Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 8/1 tsamba 30
  • Dzina la Mulungu ndi Atembenuzi a Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dzina la Mulungu ndi Atembenuzi a Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Dzina la Mulungu ndi “Chipangano Chatsopano”
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
  • Zimene Zikuchititsa Kuti Anthu Asalidziwe Dzina la Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Dzina la Mulungu ndi Otembenuza Baibulo
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 8/1 tsamba 30

Dzina la Mulungu ndi Atembenuzi a Baibulo

MU 1952, The Bible Translator inafalitsa kukambitsirana kwa “vuto” loimira dzina la Mulungu m’matembenuzidwe a Baibulo kaamba ka kugwiritsidwa ntchito m’minda ya Chikristu cha Dziko. Othandizira anazindikira kufunika kwa dzinalo m’Baibulo​—dzina lomwe limawoneka m’Malemba Achihebri chifupifupi nthaŵi 7,000. Koma iwo sanamvane pa mmene ilo liyenera kulembedwera m’zinerero zamakono. Ena anakonda mawu onga ngati “Wokhalako Nthaŵi Yonse.” Ena anakonda dzina la ulemu lakuti “Ambuye.” Palibe ndi mmodzi yemwe anavomereza katchulidwe kakuti “Yehova” kapena “Yahweh.” Nchifukwa ninji ayi?

Zifukwa ziŵiri zinatchulidwa ndi wothandizira H. Rosin. Choyamba, iye anakhulupirira kuti pamene Baibulo la Chihebri linatembenuzidwa poyambirira kupita ku Chigriki (kutemenduza kwa Septuagint ya nthaŵi ya Chikristu chisanakhale) atemenuziwo anatchula dzina la Mulungu ndi liwu la Chigriki kaamba ka “Ambuye.” Kachiŵiri, iye anawopa kuti kuyambitsa dzina lakuti Yehova m’matembenuzidwe “kungagawanitse pakati tchalitchi.” Popeza kuti, iye anawonjezera kuti, “kodi ‘mboni za Yehova’ siziri zokana Utatu?”

Ponena za nsonga yoyambirira ya Rosin, zopezedwa za sayansi yofukula zinthu zofotseredwa kale zam’tsimikizira iye kukhala wolakwa. M’chenicheni, atembenuzi a Septuagint sanaimire dzina la umulungu ndi liwu la Chigriki kaamba kakuti “Ambuye.” M’malomwake, iwo analilemba ilo m’zilembo zake zoyambirira za Chihebri m’lemba la Chigrikilo, kotero kuti makope a matembenuzidwe a Septuagint ogwiritsiridwa ntchito ndi Akristu oyambirira anali ndi dzina laumulungu.

Mosangalatsa, pamene Akrisut oyambirira anagwira mawu kuchokera ku Septuagint chiri chosayenerera mokulira kuti iwo anachotsa dzinalo kuchokera m’kugwira mawuko. Chotero, mamanuskripiti oyambirira a Malemba Achikristu a Chigriki (“Chipangano Chatsopano”) moposa ndi kuyenerera anali ndi dzina la Mulungu. Profesa George Howard, m’nkhani yowonekera mu Biblical Archaeology Review, March 1978, anapereka zitsutso zamphamvu kaamba ka mapetowa. Mwachitsanzo, iye akutchula “ndime ya urabi yotchuka (Talmud Shabbat 13.5)” yomwe “imakamba vuto la kuwononga malemba oyambirira (mwinamwakedi kuphatikizapo mabukhu a Akristu Achiyuda).” Nchiyani chimene chinali vutolo? “Malemba oyambirirawo anali ndi dzina laumulungu, ndipo kuwonongedwa kwawo kotheratu kukaphatikiza kuwononga kwa dzina laumulungu.”

Koma bwanji ponena za chitsutso chachiŵiri cha Rosin? Kodi kugwiritsira ntchito kwa dzina la Mulungu kukapangitsa mavuto kaamba ka Chikristu cha Dziko? Chabiwno, lingalirano chomwe chinachitika pamene dzinalo linachotsedwa. Pamapeto pa zana loyamba, olemba a “Chikristu” analowetsa m’malo dzina la Mulungu ndi mawu akuti “Mulungu” ndi “Ambuye” mu ponse paŵiri Septuagint ndi Malemba Achikristu a Chigriki. Mogwirizana ndi Profesa Howard, ichi mwachidziŵikire chinagawirako ku phokoso lomwe Chikristu cha Dziko chinakumanizana nalo m’zaka za pambuyo pake: “Chingakhale mwinamwake kuti kuchotsedwaka Tetragrammaton [dzina la Mulungu m’Chihebri] kunathandizira mowonekera ku mikangano ya Chikristu ndi Utatu yomwe inakantha tchalitchi cha Akristu a m’mazana oyamba.”

Ndithudi, kuchotsedwa kwa dzina la Mulungu kuchoka m’Baibulo kunapangitsa kutenga kwa Chikristu cha Dziko chiphunzitso cha Utatu kukhala kopepuka mokulira. Chotero, ngati Chikristu cha dziko chinayenera kubwezeretsa dzinalo m’Baibulo lonse ndi kulambira, chikapangitsa mavuto. Yehova, monga mmene iye wavumbulutsidwira m’Chihebri ndi Malemba Achikristu a Chigriki, ali mwachiwonekere wosiyana ndi Yesu Kristu ndipo sali mbali ya Utatu.

Profesa Howard ananena m’kuwonjezerepo kuti: “Kuchotsedwa kwa Tetragrammaton mwinamwake kunapanga kusiyana kokulira m’maphunziro a zaumulungu kuchokera ku amene anakhalako mkati mwa nyengo ya Chipangano Chatsopano ya zana loyamba. Mulungu Wachiyuda yemwe nthaŵi zonse anakhala wosamalitsa kupatulidwa kuchokera kwa ina mwakugwiritsira ntchito dzina lake la Chihebri anataya kwina kwa kukhala payekha kwake ndi kupita kwa Tetragrammaton,” Mboni za Yehova zabwezeretsa dzina la Mulungu osati kokha m’Baibulo lonse komanso m’kulambira kwawo kwa tsiku ndi tsiku. Chotero, iwo amasunga ‘kusiyana kosamalitsa’ pakati pa Mulungu wowona ndi milungu yonyenga ya dziko iri. Mwanjira imeneyi atheketsedwa kubweretsa “mkhalidwe wa maphunziro a zaumulungu” omwe analiko m’tchalitchi cha Akristu a m’zana loyamba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena