Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/1 tsamba 30-31
  • Mukuitanidwa ku Misonkhano ya Chigawo ya “Chilungamo Chaumulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mukuitanidwa ku Misonkhano ya Chigawo ya “Chilungamo Chaumulungu”
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
    Yandikirani Yehova
  • Chilungamo Chaumulungu—Chochititsa Kaamba ka Kusangalala!
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/1 tsamba 30-31

Mukuitanidwa ku Misonkhano ya Chigawo ya “Chilungamo Chaumulungu”

NDI Mpatsi Wamkulu chotani nanga mmene Mlengi wathu wachikondi Yehova Mulungu, aliri! Zowona, “mphatso iriyonse yabwino, ndi chininkho” zimachokera kwa iye. (Yakobo 1:17) Moyenerera, mu Salmo 136 timaŵerenga nthaŵi 26 kalongosoledwe kakuti: “Pakuti chifundo chake nchosatha.”

Pakati pa mphatso zake zambiri zauzimu kaamba ka anthu ake akale panali mapwando atatu a pa chaka: Paskha ndi Madyerero a Mkate Wopanda chotupitsa; Madyerero a Milungu, kapena Pentekoste; ndi Madyerero a Misasa, kapena Kusonkhanitsa. Mapwando atatu amenewa ankawonedwa ndi chiyembekezero chokulira, popeza kuti onsewo anali omangilira mwauzimu ndi nthaŵi za chisangalalo chokulira.​—Levitiko 23:40-43.

M’nthaŵi zamakono, Yehova Mulungu waika m’mitima ya atumiki ake chofananacho mwakukhala ndi mapwando atatu auzimu pa chaka: tsiku la msonkhano wapadera, msonkhano wadera wa masiku aŵiri, ndi msonkhano wa chigawo wa masiku atatu kapena anayi. Imeneyi imatumikiranso monga nyengo ya kumangilira kwauzimu ndi kuyanjana kosangalatsa. Mogwirizana ndi maripoti olandiridwa pa nthaŵi ya kulembaku, 6,128,388 anapezekapo pa Misonkhano Yachigawo ya “Khulupirirani Yehova” yomwe inayamba mu June 1987, ndipo 85,091 anabatizidwa. Chaka chino Mboni iriyonse ikuyang’ana kutsogolo kukapezekako ku Msonkhano wa Chigawo wa “Chilungamo Chaumulungu”.

Ndi mutu wokulira ndi wanzeru chotani nanga mmene “Chilungamo Chaumulungu” uliri! Ndipo uli wofunika chotani nanga! Nkulekelanji, popeza ngakhale anthu opanda ungwiro amapereka utumiki wa pakamwa ku kufunika kwa chilungamo. Chimenecho ndicho chifukwa chake okonza a Lamulo la ku United States zaka 200 zapitazo anapereka osati kokha kaamba ka nthambi za boma za nduna zolamulira ndi za lamulo komanso kaamba ka zowona pa chilungamo kotero kuti zochititsa chilungamo zisungidwe. Komabe, mazana ochulukira chimenecho chisadakhale, Yehova Mulungu iyemwini anapereka kaamba ka magawo atatu a boma, onse omwe amayang’aniridwa ndi iye. Chotero, pa Yesaya 33:22 timaŵerenga kuti: “Yehova ndiye Woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa Malamulo, Yehova ndiye Mfumu yathu.”

M’chenicheni, tikuuzidwa kuti chilungamo chiri chotsirizira, chonulirapo, kapena chofunika cha boma. Koma pamene tikulingalira lamulo lofunika limeneli, pamene chidza ku kuchigwiritsira icho ntchito, ndi kuphophonya kotani nanga kumene anthu adyera ndi opanda ungwiro amachita! Mitundu yonse ya tsankho la ufuko, mtundu, ndi chipembedzo ziri kokha zitsanzo zochulukira za kuswa chilungamo. Ndipo kulinso tero kugwiritsira ntchito kolakwa konse kwa mphamvu, kaya kodzetsedwa ndi maboma, makampani, mabungwe a zipembedzo, kapena aliyense payekha.

Tingakhale achiyamikiro chotani nanga kuti Mawu a Mulungu amatitsimikizira ife za kugonjetsa kotheratu kwa chilungamo ndi ubwino popeza kuti Yehova ali mokulira Mulungu wa chilungamo! Chimenecho ndicho chifukwa chake Mose anaimba kwa iye kuti: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndi wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Yehova Mulungu ali ndi kulemekeza kotero kwa chilungamo kotero kuti iye anapereka Mwana wake wobadwa yekha monga nsembe kuti iye akakhoze kubweretsa moyo wosatha ku mtundu wa anthu omvera. (Aroma 3:25, 26) Molondola, Yehova amayanjana ndi awo omwe ali okonda chilungamo ndi ubwino, ngakhale monga mmene timaŵerengera pa Masalmo 11:7: “Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; wowongoka mtima adzapenya nkhope yake.” Molingana ndi kutembenuza kwina, iye ali “wachilungamo ndipo amakonda kachitidwe ka chilungamo.”​—The New English Bible.a

Msonkhano wathu wa Chigawo wa “Chilungamo Chaumulungu” udzalimbikitsa chikhulupiriro chathu mu chilungamo chogonjetsa kotheratu. Chidzalimbikitsanso kugamulapo kwathu panthaŵi zonse ndi pansi pa mikhalidwe iriyonse kulabadira lamulo la pa Mika 6:8 la “kuchita chilungamo.” Ichi chiri chitokoso chenicheni titalingalira chikhoterero chathu chobadwa nacho ndi ziyeso zodzetsedwa ndi dziko ladyera lotizungulira.

M’malo ambiri, msonkhano udzayamba pa Lachinayi masana, ndipo tsiku lirilonse lidzawonetsa mutu woyenerera, mutu wa tsiku loyambirira ukumakhala “Achimwemwe Ali Awo Ochita Chilungamo,” wozikidwa pa Masalmo 106:3, NW. Nkhani yaikulu idzawunikira kuti chilungamo chimazindikiritsa njira zonse za Mulungu, ndipo idzatsatiridwa ndi maripoti kuchokera ku osunga chilungamo a nthaŵi zonse, onga ngati amishonale kuchokera ku maiko achilendo.

“Landirani Mwambo Womwe Umapereka Chidziŵitso” (wozikidwa pa Miyambo 1:3) uli mutu wa pa Lachisanu. Patsikuli, nkhani zosiyana ziŵiri zidzagogomezera kufunika kwa kupereka chilango ndi kulandira chilango. Chitsanzo chamakono, “Kuikidwa Chizindikiro kaamba ka Chipulumuko,” chidzasonyeza kufunika kwa kudziŵika monga mmodzi wa atumiki a Yehova. Programu ya tsikulo idzatha ndi uphungu wabwino kwambiri wa “Kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka Chidziŵitso.”

Wotsimikizira uli mutu wa tsiku lachitatu, Loŵeruka: “Ziweruzo Zake Ziri Zowona ndi Zolungama,” wotengedwa pa Chivumbulutso 19:2. Yoperekedwa m’mawa iri nkhani yakuti “Ubatizo Womwe Umatsogolera ku Chiweruzo Chabwino.” Programu ya madzulo idzayamba ndi nkhani yosiirana yomwe idzapereka uphungu kwa akulu wa “Kutumikira kaamba ka Chilungamo Chenichenicho.” Iyi idzatsatiridwa ndi nkhani ina yosiirana, yokhala ndi mutu wakuti “Nthaŵi Yoikika Iri Pafupi,” yochita ndi maulosi a m’Malemba Achikristu a Chigriki omwe amaneneratu za kugonjetsa kwa chilungamo.

Sande, tsiku lachinayi ndi lotsirizira la msonkhanowo, liri ndi mutu wake wakuti “Chilungamo​—Chilungamo Ndicho M’dzichitsata.” (Deuteronomo 16:20) Chapadera m’programu ya m’mawa chiri chitsanzo chabwino kwambiri ndi cha panthaŵi yake cha m’Baibulo chakuti “Ziweruzo za Yehova Molimbana ndi Anthu Onyalanyaza Lamulo.” Uthenga wotonthoza mowona kaamba ka okonda chilungamo onse udzapezeka m’nkhani ya Baibulo ya madzulo, “Chilungamo kaamba ka Onse ndi Woweruza Woikidwa ndi Mulungu.” Onse adzapeza mapindu ochulukira kuchokera m’nkhaniyi ngati choyamba adzizoloŵeretsa iwo eni ndi Machitidwe mutu 17. Moyenerera, m’nkhani yotsirizira, opezekapo onse adzalangizidwa, “Pitirizani Kutsatira Chilungamo Pamene Mapeto Ayandikira.”

Ndithudi, phwando lolemerera mwauzimu likuyembekezera onse omwe adzapezeka pa umodzi wa Misonkhano ya Chigawo ya “Chilungamo Chaumulungu.” Chotero idzani ndi chilakolako chabwino chauzimu, odera nkhaŵa kotheratu za kusowa kwanu kwauzimu. Sonyezani kuyamikira kofananako kaamba ka gome la Yehova komwe mumasonyeza pamene mupezeka pa misonkhano ya mpingo ya kwanuko​—mwanjira imene mumapesera tsitsi, mwakufika msanga programu isanayambe, ndipo mwakukhala kaamba ka pemphero lothera la tsiku lirilonse. Perekani chisamaliro chofunika ku mbali iriyonse ya programu. Lembani nsonga; izi sizidzakupatsani kokha chinachake chokumbukirira msonkhano koma zidzakuthandizaninso kusumika maganizo pa nsongazo pamene zikuperekedwa.

Ndipo lolani kuti tisanyalanyaze lamulo lomwe linalongosoledwa ndi Yesu ndipo lolembedwa pa Machitidwe 20:35: “Muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa chimene chiri m’kulandira.” Chotero chitani mbali yanu kuthandiza kugwira ntchito kwa msonkhano bwino lomwe ndi mwataŵataŵa. Ndipo khalani ogalamuka nthaŵi zonse ku mwaŵi wa kuchitira umboni wa mwamwaŵi. Khalani odera nkhaŵa mwapadera ponena za ichi popeza kuti palibe nthaŵi yomwe yaikidwa pambali kaamba ka kuchitira umboni wa kunyumba ndi nyumba mkati mwa msonkhano. M’njira zonse zoterezi, inu mungasonyeze kuti mulidi wopenyerera wachimwemwe wa chilungamo.

Mungafunse Mboni za Yehova za kumaloko kaamba ka malo osonkhanirako omwe ali kufupi ndi inu

[Mawu a M’munsi]

a Kwakukulukulu, palibe kusiyana pakati pa chilungamo ndi ubwino, ngakhale kuti chilungamo kaŵirikaŵiri chiri ndi kugwirizana kwa lamulo.​—Yerekezani ndi 2 Timoteo 2:22; Yakobo 1:20, New World Translation ndi The New English Bible.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena