Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 8/1 tsamba 12-17
  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wachilungamo Komanso Wachifundo
  • Chilungamitso Chimodzi Chopulumutsa Anthu
  • Funafunani Chilungamo ndi Kuchilondola
  • “Akalonga a Chilungamo”
  • Sungani Chilungamo ndi Kuchichita
  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Yehova Wokonda Chilungamo ndi Chiweruzo
    Nsanja ya Olonda—1996
  • ‘Muzichita Chilungamo’ Poyenda ndi Mulungu
    Yandikirani Yehova
  • “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 8/1 tsamba 12-17

Tsanzirani Yehova​—Chitani Chilungamo

“Ndine Yehova, Amene ndikuchita zokoma mtima ndi chilungamo m’dziko lapansi; pakuti zinthu zimenezi ndikondwera nazo.”​—YEREMIYA 9:24, NW.

1. Kodi nchiyembekezo chosangalatsa kwambiri chiti chimene Yehova anapereka?

YEHOVA analonjeza kuti tsiku lidzafika pamene aliyense adzamdziŵa. Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, iye anati: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Chimenecho nchiyembekezo chosangalatsa chotani nanga!

2. Kodi kudziŵa Yehova kumaphatikizaponji? Chifukwa ninji?

2 Koma kodi kudziŵa Yehova kumatanthauzanji? Yehova anavumbulira Yeremiya chimene chili chofunika koposa kuti: “Kuzindikira ndi kundidziŵa, kuti ndine Yehova, Amene ndikuchita zokoma mtima ndi chilungamo m’dziko lapansi; pakuti zinthu zimenezi ndikondwera nazo.” (Yeremiya 9:24, NW) Choncho, kudziŵa Yehova kumaphatikizapo kudziŵa mmene amachitira chilungamo. Ngati ifeyo kenako titsatira mikhalidwe imeneyo, iye adzakondwera nafe. Kodi tingaitsatire motani? M’mawu ake, Baibulo, Yehova wasunga mbiri ya zimene anachita ndi anthu opanda ungwiro m’mibadwo yapitayo. Mwa kuphunzira mbiriyo, tingafike pakudziŵa njira ya Yehova ya chilungamo ndi kumtsanzira.​—Aroma 15:4.

Wachilungamo Komanso Wachifundo

3, 4. Kodi nchifukwa chiyani Yehova anali ndi chifukwa chabwino chowonongera Sodomu ndi Gomora?

3 Chiweruzo cha Mulungu pa Sodomu ndi Gomora chili chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza mbali zosiyanasiyana za chilungamo cha Yehova. Yehova sanapereke chilango choyenerera chokha koma anaperekanso chipulumutso kwa oyenerera. Kodi panalidi chifukwa chabwino chowonongera mizindayo? Abrahamu, amene mwachionekere sanali kudziŵa za kuipa konse kwa Sodomu, anaganiza mosiyanako poyamba. Yehova anatsimikizira Abrahamu kuti ngati mudzangopezeka anthu khumi olungama, iye sadzawononga mzindawo. Ndithudi, chilungamo cha Yehova si chamtima wapachala kapena chopanda chifundo.​—Genesis 18:20-32.

4 Umboni wa khalidwe loipa la Sodomu unaonekera bwino kwambiri pamene angelo aŵiri anapita kukafufuza mzindawo. Pamene amuna a mumzindawo, “anyamata ndi okalamba,” anamva kuti amuna aŵiri abwera kudzakhala kunyumba kwa Loti, gulu la amunawo linazinga nyumba yake moukira ncholinga chogwirira amuna aŵiriwo ndi kuchita nawo mathanyula. Kuipa kwawo kunali kutafikadi pamlingo wosaneneka! Mosakayikira konse, chiweruzo cha Yehova pamzindawo chinali cholungama.​—Genesis 19:1-5, 24, 25.

5. Kodi ndi motani mmene Mulungu analanditsira Loti ndi banja lake mu Sodomu?

5 Atatchula za kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora monga chitsanzo chochenjeza, mtumwi Petro analemba kuti: “Ambuye adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo.” (2 Petro 2:6-9) Sichikanakhala chilungamo ngati Loti wokhulupirikayo ndi banja lake akanawonongedwera pamodzi ndi anthu osaopa Mulungu a m’Sodomu. Choncho, angelo a Yehova anachenjeza Loti za chiwonongeko choyandikiracho. Pamene Loti anachedwa kunyamuka, angelowo “chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova” anagwira dzanja lake, la mkazi wake, ndi manja a ana ake aŵiri aakazi ndi kuwatulutsa mumzindawo. (Genesis 19:12-16) Tingatsimikize kuti Yehova adzasonyeza kusamala kofananako kwa anthu olungama pachiwonongeko chikudzacho cha dongosolo loipali.

6. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kudera nkhaŵa mopambanitsa za chiwonongeko chikudzachi cha dongosolo loipa la zinthu?

6 Ngakhale kuti mapeto a dongosolo lino la zinthu idzakhala nthaŵi ‘yakubwezera,’ ifeyo tilibe chifukwa chodera nkhaŵa mopambanitsa. (Luka 21:22) Chiweruzo chimene Mulungu adzapereka pa Armagedo chidzakhala ‘cholungama konsekonse.’ (Salmo 19:9) Monga momwe Abrahamu anazindikirira, anthufe tingadalire chilungamo cha Yehova kotheratu, chimene chili chapamwamba kwambiri kuposa chathu. Abrahamu anafunsa kuti: “Kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi?” (Genesis 18:25; yerekezerani ndi Yobu 34:10.) Kapena monga momwe Yesaya anafotokozerera bwino kuti, ‘ndani aphunzitsa [Yehova] njira ya chilungamo?’​—Yesaya 40:14, NW.

Chilungamitso Chimodzi Chopulumutsa Anthu

7. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chilungamo cha Mulungu ndi chifundo chake?

7 Chilungamo cha Mulungu sichimangoonekera ndi mmene amalangira olakwa. Yehova amadzinenera kuti ndi “Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi.” (Yesaya 45:21) Nzodziŵikiratu kuti pali kugwirizana kwakukulu pakati pa chilungamo cha Mulungu ndi chikhumbo chake chopulumutsa anthu kuzotsatirapo zauchimo. Pothirira ndemanga lembalo, The International Standard Bible Encyclopedia, 1982 Edition, imafotokoza kuti “chilungamo cha Mulungu chimafuna njira zothandiza zosonyezera chifundo Chake ndi kukwaniritsa chipulumutso Chake.” Si kuti chilungamo cha Mulungu chimasinthidwa ndi chifundo koma, m’malo mwake, chifundo chimasonyeza chilungamo cha Mulungu. Makonzedwe a Mulungu a dipo lopulumutsira mtundu wa anthu ndiwo chitsanzo chapadera kwambiri cha mbali imeneyi ya chilungamo cha Mulungu.

8, 9. (a) Kodi mawu akuti, “chilungamitso chimodzi” anaphatikizapo chiyani? Chifukwa ninji? (b) Kodi Yehova amafunanji kwa ife?

8 Mtengo wa dipo weniweniwo​—moyo wamtengo wapatali wa Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, Yesu Kristu​—unali waukulu kwambiri chifukwa chakuti malamulo a Yehova amakhudza chilengedwe chonse, ndipo ngakhale iyeyo amawatsatira. (Mateyu 20:28) Moyo wangwiro, wa Adamu, unatayika, choncho panafunika moyo wina wangwiro kuti upulumutse moyo wa mbadwa za Adamu. (Aroma 5:19-21) Mtumwi Paulo anafotokoza njira ya Yesu ya kukhulupirika, kuphatikizapo kulipira dipo, kukhala “chilungamitso chimodzi.” (Aroma 5:18) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti malinga ndi kaonedwe ka Yehova, kuwombola mtundu wa anthu kunali chinthu cholondola ndiponso choyenerera kuchichita, ngakhale kuti anayenera kutayirapo zinthu zambiri. Mbadwa za Adamu zinali monga “bango lophwanyika,” limene Mulungu sanafune kulithyola, kapena monga “nyali yofuka,” imene sanafune kuizima. (Mateyu 12:20) Mulungu anali ndi chidaliro chakuti pakati pa mbadwa za Adamu padzakhala amuna ndi akazi ambiri okhulupirika.​—Yerekezerani ndi Mateyu 25:34.

9 Kodi chikondi ndi chilungamo chachikulu chimenechi cha Mulungu tiyenera kutani nacho? Chimodzi mwa zinthu zimene Yehova amafuna kwa ife ndicho ‘kuchita cholungama.’ (Mika 6:8) Kodi tingachichite motani?

Funafunani Chilungamo ndi Kuchilondola

10. (a) Kodi njira imodzi imene timachitira chilungamo ndi iti? (b) Kodi ndi motani mmene tingafunire choyamba chilungamo cha Mulungu?

10 Choyamba, tiyenera kutsatira malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino. Chifukwa chakuti malamulo a Mulungu ngolungama, timachita chilungamo pamene tiwatsatira. Ndizo zimene Yehova amayembekezera anthu ake kuchita. “Phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo [“chilungamo,” NW],” Yehova anawauza motero Aisrayeli. (Yesaya 1:17) Yesu anaperekanso uphungu wofananawo kwa omvetsera ake pa Ulaliki wake wa pa Phiri, pamene anawalangiza kuti ‘athange afuna Ufumu ndi chilungamo cha Mulungu.’ (Mateyu 6:33) Paulo analimbikitsa Timoteo kuti ‘atsate chilungamo.’ (1 Timoteo 6:11) Pamene titsatira malamulo a Mulungu a khalidwe ndi kuvala umunthu watsopano, ndiye kuti tikulondola chilungamo chenicheni. (Aefeso 4:23, 24) M’mawu ena, timafunafuna chilungamo mwa kuchita zinthu m’njira ya Mulungu.

11. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulimbana ndi mphamvu ya uchimo, ndipo kodi tingalimbane nayo motani?

11 Monga momwe tikudziŵira, nthaŵi zina nkovuta kuti anthu opanda ungwiro achite cholondola ndi choyenerera. (Aroma 7:14-20) Paulo analimbikitsa Akristu a ku Roma kuti alimbane ndi mphamvu ya uchimo, kotero kuti apereke matupi awo kwa Mulungu monga “ziŵalo . . . za chilungamo,” zimene Mulungu angazigwiritsire ntchito pokwaniritsa cholinga chake. (Aroma 6:12-14) Ndiponso, mwa kuphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse ndi kuwatsatira, tingadziŵe ‘maleredwe a Ambuye’ ndi kukhala ‘olangizidwa m’chilungamo.’​—Aefeso 6:4; 2 Timoteo 3:16, 17.

12. Kodi tiyenera kupeŵanji ngati tikufuna kuchitira ena zimene tikufuna kuti Yehova atichitire?

12 Chachiŵiri, timachita chilungamo pamene tichitira ena zimene tikufuna kuti Yehova atichitire. Nkosavuta kukhala ndi moyo wapaŵiri​—wodzilekerera koma wosalolera ena. Timafulumira kudzikhululukira pazolakwa zathu, koma timafulumira kudzudzula ena chifukwa cha zophophonya zawo, zimene mwina zingakhale zazing’ono kwambiri poziyerekezera ndi zathu. Yesu anafunsa momveka kuti: “Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwemwini suuganizira?” (Mateyu 7:1-3) Sitiyenera kuiŵala kuti palibe aliyense wa ife amene akanakhalabe ndi moyo ngati Yehova anali kusunga zolakwa zathu. (Salmo 130:3, 4) Ngati Yehova amanyalanyaza zofooka za abale athu chifukwa cha chilungamo chake, ifeyo ndife ndani kuti tiwaweruze mopanda chifundo?​—Aroma 14:4, 10.

13. Kodi nchifukwa ninji munthu wolungama amadzimva kuti ayenera kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu?

13 Chachitatu, timasonyeza chilungamo cha Mulungu pamene tichita ntchito yolalikira mwakhama. “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino,” akutilangiza motero Yehova. (Miyambo 3:27) Sikungakhale kolondola ngati sitigaŵira ena chidziŵitso chopatsa moyo chimene Mulungu watipatsa mooloŵa manja. Nzoona kuti anthu ambiri angakane uthenga wathu, koma malinga ngati Mulungu akuwasonyezabe chifundo, tiyenera kukhala ofunitsitsa kuwapatsa mpata wakuti “afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Ndiponso monga Yesu, timakondwera pamene tathandiza wina kutembenukira kuchilungamo. (Luka 15:7) Inoyi ndiyo nthaŵi yabwino yoti ‘tibzale m’chilungamo.’​—Hoseya 10:12.

“Akalonga a Chilungamo”

14. Kodi akulu amachita mbali yotani ponena za chilungamo?

14 Tonsefe tiyenera kuyenda m’mabande a chilungamo, koma akulu mumpingo wachikristu ali ndi udindo wapadera pankhaniyi. Ulamuliro wa Yesu ‘ukuchirikizidwa ndi chilungamo.’ Choncho, akulu amatsatira chilungamo cha Mulungu. (Yesaya 9:7) Iwo amakumbukira zofotokozedwa mwaulosi pa Yesaya 32:1 kuti: “Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo [“adzalamulira monga akalonga a chilungamo,” NW].” Pokhala oyang’anira oikidwa ndi mzimu, kapena kuti ‘adindo a Mulungu,’ akulu ayenera kuchita zinthu m’njira ya Mulungu.​—Tito 1:7.

15, 16. (a) Kodi akulu amatsanzira motani mbusa wokhulupirika wa m’fanizo la Yesu? (b) Kodi akulu amamva motani ponena za otayika mwauzimu?

15 Yesu anasonyeza kuti chilungamo cha Yehova nchachifundo ndiponso chololera. Kwenikweni, iye anayesa kuthandiza awo amene anali ndi mavuto ndi “kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.” (Luka 19:10) Monga mbusa wa m’fanizo la Yesu amene anafunafuna nkhosa yotayika mosatopa, akulu amafunafuna awo amene atayika mwauzimu ndi kuyesayesa kuwatsogoleranso ku gulu.​—Mateyu 18:12, 13.

16 M’malo motsutsa awo amene mwina anachita machimo aakulu, akulu amafuna kuwachiritsa ndi kuwatsogolera ku kulapa ngati zimenezo nzotheka. Iwo amakondwera ngati athandiza munthu wotayika. Komabe, iwo amachita chisoni ngati wochimwa safuna kulapa. Pamenepo malamulo olungama a Mulungu amafuna kuti iwo amchotse wochimwa wosalapayo. Ngakhale zitatero, monga atate wa mwana woloŵerera, iwo amalakalaka kuti tsiku lina wochimwayo ‘adzazindikire.’ (Luka 15:17, 18, NW) Choncho, akulu amachitapo kanthu kuchezera ochotsedwa ena kukawakumbutsa mmene angabwererenso ku gulu la Yehova.a

17. Posamalira nkhani ya munthu amene walakwa, kodi akulu amakhala ndi cholinga chotani, ndipo kodi ndi mkhalidwe wotani umene udzawathandiza kukwaniritsa cholinga chimenecho?

17 Akulu ayenera kutsanzira chilungamo cha Yehova makamaka posamalira nkhani za munthu amene walakwa. Ochimwa “analikumyandikira” Yesu chifukwa anaona kuti adzawamvetsetsa ndi kuwathandiza. (Luka 15:1; Mateyu 9:12, 13) Koma si kuti Yesu anali kulekerera zolakwa. Kudya chakudya kamodzi ndi Yesu kunasonkhezera Zakeyu, wolanda mwaukathyali wodziŵika bwino, kuti alape ndi kubwezera kwa eni ake zonse zimene anawalanda. (Luka 19:8-10) Akulu lerolino alinso ndi cholinga chimodzimodzicho poweruza milandu​—kuthandiza wolakwa kuti alape. Ngati ali ofikirika monga mmene Yesu analili, olakwa ambiri sadzavutika kuwapempha thandizo.

18. Kodi nchiyani chidzachititsa akulu kukhala monga “pobisalira mphepo”?

18 Mtima watcheru udzathandiza akulu kuchita chilungamo cha Mulungu, chimene sichili chaukali kapena chopanda chifundo. Chochititsa chidwi nchakuti Ezara anakonzekeretsa mtima wake, osati maganizo ake okha, kuti aphunzitse Aisrayeli chilungamo. (Ezara 7:10) Mtima womvetsa udzathandiza akulu kugwiritsira ntchito mapulinsipulo oyenerera a m’Malemba ndi kulingalira za mikhalidwe ya munthu aliyense. Pamene Yesu anachiritsa mkazi amene anali kukha mwazi, iye anasonyeza kuti chilungamo cha Yehova chimatanthauza kumvetsa mzimu wa chilamulo limodzinso ndi malemba ake. (Luka 8:43-48) Akulu amene amachita chilungamo mwachifundo tingawayerekezere ndi “pobisalira mphepo” kwa awo amene akanthidwa ndi zofooka zawo kapena ndi dongosolo loipali limene tikukhalamo.​—Yesaya 32:2.

19. Kodi mlongo wina anachita motani atakhudzidwa ndi chilungamo cha Mulungu?

19 Mlongo wina amene anachita tchimo lalikulu anaona chilungamo cha Mulungu mwachindunji. “Kunena zoona, ndinaopa kupita kwa akulu,” akuvomereza motero. “Koma iwo anandisonyeza chifundo ndi ulemu. Akuluwo anali ngati atate anga ndipo osati monga oweruza ouma mtima. Iwo anandithandiza kumvetsa kuti Yehova sadzandikana ngati ndatsimikiza mtima kuwongolera njira zanga. Ndinaona mwachindunji mmene amatilangira monga momwe Atate wachikondi amachitira. Ndinatsegula mtima wanga kwa Yehova, ndi chidaliro chakuti adzamva mapemphero anga. Ndikamakumbukira, ndinganenedi kuti kuonana ndi akulu zaka zisanu ndi ziŵiri zapitazo kunali dalitso la Yehova. Kuyambira pamenepo, unansi wanga ndi iye wakhala wolimba kwambiri.”

Sungani Chilungamo ndi Kuchichita

20. Kodi mapindu a kumvetsa ndi kuchita chilungamo ngotani?

20 Zilidi bwino kuti chilungamo cha Mulungu chimaloŵetsapo zambiri kuposa kungopatsa munthu aliyense chomuyenerera. Chilungamo cha Yehova chamsonkhezera kupereka moyo wosatha kwa awo amene akusonyeza chikhulupiriro. (Salmo 103:10; Aroma 5:15, 18) Mulungu akuchita nafe motere chifukwa chakuti pochita chilungamo chake amalingalira za mikhalidwe yathu, ndipo amafuna kupulumutsa osati kutsutsa. Ndithudi, kumvetsetsa ukulu wa chilungamo cha Yehova kumatiyandikizitsa kwa iye. Ndipo pamene tiyesetsa kutsanzira mbali imeneyi ya umunthu wake, moyo wathu ndi wa ena udzadalitsidwa kwambiri. Atate wathu wakumwamba adzaona kuti tikulondola chilungamo. Yehova akutilonjeza kuti: “Sungani chilungamo, anthu inu, ndi kuchichita. Pakuti chipulumutso changa chili pafupi kudza, ndi chilungamo changa chili pafupi kuvumbulutsidwa. Wachimwemwe ndi munthu amene achita ichi.”​—Yesaya 56:1, 2, NW.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Nsanja ya Olonda, April 15, 1991, masamba 22-3.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora kukutiphunzitsanji ponena za chilungamo cha Yehova?

◻ Kodi nchifukwa ninji dipo lili mbali yapadera kwambiri yosonyeza chilungamo ndi chikondi cha Mulungu?

◻ Kodi tingachite chilungamo m’njira zitatu ziti?

◻ Kodi akulu angatsanzire chilungamo cha Mulungu m’njira yapadera iti?

[Zithunzi patsamba 15]

Mwa ntchito yathu yolalikira, timasonyeza chilungamo cha Mulungu

[Chithunzi patsamba 16]

Pamene akulu asonyeza chilungamo cha Mulungu, awo amene ali ndi mavuto savutika kuwapempha thandizo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena