Kusangalala ndi Nyimbo—Nchiyani Chimene Chiri Mfungulo?
MKHALIDWE woipa koposa wa chisembwere ndi kulambira mafano unali kuchitidwa m’dziko lamakedzana. Chotero, mtumwi Paulo anachipeza icho kukhala choyenerera kupereka uphungu wamphamvu kwenikweni pa mkhalidwe Wachikristu. Ku mpingo wa ku Efeso iye analemba kuti: “Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m’chitsiru cha mtima wawo, odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chiri mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo.”—Aefeso 4:17, 18.
Kodi kameneko sikalinso kalongosoledwe kabwino ka njira mu imene zinthu ziriri lerolino? Ichi chimaphatikizapo m’munda wa nyimbo. Zochulukira za nyimbo zamakono zimawunikira mtundu womwe uli ‘wachilendo ku moyo waumulungu.’ Kaŵirikaŵiri kamvekedwe ka mawu kamatchera msampha ‘mtima wouma,’ wopanda chifundo kapena chikondi.
Koma Paulo anatengera uphungu wake patsogolo pang’ono mwa kunena kuti: “Kulingalira kwawo kwa chabwino ndi choipa kutanyengedwa, iwo adzipereka iwo eni ku kugonana ndi kulondola mosamalitsa ntchito ya chidetso cha mtundu uliwonse.”—Aefeso 4:19, The Jerusalem Bible.
‘Kulondola mosamalitsa ntchito ya chidetso’ kumeneku kumawunikiridwa mu zochulukira za nyimbo za lerolino. Kamvekedwe ka mawu ndi cholinga cha kaimbidweko zimakhala zosangalatsa ku mbadwo womwerekera m’kugonana, chiwawa, anam’goneka, ndi zosangulutsa. Ndimotani mmene Akristu ayenera kuwonera misampha yoteroyo? Onani mawu a Paulo: “Tsopano mmenemo simmene inu munaphunzirira kuchokera kwa Kristu, kusiyapo kokha ngati munalephera kumumva iye momvekera pamene munaphunzitsidwa chimene chiri chowonadi mwa Yesu.”—Aefeso 4:20, 21, JB.
“Kusinthanso Kwauzimu” Kuli Koyenerera
Ndimotani mmene tingagwiritsire ntchito chenjezo limeneli mu nkhani ya nyimbo zomwe zimawunikira mzimu wa dziko? M’chakuti, ngati tiri ndi “maganizo a Kristu,” uko ndiko kuti, ngati tiri ndi mkhalidwe wake wa maganizo, sitidzafuna kumvetsera ku nyimbo zomwe ziri za “padziko, unyama, uchiwanda.”—1 Akorinto 2:16; Yakobo 3:15.
Koma mungafunse kuti, ‘Ndimotani mmene ndingasinthire kukonda kwanga nyimbo?’ Kachiŵirinso Paulo akuthandiza, popeza akunena kuti: “Muyenera kusiya njira yanu yakale ya moyo; muyenera kuika pambali ukale wanu, womwe umawonongeka ndi kutsatira zikhumbo zachinyengo. Maganizo anu ayenera kukhalitsidwa atsopano ndi kusinthanso kwauzimu.”—Aefeso 4:22, 23, JB.
Limenelo ndilo yankho, kukonzanso kwa maganizo kupyolera mu kusinthanso kwauzimu. Ichi chimaphatikizapo zochulukira kuposa kukonda kwathu nyimbo. Chimaitanira pa kuphunzitsanso, kukweza miyezo ndi mapindu. Chimatanthauza kusintha m’njira yathu yolingalira, dongosolo losiyana la njira yogamulira zinthu. Ndipo chimaphatikizapo kuwona zinthu kuchokera ku lingaliro la Mulungu ndi Kristu. Monga mmene Paulo analongosolera icho momvekera bwino kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akorinto 10:31.
Zochulukira za nyimbo zamakono sizimabweretsa ulemerero uliwonse kwa Mulungu. Mosiyanako, zimatsitsa mapindu amenewo amene Akristu amaimira ndi kaamba ka amene ambiri akhala ofunitsitsa kufa m’ndende ndi m’misasa yachibalo. Chotero, nchifukwa ninji tiyenera kulingalira icho kukhala nsembe ngati tifunikira kupanga masinthidwe m’kukonda kwathu nyimbo kotero kuti tisakhale ‘tikukonda dziko lapansi, kapena za dziko lapansi’?—1 Yohane 2:15-17.
Nyimbo Zabwino—Nchiyani Chimene Chiri Mfungulo?
Ngati, chifukwa cha kulingalira kwathu maprinsipulo a Malemba, tikana nyimbo zotsitsa, kodi tidzaloŵa izo m’malo ndi chiyani? Chabwino, bwanji osasanthula mbali zina zatsopano za nyimbo? Izo zingakhale zosangalatsa kwambiri ndi zomangirira kuposa izo zimene tingakhale tinazikonda kalelo. Mwachitsanzo, katswiri woimba nyimbo za rock wakale ananena ichi ponena za masinthidwe amene anawachita:
“Ndinayenera kupanga kuyesetsa kupanga kusintha kuchoka ku kamvekedwe kopepuka ka nyimbo za rock kupita ku mtundu wotchuka wolandirika wa nyimbo ndi kaimbidwe kozama kophunzitsa. Koma pamene ndinazindikira kuti panali mbali yowonjezereka ku izo ndipo kuti sindikanathanso kuzindikiritsa mzimu wa nyimbo zochulukira zamakono, chinakhala chopepuka ndi chokhutiritsa kwenikweni. Izo mwadzidzidzi zinali zabwino. Ndinazindikira chimene ndinaphonya chifukwa cha kunyada kwanga kwa papitapo motsutsana ndi mtundu wina uliwonse wa nyimbo.”
Pali mtundu wochulukira wa nyimbo zophunzitsa, limodzinso ndi nyimbo zachikale ndi zamakono, zomwe ziri ndi kaimbidwe kabwino, kamvekedwe koyera, ndipo sizimalongosola nthanthi zosemphana ndi maprinsipulo a Baibulo. Mfungulo iri kupeza ndi kusangalala ndi nyimbo zomwe sizidzasonkhezera molakwika kulingalira kwathu, nyimbo zomwe ziri ‘zolungama, zoyera, zomveka zokoma, zaubwino, kapena zachitamando.’—Afilipi 4:8.
Mbali ya Nyimbo m’Moyo wa Mkristu
Kwa ena, njira imodzi yosangalalira ndi nyimbo iri mwa kuimba kapena kuphunzira kuseŵera chiwiya choimbira. Chisangalatso chachikulu chingatengedwe kuchokera ku kuseŵera wekha kapena kuseŵera kwa gulu ndi banja ndi mabwenzi. Mofanana ndi mu zinthu zonse, ngakhale kuli tero, kulinganizika kumafunikira. Chosangulutsa kapena kutaya nthaŵi sikuyenera kukhala konkitsa m’moyo wa Mkristu. Ngati chimenecho chingachitike, ngakhale nyimbo zabwino, chifukwa cha kupambanitsa, zikakhala ndi ziyambukiro zoipa. Chotero Mkristu akakhala m’ngozi ya kukhala ‘wokonda zokondweretsa osati wokonda Mulungu.’—2 Timoteo 3:4.
Nyimbo zirinso mbali yaikulu ya kulambira kwathu Yehova. Mu Israyeli wakale, Asafu ndi abale ake anaimba kuti: “Yamikani Yehova, itanani dzina lake; bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita za iye. Myimbireni, myimbireni zomulemekeza, fotokozerani zodabwiza zake zonse.” Inde, nyimbo zingatamande Mulungu ndi kumkondweretsa.—1 Mbiri 16:8, 9.
Nyimbo za Ufumu zogwiritsidwa ntchito ndi Mboni za Yehova pa Nyumba za Ufumu zawo ziri zozikidwa pa malemba a Baibulo, masalmo, mapemphero, ndi ziphunzitso. Kodi sitingasangalalenso mwakuya ndi nyimbo zopatulika zimenezi? Ndipo kodi sitiyenera kusonyeza chisangalalo chathu mwa kuimba nyimbo zimenezi ndi kudzimva ndi kutenthedwa maganizo? Ngakhale pa zochitika zosakhala misonkhano Yachikristu, kodi sitingasangalatse miyoyo yathu ndi makonzedwe okongola a nyimbo zimenezi zotchedwa Kingdom Melodies?
M’kuperekedwa kwa nyimbo zogwiritsira ntchito zoimbira kumeneku, akatswiri oimba onsewo ali Mboni za Yehova. Ena ali ogwira ntchito yoimba omwe amaseŵera m’magulu ogwiritsira ntchito zoimbira zosiyanasiyana. Ena, kuphatikizapo yemwe kale anali katswiri wa nyimbo za rock wogwidwa mawu pamwambapoyo, ali anthu achichepere okhala ndi luso omwe amasangalala ndi mitundu yambiri ya nyimbo zodekha. Iwo samadzimva kuti akuphonya chirichonse chifukwa chokana nyimbo zomwe zimawunikira mikhalidwe yakudziko lapansi, yauchiwanda. Chitsanzo chawo chabwino chimasonyeza kuti ife nafenso, ngati tilola maprinsipulo a Baibulo kulamulira chosankha chathu, tingapeze chisangalalo chabwino m’nyimbo, ponse paŵiri zakudziko ndi zopatulika.—Aefeso 5:18-20.
[Bokosi patsamba 28]
“Nyimbo za rock ziri ndi chisonkhezero chimodzi chokha, chisonkhezero chaumbuli, ku chikhumbo cha kugonana—osati chikondi, osati eros, koma chikhumbo cha kugonana chosakulitsidwa ndipo chosaphunzitsidwa. . . . Anthu achichepere amadziŵa kuti nyimbo za rock ziri ndi kaimbidwe ka kuyanjana kwa kugonana.”—The Closing of the American Mind, lolembedwa ndi Allan Bloom.