Ripoti la Olengeza Ufumu
‘Zotuta Zachetsa’ mu Burma
◻ DZIKO lokongola la Burma liri ndi olengeza a mbiri yabwino oposa 1,500. Misonkhano yawo ya posachedwapa inachitidwa m’zinenero za Burmese, Lushai, ndi Haka Chin, ndi chiwonkhetso cha opezekapo 2,273. Zokumana nazo zotsatirazi zikuvumbula chikondwerero chimene anthu onga nkhosa ali nacho mu uthenga wa Ufumu ndipo zinagogomezera chimene Yohane anawona m’masomphenya: “[Zotuta, NW] za dziko zachetsa.”—Chibvumbulutso 14:15.
Zinachitikira mu Dinam
◻ Pamene anali mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba mu Matupi, mpainiya wapadera anakumana ndi wophunzira yemwe anali wokondweretsedwa mwachindunji m’kudziŵa ponena za helo. Pamene iyo inalongosoledwa kwa iye kuti helo wa Baibulo ali manda wamba a mtundu wa anthu, iye anadabwitsidwa kwenikweni. Iye sanakhoze kuchisunga icho kwa iyemwini koma anafuna kuwuza anansi ake okhala m’mudzi wake wa Dinam. Mkati mwa matchuthi a sukulu, iye anabwerera kumudzi wake ndi kufalitsa chowonadi ponena za helo. Mlamu wake wamwamuna anali wokondweretsedwa kwenikweni m’kudziŵa zochulukira, chotero iye anatsagana ndi wophunzirayo kubwerera ku Matupi kukalankhula kwa mpainiyayo iyemwini. Iye anakhala kwa milungu ingapo mu Matupi ndi kuphunzira ndi mpainiyayo. Pambuyo pake, mkati mwa kuchezera kwake kwachiŵiri ku Matupi, iye anaumirira kuti apainiyawo achezere mudzi wake, popeza kuti, iye ananena kuti, kunali anthu okondwerera ambiri kumeneko. Apainiya atatu onsewo analandira mosangalala chiitanocho. Chinawatengera iwo maora 12 athunthu kuti afike ku Dinam.
Panali maliro mu Dinam pa tsiku limene apainiyawo anafika, ndipo anthu ochokera mu midzi yapafupi anali kumenekonso kukamvetsera zochulukira ponena za helo wa m’Baibulo ameneyu. Onsewo anathamangira kukawona alendowo. Kukambitsirana kwa Baibulo kunayambika komwe kunatha kuyambira pa 7:00 p.m. mpaka 11:00 p.m. Munthu womvetsetsa m’khamulo anaimitsa kukambitsiranako pa 11:00 p.m., kulola apainiyawo kupuma pang’ono kaamba ka tsiku lotsatira. M’mawa motsatira, iwo anayamba kukambitsirana kwa Baibulo pa chifupifupi ora lachisanu ndi chiŵiri ndi kupitirizabe kufika pa ora la khumi madzulo, ndi kokha kupuma kochepera kaamba ka zakudya. Pamene apainiyawo anachoka pamudzipo, anthu onga nkhosa anali kufunsa kuti iwo abwerereko ndi kuthera nthaŵi yochulukira ndi iwo. Ndi mwaŵi wotani nanga kuthandiza anthu ophunzitsika oterowo ndi mbiri yabwino ya mtengo wapatali ya Ufumu. Zowonadi, zotuta ‘zachetsa’ mu Burma!
Kupeza Chowonadi Kuchokera m’Bukhu Lotayidwa
◻ Mwamuna mu Burma ankachezera bwenzi lake lomwe limagulitsa mabukhu akale ndi manyuzipepala monga mapepala opanda ntchito ndipo anawona bukhu lakale lopanda chikuto pakati pa mapepala opanda ntchitowo. Iye analinyamula ilo ndi kuyamba kuliŵerenga ilo. Mwamsanga iye anamwerekera mu ilo. Zinangochitika kuti ilo linali bukhu la Watch Tower Society la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo. Iye analembera ofesi ya nthambi ya Sosaite kupeza mabukhu owonjezereka. Ofesi ya nthambi mwamsanga inatumiza apainiya kukaitanira pa iye. Phunziro linayambika ndi iye, ndipo pambuyo pa kokha maphunziro oŵerengeka, iye anazindikira ukoma wa chowonadi ndi kuyamba kuyeretsa moyo wake wa zizoloŵezi zoipa ndipo pambuyo pake kutaya mafano ake a chipembedzo a Chihindu. Pasanapite nthaŵi yaitali, iye ndi mwana wake wamkazi wamkulu koposa anadzipereka iwo eni kwa Yehova ndipo anabatizidwa. Tsopano iye ndi mpainiya wokhazikika.
Zowonadi, “zotuta zichulukadi, koma antchito ali oŵerengeka” m’munda wobala zipatso wa Burma.—Mateyu 9:37, 38.