kukhala ndi matrakiti amenewa limodzi nafe, popeza kufalitsa mbiri yabwino pa mwaŵi uliwonse kuyenera kukhala chizindikiritso cha mboni iriyonse ya Yehova ndipo iri njira ya kusonyezera kuti timakhulupirira mwa iye.
Yoyamikiridwa kwambiri inali nkhani yakuti “Makolo—Fikirani Mtima wa Mwana Wanu Kuyambira pa Ukhanda.” Kwa mwana kuti akule ndi kukhulupirira Yehova, kuphunzitsidwa kwake kuyenera kuyambira ku ubwana ndipo kuyenera kukhala koyambirira. Kokha mwanjira imeneyo chidzakhala chotheka kuchotsa zisonkhezero zonse zoipa za wailesi ya kanema, ndi sukulu, za m’khwalala. ‘Lolani mwana wanu awone mwa inu chimene mukufuna kuti iye akhale,’ makolo anauzidwa tero. Inde, kupereka chitsanzo chabwino iri njira yabwino koposa ya kufikira mtima wa mwana. Mbali zonse za utumiki wopatulika ziyenera kudza mwachibadwa ndipo zodzetsa chimwemwe ngati mkhalidwe wa panyumba uti ukhale wauzimu. Sitiyenera kufunikira kuipidwa ndi nthaŵi ndi kuyesetsa kolowetsedwamo. Pitirizani kufikira mtima wa mwanayo mwakulankhuzana kwabwino. Sonyezani kulimba mtima ndi chikondi, ndipo sonyezani kumvetsetsa pamene mukupereka chilango. Perekani chitamando ndi mphatso pamene ziyenerera, koma musapatse chiphuphu mwana wanu.
Kubwera ku chigwirizano chathithithi ndi mavuto owopsya pakati pa zina za Mboni zachichepere inali nkhani yakuti “Achichepere—Pewani Kutsogoza Moyo wa Paŵiri.” Nchifukwa ninji ena amayesera kutsogoza moyo wa paŵiri? Chifukwa iwo amafuna chivomerezo cha makolo awo ndi mpingo ndipo komabe amawopa kutonzedwa ndi a msinkhu wawo a kudziko. Kapena iwo amadzimva kuti akuphonya zosangulutsa zina ngati sasuta fodya, kumwa anamgoneka, kapena kutengamo mbali mu mkhalidwe woipa wa chisembwere. Koma palibe njira yopulumukira nsonga yakuti kutsogoza moyo wa paŵiri koteroko kumabweretsa chitonzo pa Yehova, kuvutika mtima kwa makolo, ndi chisoni kwa mwiniyo. Aliyense wofesa kuthupi adzatuta chivundi, pamene kuli kwakuti kusunga unansi wabwino ndi Yehova, kukhulupirira iye kotheratu, kumachinjiriza munthu kuchokera ku kutsogoza moyo wa paŵiri.—Agalatiya 6:8.
Kugogomezera mwamphamvu maprinsipulo amenewa chinali chitsanzo chomwe chinatsatirapo mwamsanga. Chokhala ndi mutu wakuti Kugonjera Mokhulupirika kwa Yehova ndi Gulu Lake, chinali ndi chakudya chambiri kaamba ka malingaliro pamene chinachitira chitsanzo mmene mkulu anadzimvera kukhala wokakamizidwa kutsika pa mathayo chifukwa mwana wake wamkazi anavumbulutsidwa kukhala mmodzi wotsogoza moyo wa paŵiri. Chitsanzocho chinatulutsa zisonyezero za chiyamikiro zambiri zodzutsa maganizo.
“Khulupirira Yehova ndipo Chita Chokoma”
Wozikidwa pa Masalmo 37:3, uwu unali mutu wa tsiku lachiŵiri la msonkhano. Pambuyo pa kulingaliridwa kwa lemba latsiku, limene linaphatikizapo chilimbikitso cha kuchita ichi tsiku ndi tsiku, programuyo inasonyeza nkhani yosiirana yokhala ndi mbali zitatu yokhala ndi mutu wakuti “Kusonyeza Kukhulupirira Kwathu Yehova.” Mlankhuli woyamba anasonyeza kufunika kwa kuchita ichi “Mwakuphunzira Mwaluso Mawu a Mulungu.” Ichi tiyenera kuchita kuti tipeŵe msampha wa kukhutiritsidwa ndi machenjera a kukondetsa zinthu zakuthupi, khalidwe loipa la chisembwere, ndi mpatuko. Sosaite yapereka zothandizira phunziro la Baibulo zambiri, monga ngati Watch Tower Publications Index 1930-1985 yatsopano. Kokha mwakutenga mwaŵi wokulira wa choperekachi ndi pamene tingapeze unansi wabwino wokhulupirika ndi Atate wathu wa kumwamba ndi kukhala okhutiritsa monga Mboni zake.
Mlankhuli wotsatira anagogomezera nsonga yakuti kukhulupirira Yehova kumasonyezedwa “Mwakugwiritsira Ntchito Zinthu Zophunziridwa.” Inde, tifunikira kukhala ochita nawo Mawu, nthaŵi zonse kudera nkhaŵa za kupanga kupita patsogolo. M’njira zotani? Nkulekeranji, mu unansi wathu ndi ena, m’kavalidwe ndi kapesedwe kathu, m’kufunafuna choyamba Ufumu wa Mulungu, ndi m’kupititsa patsogolo mtendere ndi umodzi pakati pa abale athu! Kuti tipeŵe chimo la kulankhula mwasontho, tiyenera kukhala osamalira kusunga malo athu m’banja ndi mu mpingo. Ngati ife chotero tigwiritsira ntchito zinthu zimene tiphunzira, chidzakhala chowonekera kwa onse kuti timakhulupirira mwa Yehova.
Nkhani yosiiranayo inatha ndi kukambitsirana kwa mutu wakuti “Kusonyeza Kukhulupirira Kwathu Yehova—Mwa Kudzikangalitsa Ife Eni M’munda.” Mwakuchita ichi, timasonyeza chikondi chathu kaamba ka Mulungu ndi mnansi ndi kudzichinjiriza ife eni. Tingakhale okhutiritsidwa ndi utumiki wofunda, wongokwaniritsa thayo, koma kodi Yehova ali? Kodi Mwana wake samatifulumiza ife kudzikanikiza ife eni mwamphamvu? (Luka 13:24) Ziwonjezeko zimene timapitiriza kuwona mu ofalitsa, apainiya, ndi avereji ya maora owonongedwa mu utumiki wa m’munda ziyenera kutisonkhezera ife kuyesera kuchita zowonjezereka mwaumwini. Kodi icho sichiri tero? Mwa ntchito yachangu yoteroyo, tidzaika chitsanzo chabwino, kusonyeza kukhulupirira kwathu Yehova, ndipo tidzapeza kumwetulira kwake kwa chivomerezo.
Kenaka chinabwera chifunsiro ku chikumbumtima chathu m’nkhani yakuti “Zolowerani Kupereka Modzala Manja.” Ndi mochulukira chotani nanga mmene Yehova amapereka kwa ife mwauzimu ndi mwa kuthupi! Timasonyeza chiyamikiro chathu mwa kumutsanzira iye ponse paŵiri m’kuchitira umboni ndi mwa kupereka mwachuma kulinga ku ntchito yolalikira. Kodi tingachepetseko zosangulutsa za mtengo wapatali kotero kuti tigawire modzala manja?
Nkhani ya ubatizo, “Kudzipereka Kwanu ndi Ubatizo Kumachitira Chithunzi Kukhulupirira Kwanu Yehova,” inasonyeza chifukwa chimene timakhulupirira Mulungu ndipo osati anthu. Ubatizo wa m’madzi umasonyeza kufa ku njira ya khalidwe lathu lakale ndi kuukitsidwa ku njira ya moyo yomwe imagwirizana ndi chifuno cha umulungu. Pambuyo pa chimenecho, tiyenera kupitirizabe ‘kusonyeza chiweruzo, chikondi, kukoma mtima, ndi kuyenda modekha ndi Mulungu wathu.’ (Mika 6:8) Pakati pa awo amene anabatizidwa panali mtsikana wa zaka zakubadwa 8 yemwe amatsogoza maphunziro aŵiri a Baibulo ndi anzake a ku sukulu, mwamuna wa zaka zakubadwa 79, ndi wakufa ziwalo zonse wa zaka zakubadwa 44.
Programu ya pa Loŵeruka masana inayamba ndi nkhani yakuti “Kuchita ‘Zinthu Zofunika’ kuti Tikondweretse Mulungu.” Yozikidwa pa Machitidwe 15:28, 29, iyo inasonyeza kufunika kwa kuzoloŵeretsa adokotala athu ndi kaimidwe kathu pa mwazi vuto la zamankhwala lisanabuke ndipo inapereka malingaliro abwino a mmene ichi chingachitidwire.
Nkhani imene inadzutsa ndemanga yoyanjidwa kwambiri inali yakuti “Thayo la Kubala Ana M’nthaŵi Ino ya Mapeto.” Iyo inapereka kawonedwe kolinganizika, kusonyeza kuti pamene kuli kwakuti kubala ana kungabweretse chimwemwe chochuluka, iko kumabweretsanso mathayo ambiri ndipo kaŵirikaŵiri amatulukamo m’kuwaŵidwa mtima, monga ngati pamene ana achita cholakwa. Amayi mwapadera angakhoze kuvutika mwauzimu chifukwa cha thayo la kubala ana.
Kenaka panabwera nkhani yakuti “Akulu—Chinjirizani Kukhulupirira Kwanu.” Kukhulupirira kumeneku kuli kuŵeta gulu la Mulungu—kutsogolera, kudyetsa, ndi kulichinjiriza, m’chigwirizano ndi Yesaya 32:1, 2. Kupanga chilungamo ku mathayo a banja pamene akusamalira mathayo a mpingo kumapereka chitokoso chenicheni. Kwa akulu kuti achinjirize kukhulupirira kwawo kumatanthauzanso kupewa msampha wa zinthu za kuthupi, zosangulutsa zonkitsa, ndi zosangulutsa zoipa. Pakati pa awo amene anafunsidwa pa msonkhano wa chigawo wa pa Dortmund mu Federal Republic ya Germany anali mkulu yemwe wakhala akuchinjiriza kukhulupirira kwake kwa zaka 60.
Nkhani yakuti “Khalani Omvera kwa Awo Okutsogolerani” moyenerera inatsatira. Chikondi chidzatithandiza ife kukhala ogonjera ndi omvera kwa oyang’anira a mpingo ndipo kudzatichinjiriza ife kusakhala osaleza mtima chifukwa iwo sali angwiro, popeza nafenso sitiri angwiro. (Ahebri 13:17) Mwakusonyeza ulemu kaamba ka akulu m’nkhani zazikulu ndi zazing’ono, timawathandiza iwo kusenza mathayo awo m’malo mwa kuwonjezera ku iwo.
Programu ya pa Loŵeruka inafika kumapeto ndi nkhani yosiirana ya mbali zitatu “Mawu a Mulungu Ngamoyo,” yozikidwa pa Ahebri 4:12. Mlankhuli woyamba anasonyeza kuti ali amoyo chifukwa “Amapereka Mphamvu ya Kusintha.” Lerolino, mofanana ndi m’nthaŵi ya Baibulo, tiri ndi zitsanzo zambiri zosonyeza mmene kukhulupirira Mawu a Mulungu kwapangitsira anthu kupanga masinthidwe a akulu m’miyoyo yawo ndipo kwapatsa iwo mphamvu kulalikira mopanda mantha.
Mbali yachiŵiri ya nkhani yosiirana imeneyi pa Mawu a Mulungu inasonyeza kuti “Ali Akuthwa Koposa Lupanga Lakuthwa Konse Konse.” Amatithandiza ife kudula ziphunzitso zonyenga za Chibabulo kukhala zidutswa. Amatithandizanso ife ‘kugawanitsa pakati moyo ndi mzimu’ m’chakuti amatitheketsa ife kusiyanitsa pakati pa kachitidwe kathu ndi zisonkhezero zathu zenizeni. Mwa kugwiritsira ntchito “lupanga” m’njira imeneyi, tidzakhala osangalatsa kwambiri kwa Yehova Mulungu ndipo tidzakhala pa mtendere koposa ndi ena ndi ife eni.
Mbali yomalizira inasonyeza kuti Mawu a Mulungu Ngamoyo chifukwa “Amalimbikitsa ndi Kufulumiza Mtima Wathu.” M’Baibulo, liwu lakuti “mtima” limagwiritsiridwa ntchito mwachisawawa mophiphiritsira ndipo limalozera ku munthu wa mkati wosonyezedwa m’malingaliro athu ndi mtundu wa maganizo. Mawu a Mulungu amalimbitsa mtima wathu mwa kuvumbulutsa mikhalidwe yake yozizwitsa kupyolera m’zochita zake ndi mtundu wa anthu. Chikondi chopanda dyera cha Mulungu chimatifulumiza ife kumtsanzira iye. M’ndemanga zake zomalizira, mlankhuliyo anabwereramo m’mbiri ya Watch Tower Society ya kufalitsa maBaibulo ndipo anasangalatsa gulu mwa kulengeza kusindikizidwa kokhoza kuika m’thumba kwa New World Translation ya chikuto chofewa.
“Khulupirira Yehova Ndi Mtima Wako Wonse”
Mutuwu kaamba ka Sande, wotengedwa pa Miyambo 3:5, unalingaliridwa ndi mkulu yemwe anatsegula programu ndi kukambitsirana kwa lemba la tsiku. Kenaka panabwera nkhani yofufuza moyo “Kodi Mumatenga Zinthu Zopatulika Mosasamala?” Dziko limadzimva kuti liribe mangawa aliwonse kwa Mulungu, koma monga Mboni za Yehova, timadziŵa kuti kuti tipeze chivomerezo chake, tiyenera kutsanzira amuna akale okhulupirika mwakusonyeza chiyamikiro kaamba ka zinthu zopatulika. Mlankhuliyo anakambitsirana 13 za izi, pakati pa zimene pali dzina la Yehova, Mawu ake, mzimu wake woyera, malamulo ake, gulu lake lowoneka ndi maso, unansi wathu ndi Mulungu, misonkhano yathu, ndi mwaŵi wathu wa utumiki. Ngati ife mowonadi timayamikira zinthu zopatulika zimenezi, tidzaiika izo m’malo oyamba mu miyoyo yathu kukhululupirira Yehova kotheratu, ndipo kufupidwa ndi iye.
Kenaka inabwera nkhani yotokosa “Danani Nayo Kotheratu Njira Yochititsa Manyazi ya Dziko.” Chifukwa cha kusabisira mawu kwake, inatulutsa ndemanga zonga ngati, “Kokha chimene timachifunadi!” Popeza kuipa kwakhala kofala, Akristu ayenera kudzichinjiriza motsutsana ndi kulekerera mkhalidwe woipa wa chisembwere ndi chiwawa. (2 Timoteo 3:1-5) Chotero, sitiyenera kuwonera kapena kumvetsera ku zowulutsidwa zoterozo pa TV kapena pa wailesi ndiponso sitiyenera kuŵerenga ponena za izo m’manyuzipepala. Ndithudi, sitifuna nkomwe kulingalira ponena za izo. ‘Akristu enieni omwe amakhumba kusunga unansi wabwino ndi Yehova sangakhale ndi chinachake chochita ndi zinthu za maliseke,’ ayi, osati mpang’ono pomwe!
Programu ya Sande m’mawa inatha ndi chitsanzo cha Baibulo chogwira maganizo “Yehova Amapulumutsa Awo Oitanira pa Dzina Lake.” Icho chinachita ndi zochitika zambiri m’moyo wa Yoswa. M’chenicheni, icho chinasonyeza mmene nzika za Yeriko zinawonera kuyenda kwa amuna ankhondo a Israyeli mozungulira mzinda tsiku ndi tsiku. Ndiponso chowunikiridwa chinali chikhulupiriro chachikulu cha Rahabi, chomwe chinatulukamo m’kupulumutsidwa kwake ndi banja lake. Pomaliza, onse anafunsidwa kuti: ‘Kodi muli ndi chikhulupiriro cholimba ndi chidaliro chonga cha Yoswa ndi anzake amphamvu? Ngati ndi tero, tingayembekezere kugawana m’chipambano chomalizira cha Yehova pa adani ake.’
Mbali yapoyera ya Msonkhano wa Chigawo wa “Khulupirirani Yehova” inabwera ndi nkhani yokhala ndi mutu wakuti “M’nthaŵi Zathu Zowopsya, Kodi Ndani Amene Mungakhulupirire Kwenikweni?” Inawonetsa bwino nsonga yakuti mtundu wa anthu mopanda thandizo ukufuna magwero a chikhulupiriro! Mwachimvekere, iyo inasonyeza kupusa kwa kukhulupirira anthu. Chotero, Mawu a Mulungu amatipatsa ife uphungu wa kukhulupirira Yehova ndipo amatipatsa ife zifukwa zamphamvu za kuchitira tero. Tiyenera kukhulupirira iye chifukwa cha mikhalidwe yake ndi mbiri yake m’kupulumutsa awo amene anakhulupirira iye, Mfumu Hezekiya akumakhala chitsanzo chabwino koposa. Mwamsanga chipulumutso chofananacho chidzakumanizidwa ndi awo amene njira yawo ya kachitidwe imachitira chitsanzo kukhulupirira Yehova.
“Pitirizani ‘Kukhala Mwamtendere’” unali mutu wa nkhani imene mwamsanga inatsatirapo. Kukhala mwamtendere kumatanthauza kumapititsa patsogolo mtendere mokangalika. Kumatanthauzanso kukhala pa mtendere ndi ife eni chifukwa cha kukhala ndi chikumbumtima chabwino. Mwakusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu, makamaka chikondi ndi kudziletsa, tidzakhala okhoza kukhala mwamtendere ndi mabanja athu ndi abale ndi alongo mu mpingo.
Palibe chikaikiro ponena za nsonga yakuti msonkhano umenewu unatikonzekeretsa tonsefe “Kuyang’ana Kutsogolo ndi Chikhulupiriro Chotheratu mwa Yehova,” mutu wa nkhani yomalizira. Iyo inafupikitsa bwino chotani nanga programuyo! Mlankhuliyo anagogomezera kuti tsiku ndi tsiku timafunikira kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse, kumlemekeza iye m’njira zathu zonse, ndi kumlola iye kuwongolera mayendedwe athu. (Miyambo 3:5, 6) Osonkhanawo anayamikira mokulira kumva ponena za nkhani za poyera 16 zatsopano, makaseti a Nsanja ya Olonda, (Chingelezi) ndi kusindikizidwanso kwa nkhani ya mwazi yomwe inawoneka mu Galamukani! ndipo kuti idzakhalako kaamba ka ife kuti tiipereke kwa adokotala athu. Inde, ndipo tinasangalatsidwa kumva ponena za kutulutsidwa kwa kaseti ya chitsanzo cha Baibulo ina, ndi kusindikizidwanso kwa mavolyumu akulu a Nsanja ya Olonda (1960-79) (Chingelezi), ndi kufalitsidwa kwa matrakiti ena atatu!
Onse opezekapo pa Msonkhano wa Chigawo wa “Khulupirirani Yehova” analimbikitsidwa mwauzimu. Iwo tsopano ali okonzekera kuyang’anizana ndi mtsogolo ndi chidaliro chotheratu mwa Atate wawo wa kumwamba. Ndipo onse moyenerera analimbikitsidwa ndi uphungu womalizira: “Pamene tiyang’anizana ndi mtsogolo, lolani kuti tonsefe mogwirizana titsimikizire mwanjira yathu ya moyo kuti ‘timakhulupirira Yehova.’”
[Tchati patsamba 26]
Misonkhano ya Chigawo Yosiyanasiyana ya “Khulupirirani Yehova”
Opezekapo Obatizidwa
Austria 24,686 360
Brazil 442,731 7,626
British Isles 156,417 1,225
Colombia 82,321 1,852
Denmark 23,029 200
Federal Republic of
Germany 159,361 1,455
Finland 26,144 284
France 138,683 2,705
Hong Kong 2,661 49
Ireland 4,326 61
Italy 221,227 5,496
Jamaica 18,540 184
Japan 232,904 3,416
Korea 82,296 2,013
Malaysia 1,154 15
Norway 12,703 218
Portugal 55,057 1,074
Puerto Rico 49,953 377
Spain 105,591 2,394
Sweden 30,099 312
Switzerland 19,459 261
Trinidad 10,649 132
United States 1,288,313 13,562
Venezuela 100,777 1,664
Zimbabwe 45,544 580
[Zithunzi patsamba 25]
Zitsanzo zodzutsa malingaliro zinawunikira kufunika kwa kukhulupirira Yehova
F. W. Franz, chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, akupereka nkhani ku gulu lopezeka pa msonkhano lopereka chisamaliro chomvetsera
[Chithunzi patsamba 26]
Ambiri anasonyeza kukhulupirira Yehova mwa kubatizidwa kuchitira chitsanzo kudzipereka kwawo kwa iye