Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 8/1 tsamba 27-29
  • Chifundo Chokoma Mtima cha Mulungu—Musaphonye Chifuno Chake!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifundo Chokoma Mtima cha Mulungu—Musaphonye Chifuno Chake!
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifuno cha Mulungu Chizindikiritsidwa
  • Chitsanzo Chamakedzana
  • Chifuno cha Kupulumutsidwa Kwathu
  • ‘Musaphonye Chifuno Chake’
  • Tiziyamikira Kukoma Mtima Kwakukulu kwa Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Tizilalikira Uthenga wa Kukoma Mtima Kwakukulu kwa Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Tinamasulidwa ku Uchimo Chifukwa cha Kukoma Mtima Kwakukulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Mkondweretseni Yehova Mwakusonyeza Kukoma Mtima
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 8/1 tsamba 27-29

Chifundo Chokoma Mtima cha Mulungu​—Musaphonye Chifuno Chake!

“KULANKHULA ponena za chipembedzo . . . iyo iridi ntchito ya pasitala,” chinatero chiwalo chimodzi cha tchalitchi. (Kanyenye ngwathu.) Ena avomereza tero, “Akristu ochepera kwambiri amapanga kuyesetsa kugawana chikhulupiriro chawo ndi ena.” (Kanyenye ngwathu.) Ndemanga zoterozo mowonekera zimagogomezera kuti ambiri a anthu opita ku tchalitchi lerolino, Chikristu chimafikira ku chochepera kuposa chikhulupiriro chosagwira ntchito mwa Mulungu ndi mwa Kristu monga Mesiya.

Nchiyani chimene chiri kawonedwe kanu? Ophunzira a Yesu anagawana chikhulupiriro chawo ndi ena. (Luka 8:1) Kodi Akristu lerolino ayenera kuchita chofananacho? Kapena ngati Mulungu safunanso odzinenera kukhala Akristu kukhala alengezi, nchiyani chimene iye akuyembekezera kwa iwo? Kodi Mulungu ali ndi chifuno kaamba ka Akristu lerolino? Inde! Ndipo kaamba ka chifukwa chimenechi, chenjezo la mtumwi Paulo kwa Akristu a ku Korinto lakuti “asalandire chifundo chokoma mtima cha Mulungu ndi kuphonya chifuno chake” liri ndi tanthauzo kwa ife. (2 Akorinto 6:1, NW) Tiyeni tiwone nchifukwa ninji.

Chifuno cha Mulungu Chizindikiritsidwa

Mofanana ndi Paulo, Akristu a ku Korinto analandira nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. Chifukwa cha chikhulupiriro chawo m’chopereka chimenechi, Yehova anawalengeza iwo olungama. Kulandira kwawo kwa zowonadi za Umesiya zolandiridwa kupyolera mu utumiki wa Paulo kunawapulumutsa iwo kuchokera ku ukapolo ku chinyengo, machitachita achikunja, ndi makhalidwe oipa kaamba ka amene Korinto wakale anali wotchuka. Kwa iwo, chifundo chokoma mtima cha Yehova chinatanthauza chipulumutso chawo. Ngakhale kuli tero, kodi chifundo chokoma mtima choterocho chinali chopanda chifuno?

Ayi. M’malomwake, chifuno cha Yehova m’kuwapulumutsa iwo chinali chofanana ndi mmene chinaliri chifuno chake m’kupulumutsa Paulo kuchokera ku miyambo yosakhala ya m’malemba ya atate a Paulo. Paulo iyemwini akuchipangitsa chifuno chimenecho kukhala chomvekera: “Umene anadikhalitsa mtumiki wake monga mwa mphatso ya [chifundo chokoma mtima, (NW) cha Mulungu chimene anandipatsa ine . . . ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Kristu.” (Aefeso 3:7, 8; yerekezani ndi Agalatiya 1:15, 16.) Inde, chifuno cha chifundo chokoma mtima cha Mulungu chinali chakuti atumiki ake atenge kulambira kowona​— kukwezeka dzina lake, Yehova, ndi kulidziŵikitsa ilo mu utumiki Wachikristu, monga mmene Paulo anachitira.​—Aroma 10:10.

Ngakhale kuli tero, pamene Paulo analemba kalata yake yoyamba kwa Akorinto, chinali chachidziŵikire kuti ambiri a iwo anaphonya chifuno cha chifundo chokoma mtima cha Mulungu. Motani? M’malo mwakusungilira mtundu wa kulambira umene unali woyera ndi wolandirika pamaso pa Mulungu, iwo analola chisonkhezero cha chisembwere cha nzika za mu Korinto kufooketsa malingaliro awo. Ponse paŵiri mipatuko ndi dama zinasimbidwa pakati pawo. (1 Akorinto 1:11; 5:1, 2) Ambiri a awo oyanjana ndi mpingo anawongoleredwanso ndi uphungu wa Paulo. Mosasamala kanthu za chimenecho, Paulo sanafune iwo kukhala ndi zochewutsa zowonjezereka kuchoka ku utumiki Wachikristu. Chotero, iye pambuyo pake anawakumbutsa iwo “kusalandira chifundo chokoma mtima cha Mulungu ndi kuphonya chifuno chake.”​—2 Akorinto 6:1, NW.

Chitsanzo Chamakedzana

Mkhalidwe wofanana ndi uwu unakula zaka mazana angapo kumayambiriro. M’ngululu ya 537 B.C.E., Yehova Mulungu anamasula mtundu wake wosankhidwa wa Israyeli kuchoka ku ukapolo Wachibabulo kupyolera mwa mfumu ya Peresiya Koresi. Chifuno cha kuwomboledwa kwawo chinazindikiritsidwa ndi Koresi iyemwini mu lamulo lotsatirali: “Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye. Akwere kumka ku Yerusalemu, ndiwo m’Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israyeli.”​— Ezara 1:1-3.

Inde, inali nthaŵi yoikidwiratu ya Yehova kukhala ndi kulambira kowona kutabwezeretsedwa m’dziko la Yuda. Chifukwa cha chifundo chokoma mtima cha Yehova, Auyda obwezeretsedwa kwawo amenewo anali ndi mwaŵi wa kumanganso kachisi wake m’Yerusalemu. Akumachilandira chitokosocho, othaŵa kwawo obwererawo anakhazikikanso m’dziko la kwawo ndi kuyamba ntchito yobwezeretsanso pa kachisi.​—Ezara 1:5-11.

Mkati mwa kanthaŵi kochepa, ngakhale kuli tero, mtundu wa Chiyuda wobwezedwa umenewo unalola chitsutso chakunja kusokoneza ntchito yawo. M’malo mwa kupitiriza kukhala osumika m’maganizo chifuno cha chipulumutso chawo, iwo anayamba kunena kuti: “Nthawi siinafike, nthaŵi yakumanga nyumba ya Yehova.” (Hagai 1:2) Monga chotulukapo chake, ntchito yomangansoyo inasiidwa kotheratu kwa chifupifupi zaka 16.

Panthaŵiyi, iwo anatanganitsidwa ndi zolondola zadyera, kuika chigogomezero chokulira pa zinthu zakuthupi, zosangalatsa zakuthupi, kuposa kumanganso nyumba yopatulika ya Yehova. (Hagai 1:3-9) Pa Hagai 1:4 timaŵerenga kuti: “Kodi imeneyi ndiyo nthaŵi yakuti inu nokha mukhale m’nyumba zanu zochingidwa mkatimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?” Nyumba yolambirira ya Yehova inali “yopasuka,” yokhala kokha ndi maziko, pamene Auyda anali kukhala m’nyumba zofoleredwa bwino ndi zipupa zawo zochinjirizidwa bwino ndi mitengo yabwino.

Kupyolera mwa aneneri ake Hagai ndi Zekariya, Yehova anakumbutsa Ayudawo za chifuno cha kupulumutsidwa kwawo, ndipo ntchito yomangansoyo pomalizira pake imatsirizedwa. Ngakhale kuli tero, aliyense amene anapitiriza kusungilira zinthu zakuthupi m’malo apamwamba kuposa mwaŵi wa kuwona kubwezeretsedwa kwa kulambira kowona m’Yerusalemu mwachiwonekere anaphonya chifuno cha chikondi chokoma mtima cha Mulungu.

Chifuno cha Kupulumutsidwa Kwathu

Nchiyani chimene tingaphunzire lerolino kuchokera ku chitsanzo cha Ayuda obwezeretsedwa ku dziko la kwawo mu 537 B.C.E., ndi kuchokera kwa Akristu a ku Korinto a m’tsiku la Paulo? Monga atumiki odzipereka a Yehova Mulungu, ifenso takumana ndi chipulumutso. Kupyolera mwa chikondi chake chokoma mtima, sitirinso akapolo ku ziphunzitso zonyenga ndi miyambo ya Babulo Wamkulu kapena ku kuipa kwa dongosolo lino lakale la kachitidwe ka zinthu. (Yohane 8:32; 2 Akorinto 4:4-6) Kupulumutsidwa koteroko, limodzinso ndi ufulu umene kumabweretsa, kumatitheketsa ife mwaŵi wa kusonyeza Mulungu chiyamikiro chathu kaamba ka chikondi chake kaamba ka ife. (1 Yohane 4:9) Motani?

Mwakusaphonya kwathu chifuno cha chifundo chokoma mtima cha Mulungu. Ichi chiri chofanana ndi mmene chinaliri ndi atumiki oyambirira amenewo a Yehova, kuti ife tiyenera kutenga kulambira kowona. Lerolino, mofanana ndi m’tsiku la Paulo, ichi chimatanthauza kuti “tilengeze kwa amitundu mbiri yabwino yonena za . . . Kristu.” (Aefeso 3:8) Onse, chotero, omwe alandira chifundo chokoma mtima cha Mulungu ayenera kugawana mu utumiki Wachikristu. Ichi chimatanthauza kuti monga atumiki odzipereka a Yehova Mulungu, tiri ndi thayo la kupanga chowonadi kuwonekera kwa ena, kukweza ndi kutamanda dzina la Mulungu, ndi kumtumikira iye m’kulambira komwe kuli koyera ndi kopatulika.​—Mateyu 28:19, 20; Ahebri 13:15; Yakobo 1:27.

‘Musaphonye Chifuno Chake’

Kodi chiri chothekera kuti aliyense wa ife, mofanana ndi Akristu oyambirira amenewo, ali m’ngozi ya ‘kuphonya chifuno’ cha chifundo chokoma mtima cha Mulungu? Inde. Mofanana ndi iwo, ambiri a ife, pa ntchito kapena ku sukulu, timakhudzana mapewa ndi anthu omwe amachita mkhalidwe woipa wa chisembwere, kuba, kunama, ndi kunyenga, limodzinso ndi zinthu zina zomwe ziri zonyansa kwa Yehova Mulungu. (1 Akorinto 6:9, 10; Agalatiya 5:19-21) Chotero chiri chofunika kwambiri kuti tipewe kuyanjana ndi anthu otero, kupanda apo tidzayamba kukulitsa kulaŵa kaamba ka chimene chiri choipa. (1 Akorinto 15:33) Mayanjano oterowo angakhale kokha ndi chiyambukiro chosakaza pa chikhulupiriro chathu. Moyenerera, Paulo analembera Tito kuti: “Pakuti chawonekera [chifundo chokoma mtima, (NW)] cha Mulungu cha kupulumutsa anthu onse, ndi kutiphunzitsa ife kuti pokana chisapembedzo ndi zilakolako zadziko lapansi tikhale ndi moyo m’dziko lino odziletsa ndi olungama ndi opembedza.”​—Tito 2:11, 12.

Ena angamalize kuti akukwaniritsa utumiki wawo ngati apezeka pa misonkhano pa Nyumba ya Ufumu, kugawana mokhazikika m’kulengeza mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, ndipo sakudzilowetsa mu mkhalidwe uliwonse wa chisembwere. Ngakhale kuli tero, pali nsonga ina imene tiyenera kuilingalira. Yesu ananena kuti: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri.” (Mateyu 6:24) Kodi nchiyani chimene iye anatanthauza? Kuti ngakhale ngati tingapereke mlingo wa nthaŵi yathu ku kupititsa patsogolo kwa mbiri yabwino, chiri chothekera kaamba ka chikondwerero chathu chenicheni m’moyo kukhala chija cha kukalamira kaamba ka zinthu zakuthupi zowonjezereka. Zowona, tingapeze chiyembekezo cha dongosolo latsopano la kachitidwe ka zinthu pansi pa Kristu Yesu kukhala chosangalatsa moyenerera, komabe panthaŵi imodzimodziyo tingafune kupeza zochuluka koposa kuchokera ku dongosolo lino pamene lidakalipo. Mkhalidwe woterowo ungangotipatutsa kokha kuchoka ku chifuno chenicheni cha kupulumutsidwa kwathu. Kodi sunali mkhalidwe wofananawo kulinga ku zolondola za zinthu zakuthupi umene unapatutsa Ayuda obwezeretsedwa ku dziko la kwawo kuchokera ku kukwaniritsa chifuno cha chipulumutso chawo?

Kodi ntchito zathu zimasonyeza kuti taphonya chifuno cha chipulumutso chathu kuchokera ku dongosolo iri lakale la kachitidwe ka zinthu ndi chipembedzo chake choyenga? Paulo anauza Akorinto kuti “tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa” kuthandiza ena kupeza chipulumutso. (2 Akorinto 6:2) Lerolino, ndi chiwonongeko chomayandikira cha dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu loipa chiri pafupi, pali chisonkhezero chokulira ku mawu a Paulo. Pamene kuli kwakuti chiri chachiwonekere kuti ambiri a anthu opita ku tchalitchi lerolino amasankha kusagawana chikhulupiriro chawo ndi ena, Akristu osonyeza chikondi cha mtima wonse kaamba ka Yehova Mulungu adzawuŵerengera iwo kukhala mwaŵi kugawana mokwanira mu utumiki Wachikristu umene iye wagawira iwo. Awo onse amene mokhulupirika amalalikira mbiri yabwino m’nyengo yolandirikayi ndi kutumikira Yehova m’kulambira komwe kuli koyera ndi kopatulika angachite tero ndi chitsimikizo chakuti iwo ‘alandira chifundo chokoma mtima cha Mulungu ndipo sanaphonye chifuno chake.’​—2 Akorinto 6:1, NW.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena