Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 11/15 tsamba 3
  • Kodi Ndimotani Mmene Mumawonera Malamulo Khumi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndimotani Mmene Mumawonera Malamulo Khumi?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Malamulo Khumi a Mulungu Ndi Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mmene Malamulo 10 Amakukhudzirani
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Kodi Ife Tiri Pansi pa Malamulo Khumi?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Muyenera Kumvera Malamulo Khumi?
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 11/15 tsamba 3

Kodi Ndimotani Mmene Mumawonera Malamulo Khumi?

ANTHU amawona Malamulo Khumi a Baibulo m’njira zosiyanasiyana. A Seventh-Day Adventist amanena kuti Malamulo Khumi adakagwirabe ntchito kwa anthu onse. A Lutheran amaŵalingalira kukhala “mpambo wabwino koposa wa malamulo operekedwa pa amene munthu angakhazikitse njira yake ya moyo.” Mlankhuli Wachikatolika akulongosola kuti, “atamvetsetsedwa bwino, Malamulo Khumi adakaperekabe maziko a kakhalidwe Kachikristu.”

Chotero, pamene kuli kwakuti magulu ena achipembedzo amakhulupirira kuti tiyenera kumvera Malamulo Khumi onse, ena amaŵalingalira kukhala kokha chitsogozo cha makhalidwe abwino. Ndithudi, mogwirizana ndi Encyclopædia of Religion and Ethics, “mwinamwake palibe bukhu la munthu limene limapereka chisonkhezero chachikulu pa moyo wachipembedzo ndi makhalidwe kuposa Decalogue [Malamulo Khumi].” Kodi nchifukwa ninji ziri choncho? Choyamba lingalirani zimene amanena. Iwo ngachidule, okhoza kumveka, ndipo amphamvu. Koma kodi ndimotani mmene muyenera kuwonera Malamulo Khumi? Kodi amatanthauzanji kwa inu?

[Bokosi patsamba 3]

MALAMULO KHUMI

1. Usakhale nayo milungu ina koma ine ndekha.

2. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chirichonse cha zinthu za m’thambo lakumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo . . .

3. Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe . . .

4. Uzikumbukira tsiku la Sabata likhale lopatulika. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito zako zonse; . . . Usagwire ntchito iriyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m’mudzi mwako . . .

5. Uzilemekeza atate wako ndi amako . . .

6. Usaphe.

7. Usachite chigololo.

8. Usabe.

9. Usamnamizire mnzako.

10. Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.​—Eksodo 20:3-17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena