Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 8/1 tsamba 16-20
  • Achichepere Dzichinjirizeni Molimbana ndi Kutsogoza Moyo Wapaŵiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere Dzichinjirizeni Molimbana ndi Kutsogoza Moyo Wapaŵiri
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chimene Ena Amatsogozera Moyo Wapaŵiri
  • Makolo, Mungathandizire
  • Chimene Moyo Wapaŵiri Uli Kwenikweni
  • Mmene Mungapewere Iko
  • Thandizani Ena Kupewa Iko
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kukhala Moyo Wachiphamaso?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri—Kulekeranji?
    Galamukani!—1994
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kuulula Zimene Ndimachita Mseri?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndingasiye Motani Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri?
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 8/1 tsamba 16-20

Achichepere Dzichinjirizeni Molimbana ndi Kutsogoza Moyo Wapaŵiri

“Kondwera, ndi unyamata wako, mnyamata iwe . . . Koma dziŵitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.”​—MLALIKI 11:9.

1, 2. Ndi chitsanzo chotani chimene chiripo cha wachichepere wotsogoza moyo wapaŵiri?

“KUYAMBIRA ku ubwana ndinaleredwa m’malo a Chikristu, pakati pa Mboni za Yehova,” analemba tero wachichiepere. Komabe, moyo umene ndinakhalamo, ngakhale pamene ndinali panyumba, unali wosiyana kotheratu ndi miyezo ndi kulingalira kwa makolo anga. Moyo wanga kwa mbali yaikulu unali wachiwerewere, moyo wosalangidwa wa kudziko.”

2 Wachichepereyo mowonjezera analongosola kuti: “Ngakhale pamene ndisanafike msinkhu wa zaka khumi, ndinayamba kuseŵera maiko aŵiri onsewo mwabwino koposa monga mmene ndikanathera​—kuti ndipeze chivomerezo ndi ubwenzi pa sukulu ndi kukhala wolandiridwabe ndi makolo anga. Ku sukulu ndinagwirizana modwanira monga mmene ndikanathera m’masitaelo ndi khalidwe . . . Koma kunyumba ndinali wosiyana kotheratu. Ndinali Mkristu wa khalidwe labwino amene makolo anga anayembekezera.”

3. (a) Ndi chidaliro chotani chimene tiri nacho, komabe nchiyani chimene timazindikira? (b) Nchiyani chomwe chasonkhezera kulunjikitsa kwathu chisamaliro kwa achichepere?

3 Tikundikira kuti khalidwe la wachichepere ameneyu siliri loimira amabiri a inu achichepere mu mpingo. Ambiri a inu, tiri ndi chidaliro, kuti muli owona mtima ndi makolo anu ndi mpingo, ndipo ichi chimatenthetsa mitima yathu. Panthaŵi imodzimodziyo, timadziŵa kuti ena amaika chophimba cha kukhala owongoka, mwabwino koposa monga mmene angathere, amabisa kuchokera kwa achikulire njira ya kachitidwe yolakwa. Chotero funso liri lakuti: Kodi muli mtundu wa munthu amene mukutipangitsa ife kulingalira kuti muli, kapena kodi mukutsogoza moyo wapaŵiri? Sitikufuna ichi mu mzimu wofuna kupeza cholakwa koma, m’malomwake, chifukwa timakukondani mowonadi ndipo tikufuna kukuthandizani kusangalala ndi uchichepere wanu mwa kukhala ndi inu m’njira imene idzasangalatsa Yehova.​—Mlaliki 11:9, 10; 12:14; 2 Akorinto 5:10.

4. Ndimotani mmene achikulire enanso atsogozera miyoyo yapaŵiri, koma nchiyani chomwe chawonedwa posachedwapa pakati pa anthu achichepere?

4 Komabe, inu mungafunse kuti: ‘Nchifukwa ninji kuloza pa ife achichepere? Bwanji ponena za achikulire?’ Palibe kukaikira kuti iwonso ayenera kudzichinjiriza molimbana ndi kutsogoza moyo wapaŵiri. Gehazi, mtumiki wa Elisa, anachita monyenga, kuyesera kubisa chenicheni chakuti iye analandira mphatso kuchokera kwa Namani. (2 Mafumu 5:20-26) Ndipo Hananiya ndi Safira, omwe anali achikulire, ananyenga mwakunena kuti anapereka kwa atumwi mtengo wonse wa munda​—kuyesera kudzipanga iwo eni kuwoneka abwino​—pamene m’chenicheni iwo anasiyako zina za ndalamazo kaamba ka iwo eni. (Machitidwe 5:1-4) Ngakhale kuli tero, chifukwa chimene, tikulunjikitsira chisamaliro kwa inu achichepere chiri chakuti mwachiwonekere pakhala chiwonjezeko m’zochitika za vutoli pakati pa inu.

Chifukwa Chimene Ena Amatsogozera Moyo Wapaŵiri

5. (a) Nchifukwa ninji achichepere ena amatsogoza moyo wapaŵiri? (b) Ndimotani mmene achichepere kaŵirikaŵiri amachitidwira pamene akhala ndi miyoyo yoyamikirika, ndipo chotero nchiyani chimene ena amachita?

5 Nchifukwa ninji ichi chiri tero? Wachichepere mmodzi analoza mwachindunji pa chifukwa chokulira, akumalongosola kuti: “Sindinafune kutaya mabwenzi anga mwa kukhala wosiyana.” Chiri chowona kuti kukhala wosiyana m’njira yabwino kaŵirikaŵiri kumapangitsa wina kukhala maziko a chitonzo. (Yerekezani ndi 1 Petro 3:16; 4:4.) Kuti apewe ichi ndi kupeza kulandirika kwa anzawo a msinkhu wawo, achichepere ena amakhoza ngakhale kuledzera kapena kukhala ndi mayanjano a kugonana. Mtsikana yemwe siali Mboni wa zaka 13 zakubadwa, yemwe ankapeza ma A m’zonse ndi amene nthaŵi zonse ankatengamo mbali m’kukambitsirana kwa kalasi, anamvera chisoni kuti: “Anyamata sadzasangalatsidwa mpang’ono pomwe mwa winawake amene mwachidziŵikire ali wabwino monga ine. . . . Ndikulingalira za kuchepetsako magredi anga kapena kuchita chinachake kuti ndidzutsenso kuchuka kwanga.”

6. Ndimotani mmene Petro anasonkhezeredwera mu mkhalidwe wolakwa, ndipo chotero ndimotani mmene ichi chiyenera kuyambukirira kuweruza kwathu kwa achichepere?

6 Mwapadera, mtumwi Petro iyemwini pa nthaŵi imodzi analingalira amokulira za chithunzi chake, kapena kutchuka, kuposa za kuchita chimene anadziŵa kuti chinali cholondola. Pamene Akristu Achiyuda kucokera ku Yerusalemu anachezera Antiokeya, Petro anachoka m’mayanjano, ndi Akristu Achikunja chifukwa cha kuwopa kusulizidwa ndi Ayuda kaamba ka kusanganizana ndi Akunja amenewa. (Agalatiya 2:11-14) Popeza ngakhale Akristu achikulire mwakutero anagonjera ku chitsenderezo cha anzawo a msinkhu wolingana, kodi chiri chodabwitsa kuti achichepere opanda kuzolowera angachite chimenechonso?​—Miyambo 22:15.

7. Nchiyani chomwe chingayese achichepere ena kutsogoza moyo wapaŵiri?

7 Chifukwa chogwirizana nacho chimene achichepere ena amatsogozera moyo wapaŵiri chiri chakuti amakhulupirira kuti iwo akuphonya zosangalatsa. Iwo amamva achichepere ku sukulu akulankhula ponena za machitachita awo​—mmene linaliri losangalatsa phwando, nyimbo zosangalatsa, kumwa, anamgoneka, zinali zinthu zosangalatsa chotani nanga zimene anali nazo! Kapena amamva mmene iye wamwamuna, kapena wamkazi, angapsyompsyonere ndi kugonana. Chotero chikhumbo cha kulawa zinthu zimenezi chimadzutsidwa, ndipo achicheperewo amasonkhezeredwa kuyesera chimene Baibulo limachitcha “chikondwerero cha kanthaŵi cha chimo.”​—Ahebri 11:24, 25, NW; 1 Akorinto 10:6-8.

8. Nchiyani chomwe chiri chifukwa chokulira chimene achichepere amatsogozera miyoyo yapaŵiri?

8 Ngakhale kuli tero, chifukwa chokulira chimene achichepere ena amatsogozera moyo wapaŵiri chiri chakuti Yehova ndi dziko latsopano likudzalo siziri kokha zinthu zenizeni kwa iwo. Iwo samakhulupirira mowanadi malonjezo a Yehova kapena machenjezo operekedwa kupyolera m’Mawu ake ndi gulu lake lowoneka ndi maso ponena za zotulukapo za kusamvera Yehova. (Agalatiya 6:7, 8) Iwo ali osiyana ndi Mose, za amene Baibulo limanena kuti: “Anapenyerera chobwezera cha mphotho ya [Mulungu]. . . . Anapirira molimbika monga ngati kuwona Wosawonekayo.” Kwa Mose, Yehova ndi malonjezo Ake zinali zenizeni. Koma awo amene amatsogoza moyo wapaŵiri amasowa chikhulupiriro chimenecho. Zonse zimene amawona ziri zimene Satana amawafuna iwo kuwona​—kunyezimira kwa dongsolo lake lakachitidwe ka zinthu. Ndipo chotero iwo amatsatira zikondwerero zosankhalitsa za chimo ndipo komabe, panthaŵi imodzimodziyo, amayesera kuvala chiyero.​—Ahebri 11:26, 27.

Makolo, Mungathandizire

9. (a) Ndimotani mmene makolo angathandizireko ku kutsogoza moyo wapaŵiri kwa ana awo? (b) Nchiyani chimene achikulire afunikira kuyamikira ndi kukhala amaso kuchita?

9 Wachichepere wogwidwa mawu poyambirirapo anawona kuti: “Chimene chinandipangitsa ine kukhala wosatchuka ku sukulu chinabweretsa chivomerezo ndi kumwetulira kwa chivomerezo panyumba. Koma ndinafuna zowonjezereka kuposa chimenecho. Ndinafuna winawake amene ndingachirikizike kwa iye, kulankhula kwa iye, ndi kumdalira, ndipo sindanali kupeza chimeneco kuchokera kwa makolo anga.” Makolo, kodi mukukukhala osamalitsa kusathandizira ku kutsogoza moyo wapaŵiri kwa ana anu? Kodi mukuwapatsa iwo chisamaliro chaumwini ndi chitsogozo chimene amachifunikira? Achikulire ayenera kuyamikira chitsenderezo chokulira, chofooketsa chikhulupiriro chimene achichepere athu amakumanizana nacho m’sukulu ndi kukhala amaso kuchita chirichonse chothekera kuwalimbikitsa ndi kuwathandiza iwo.​—Masalmo 73:2, 3; Ahebri 12:3, 12, 13.

10. (a) Ndi kufunitsitsa kotani kumene kuli thayo kaamba ka makolo kukufikira? (b) Nchiyani chimene kaŵirikaŵiri chimakhala chotulukapo pamene makolo alephera kupereka chitsogozo?

10 Kaŵirikaŵiri mafunso a achichepere amazungulira pa maunansi ndi anzawo a ziwalo zosiyana, nkhani imene, mwatsoka, makolo ambiri amaipewa. “Iwo sanalankhulepo nkhani ya mtima wonse ndi ine.” anasimba tero wophunzira wa maphunziro apamwamba wokogola wa zaka 15 zakubadwa. “Zonse zimene ndinaphunzira ponena za kugonana ndinayenera kuziphunzira pa ndekha. . . . Ndinali wamanyazi kwambiri kubweretsa nkhaniyo ngakhale kuti panali zinthu zambiri zomwe ndinafuna kudziŵa. “Kodi chotulukapo chinali chotani? Iye ananena kuti: “Chipupa chosawonekacho chinakula mochindikalachindikala pakati pa makolo anga ndi ine, ndipo ndinakhala wofunitsitsa, mtsikana wopusa ndi wogonjera.” Inde, iye anagonjera kukufunsira kwa kugonana kwa mwamuna wachichepere, koma kodi ndani amene munganene kuti anagawanako thayo kaamba ka ichi?​—Miyambo 22:3; 27:12.

11. (a) Ndimotani mmene makolo angasonyezere kuti amakonda ana awo? (b) Ndimotani mmene achichepere mwachidziŵikire angavomerezere ku chikondi choterocho?

11 Chiri chofunika kwambiri kuti makolo asonyeze achichepere awo kuti iwo ndithudi amawakonda iwo mwakuthera nthaŵi ina ndi iwo, kugawana m’nkhani ya chinsinsi, ndi kupereka zitsogozo. (Miyambo 15:22; 20:18) “Ndiri ndi lingaliro lakuti ngati iwo ndithudi amasamalira ponena za ine akanapanga malamulo ena,” anawona tero wachichepere wina. Ngakhale ngati achichepere angatsutse malamulo anu ndi zitsogozo tsopano, pambuyo pake iwo adzayang’ana m’mbuyo pa iwo ndi chiyamikiro. Wachichepere analemba kwa amayi ake kuti: “Monga mmodzi amene mokhazikika ndinali kuyesa malirewo, kuyang’anayang’ana kaamba ka malo ofewa ndi njira za kupulumukira malamulo ndi zitsogozo zolimbazo, ndiri woyamikira koposa kuti munasungirira ulamuliro wolimba pa ine.” Chotero sonyezani kuti mumakonda ana anu mwakufuna kuti iwo agonjere ku zitsogozo zanu. Lolani kuti musathandizire nkomwe ku kutsogoza kwawo moyo wapaŵiri mwakulephera kusunga njira zolankhulira zotseguka kapena mwakulephera kukhalapo pamene akufunani!

12. Ndi kawonedwe kopanda nzeru kotani kamene makolo ena angathandizireko ku kutsogoza moyo wapaŵiri kwa ana awo?

12 Makolo angathandizirenso m’njira yosiyana ku kutsogoza moyo wapaŵiri kwa ana awo. Ndemanga za woweruza wa bwalo lamilandu lapamwama mu boma la New Jersey zikuchitira chitsanzo. “Aphunzitsi,” ananena tero woweruzayo, “Amayesera kulanga ana kaamba ka kuchita cholakwa m’sukulu ndipo kenaka amazonzidwa ndi makolo m’malo mochirikizidwa.” Chikuwoneka kuti makolo ena molakwa amakhulupirira kuti achichepere awo sangachite cholakwa. Ngakhale pamene mkulu Wachikristu kapena munthu wina wathayo mu mpingo abweretsa cholakwa cha ana awo ku chisamaliro chawo, makolo amatembenuzira khutu logontha. Mwakuchita tero, iwo amathandizira ku kukhala paŵiri kwa ana awo.

Chimene Moyo Wapaŵiri Uli Kwenikweni

13. Kutsogoza moyo wapaŵiri ndithudi kumafikira ku chiyani?

13 Ichi chiri chofunika kwambiri kulingalira: Kutsogoza moyo wapaŵiri ndithudi kumafikira ku kusewera ndi bodza​—kukhala wabodza, wonyenga. (Masalmo 12:2; 2 Timoteo 3:13) Chiri kukhala monga Satana, yemwe “amadziwonetsera ngati mngelo wakuwunika.” (2 Akorinto 11:14, 15) Chimatanthauzanso kukhala monga atsogoleri aja a chipembedzo amene ponena za iwo Yesu ananena kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene awonekera okoma kunja kwake koma adzala mkatimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. Chomwecho inunso, muwonekera olungama pamaso pa anthu, koma mkati muli odzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika.” (Mateyu 23:27, 28) Mwachiwonekere, kutsogoza moyo wapaŵiri liri chimo lokulira molimbana ndi Mulungu.

14. Nchifukwa ninji munthu afunikira kupewa kutsogoza moyo wapaŵiri?

14 Nsonga ina yofunikira kuilingalira mosamalitsa iri iyi: Njira ya chinyengo singabisidwe kosatha. “Ngakhale mwana adziŵika ndi ntchito zake ngati ntchito yake iri yoyera ngakhale yolungama,” limatero Baibulo. (Miyambo 20:11; Luka 12:1-3) Inde, zochitachita zanu, kaya zabwino kapena zoipa, m’kupita kwanthaŵi zidzadziŵika. Ndipo Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzalanga mowopsya onyenga. (Mateyu 24:51) Ndithudi inu muyenera kufuna kupewa kutsogoza moyo wapaŵiri!

Mmene Mungapewere Iko

15. Nchiyani chomwe chidzathandiza achichepere kupewa kutsogoza moyo wapaŵiri?

15 Njira imodzi ya kupewera kutsogoza moyo wapaŵiri iri kuyang’anizana ndi chimene icho kwenikweni chimafikira ndipo kenaka kudzifunsa inu eni: Kodi mmenemo ndi mmene ndizafunira kukumbukiridwa, monga wonyenga, monga mtsanzira wa Satana ndi Afarisi? Ndithudi ayi! Cinachake chimene chidzakuthandizani inu kupewa kutsogoza moyo wapaŵiri chiri kulingalira za kuŵawidwa mtima ndi tsoka laumwini limene moyo woterowo udzabweretsa kwa inu. Kumbukirani chimene chinachitika kwa Gehazi kaamba ka kuyesera kukhala ndi bodza. Khate la Namani linamkantha iye, ndipo anali wakhate kwa moyo wake wonse. Ndipo Hananiya ndi Safira onse aŵiri anakanthidwa mpaka kufa ndi Mulungu kaamba ka kuyesera kuyengezera kukhala oolowa manja.​—2 Mafumu 5:27; Machitidwe 5:5, 9, 10.

16. Nchiyani chimene chinachitika kwa wachichepere mmodzi yemwe anadzilowetsa m’njira ya moyo ya kudziko?

16 Palinso zitsanzo zamakono. Wachichepere mu United States anayamba kuphunzira Baibulo ndi kupezeka pa misonkhano pa Nyumba ya Ufumu. Koma kenaka iye anayamba kudzikowetsa m’njira ya moyo ya kudziko ndi kuleka kuyanjana. Zaka zambiri zinapita, ndipo iye analemba kuti: “Chifupifupi miyezi iŵiri yapitayo ndinafunsa Mulungu kutumiza kwa ine Mboni chifukwa chakuti ndinachimva chikhumbo cha kuyambanso. Ndinayamba kuphunziranso kachiŵiri pamene bombalo linaphulika. Mwezi wathawu ndinapimidwa kukhala ndi matenda a Kaposi’s sarcoma, mbali yatsopano yosachiritsika ya dongosolo la AIDS.” Iye anamaliza kuti: “Ngati kokha ndinatsatira ndi kumvera machenjezo a Malemba kumbuyoko, sindikanakhala mu mkhalidwe uwu lero.” Ndithudi mufunikira kupewa zotulukapo zirizonse zomvetsa chisoni zoterozo! Dziko ndithudi liribe chirichonse chopindulitsa choti lipereke.​—1 Yohane 2:15-17.

17. Ndi kulingalira kowonjezereka kotani kumene kuyenera kuthandiza achichepere kupewa kutsogoza moyo wapaŵiri?

17 Chimene chidzakuthandizaninso kupewa kutsogoza moyo wapaŵiri chiri kulinglaira chotulukapo chimene kuchita tero chidzakhala nacho pa dzina la Yehova. Wachichepere wotchulidwa m’mawu oyambirirayo ananena kuti winawake amene anamuwona iye akulandira ndudu anachitira ndemanga kuti: “Sindinadziŵe kuti Mboni za Yehova zimasuta. Kodi iwe suli Mboni?” Iye pambuyo pake ananena kuti funsolo linampangitsa iye kudzimva moipidwa chifukwa chomwe anali kuchita chinali kubweretsa chitonzo pa Yehova. Kodi mukufuna chimenecho? Kodi mumalingalira mochepera chotero za Mulungu wathu chakuti mofanana ndi Israyeli wosakhulupirika wa nthaŵi zakale mudzabweretsa manyazi pa dzina lake?​—Masalmo 78:36, 37, 41; Ezekieli 36:22.

18. (a) Ndimotani mmene makolo mwachidziŵikire angachitire ngati adziŵa kuti mwana wawo anali kutsogoza moyo wapaŵiri? (b) Nchifukwa ninji ichi chiyenera kuletsa achichepere Achikristu kutsogoza moyo wapaŵiri?

18 Pambali pa icho, lingalirani dzina ndi kudzimva kwa makolo anu. “Tsikulo linafika pamene makolo anga anadziŵadi amene ndinali kwenikweni,” analemba tero wachichepere wotchulidwa pamwambayo. “Chinawadabwitsa iwo. Ndipo kwanthaŵi yoyamba m’moyo wanga ndinawona amayi wanga ndi atate akulira. Iwo anapwetekedwa koposa ndi chimene ndinachita.” Makolo anu mwinamwake angalire, nawonso, ngati adziŵa kuti munali kutsogoza moyo wapaŵiri. Kodi chimenecho ndi chimene mukufuna? “Dzina labwino liri lokhumbirika koposa kuposa chuma chokulira,” limatero Baibulo. (Miyambo 22:1, The Jerusalem Bible) Mwa kutsogoza moyo wapaŵiri, mumawononga dzina lanu lenileni labwino. Koma sichokhacho. Mumawononganso dzina labwino la makolo anu ndi kulikwirira ilo m’matope, kuwachepetsa ndi kuwachititsa manyazi.​—Miyambo 10:1; 17:21.

19. Ndimotani mmene mkhalidwe woipa wa ana amuna a Yakobo unawunikirira pa iye, ndipo ndi phunziro lotani limene tingatenge kuchokera ku ichi?

19 Ana a amuna a Yakobo amachitira bwino chitsanzo mmene ana angaipitsire dzina labwino la makolo. Pamene mwana wamkazi wa Yakobo Dina anaipitsidwa, abale ake anapha amuna a mu mzindawo ndipo kenaka kuwufunkha mzindawo, kumpangitsa Yakobo kulira: “Mwandisautsa ndi kundinunkhitsa ine kwa anthu okhala m’dzikomu.” Mulungu anfikira pa kutsogoza Yakobo kuchoka m’gawolo. (Genesis 34:30; 35:1) Inunso mungapangitse dzina la atate ndi amayi wanu kununkha, kuwapangitsa iwo kukhala amanyazi ngakhale kuyang’anizana ndi anansi awo ndi mabwenzi. Ndithudi, monga momwe Baibulo limanenera: “Mwana wopusa achititsa atate wake chisoni namvetsa zoŵaŵa amake wombala.”​—Miyambo 17:25.

20. Ndi mphatso yaikulu yotani imene makolo Achikristu aipanga kukhalapo kwa ana awo?

20 Tiri ndi chidaliro, ngakhale kuli tero, kuti simukufuna kuchititsa chisoni ndi zoŵaŵa makolo anu. Chotero lingalirano zotulukapo za kachitidwe kanu pa iwo. Ndiponso, ngati muli ndi mwaŵi wa kukhala ndi makolo Achikristu, lingalirani za chimene iwo akupatsani​—osati kokha moyo​—koma chinachake cha mtengo wapatali mokulira. Baibulo limanena za Yehova: “Pakuti chifundo chanu chiposa moyo.” (Masalmo 63:3) Mwakukulerani m’chowonadi, makolo anu apanga chifundo chokoma mtima cha Mulungu kukhalapo kwa inu, kukuthandizani kukhala ndi unansi ndi iye. Kukhala ndi ichi chiri chabwino koposa moyo weniweniwo chifukwa ngakhale ngati muyenera kufa, Mulungu adzakubwezeretsani inu ku moyo wosatha m’Paradaiso.

Thandizani Ena Kupewa Iko

21. (a) Ndi thayo lotani limene achichepere omwe amadziŵa za kachitidwe kolakwa ka ena ali nalo? (b) Ndi chitanzo chabwino chotani chimene mmodzi wa zaka 13 zakubadwa anapereka?

21 Bwanji ngati mudziŵa winawake amene akutsogoza moyo wapaŵiri? Choyamba, limbikitsani munthuyo kufikira akulu. Ndipo bwanji ngati mwamunayo kapena mkaziyo akana kuchita chimenecho? Chotero liri thayo lanu la m’Malemba kusimba icho. (Levitiko 5:1) Tikuzindikira kuti ichi sichingakhale chopepuka, koma chiri chinthu choyenera kuchichita. “Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika,” limatero Baibulo. (Miyambo 27:6) Mtsikana wa zaka 13 zakubadwa, pambuyo pa kumva nkhani yolongosola thayo lake la m’Malemba, anapita kwa bwenzi lomwe anadziŵa kuti linali kudzilowetsa m’kachitidwe kolakwa ndi kumuuza iye kulapa kwa akulu. “Ndinapita ndi kufufuza ngati iye analankhula kwa mkulu aliyense,” mtsikanayo akulemba tero. “Iye sanatero. Chotero ndinapita ndi kulankhula ndi mmodzi wa iwo.” Mtsikana wachichepereyo anafunsa kuti: “Kodi ndinachita chinthu chabwino mwakuneneza ‘bwenzi langa lapamtima lakale?’” Ndithudi iye anatero! Pamene kuli kwakuti zotulukapo zamwamsanga za kuchita ichi zingakhale zomvetse chisoni, chotulukapo pambuyo pake chingakhale chachimwemwe, ngakhale chopulumutsa moyo kwa wochita cholakwayo.​—Ahebri 12:11.

22. Ndi njira yanzeru yotani imene achichepere akulimbikitsidwa kutenga, ndipo nchiyani chomwe chidzakhala chotulukapo chake?

22 Komabe zonsezi zingapewedwe ngati inu simutsogoza moyo wapaŵiri m’malo oyamba. Chotero khalani anzeru. Kulitsani unansi wamphamvu waumwini ndi Mulungu, monga mmene mungachitire ndi bwenzi lapafupi. Chitani ichi mwakupemphera mokhazikika kwa iye, mwa kufunsira kaamba ka thandizo lake, ndipo mwakhama kuphunzira Mawu ake, Baibulo, kotero kuti inu ndithudi mufikire kukuyamikira mikhalidwe yake. Achichepere, mwakutero mudzadalitsidwa ndipo mudzapanga mtima wa makolo anu kusangalala. Koma chofunika koposa, mudzapanga mtima wa Yehova kusangalala.​—Miyambo 27:11.

Kodi Mukayankha Motani?

□ Nchifukwa ninji achichepere ena amatsogoza moyo wapaŵiri?

□ Ndimotani mmene makolo ena amathandizira ku kutsogoza moyo wapaŵiri kwa ana awo?

□ Kutsogoza moyo wapaŵiri ndithudi kumafikira ku chiyani?

□ Ndimotani mmene achichepere angapewere kutsogoza moyo wapaŵiri?

□ Ndi thayo lotani limene achichepere ali nalo ngati adziŵa za achichepere ena omwe achita zolakwa zazikulu?

[Chithunzi patsamba 18]

Kulankhula kwa chinsinsi kumachitira chitsanzo chikondi cha kholo

[Chithunzi patsamba 20]

Ngati mukudziŵa kuti winawake wachita chimo lokulira, limbikitsani ameneyo kulisimba ilo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena