Ripoti la Olengeza Ufumu
Kuvomereza Mbiri Yabwino m’Belgium
“KODI ndani anawona zinthu zoterozo?” ikutero ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova m’Belgium. (Yerekezerani ndi Yesaya 66:8.) Dziko lokongola limeneli likuchitira ripoti chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 24,464 m’chaka chautumiki cha 1989. Panalinso chiwonjezeko cha 4 peresenti mu avereji ya chiŵerengero cha kukhala ndi phande mu ntchito ya kulalikira mwezi uliwonse.
◻ Mbiri yabwino yolengezedwa ndi Mboni za Yehova inavomerezedwa ndi wansembe wa Katolika amene pa Misa ya pa Sande anauza gulu lake kuti: “Ngati Mboni za Yehova zifika pakhomo panu, atsegulireni. Izo ziri ndi chowonadi!” Izi ndizo zimenedi dona wina anachita. Pamene Mboni zinafika, anatsegula khomo lake ndi kulandira bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Pambuyo pake anapempha bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso Padziko Lapansi. Phunziro Labaibulo linayambidwa naye, koma mwamuna wake sanatsaganemo. Chotero mbale anachitira telefoni mwamunayo nam’funsa ngati akanakonda kukhala ndi moyo ndi mkazi wake mdziko labwino kwambiri? Monga chotulukapo, iye anatsagana nawo paphunzirolo. Aŵiriwo anali kukhala pamodzi popanda kulembetsa ukwati mwalamulo, koma analembetsa ukwati wawo ndipo mwamsanga anabatizidwa.
◻ Chowonadi chinasintha moyo wa msungwana wina wachichepere. Pamene anali asanafike zaka 14 za kubadwa, anasiidwa ali yekhayekha. Anakomana ndi mnyamata wina nakhala naye muumoyo wopanda pake, kumwa mankhwala oledzeretsa ndi kusonyeza mzimu wachiwawa. Ndiyeno mnyamatayo anafera mngozi ya galimoto. Zimenezi zinasiya msungwanayo ali wosokonekera maganizo ndi thupi, ndipo analingalira za kudzipha. ‘Kodi ndingapeze kuti chothetsera mavuto anga?’ anadabwa motero. Iye anakomana ndi munthu wolankhula ndi mzimu amene anamchititsa kukhulupirira kuti akakhoza kulankhulana ndi bwenzi lake lakufalo. Iwo anayesa mchitidwe wogoneka munthu mwa matsenga ndi chidziwitso chopezedwa mwapadera. Atalephera kupeza chitonthozo choyembekezeredwa mu izi, msungwanayo anagweranso m’kukhala wa tondovi kwambiri. Kwa miyezi ingapo iye anadzibindikiritsa kotheratu. Ndiyeno mmodzi wa Mboni za Yehova anakumana naye nayesayesa kumuthandiza mwauzimu. Kwakanthaŵi izi zinachitika mwa kalata, ndipo mnthaŵi yokwanira zinthu zinalinganizidwa pambuyo pakuyesayesa kwakukulu ndi kulimba mtima kumbali yake. Tsopano anawonjoledwa ku chisonkhezero cha ziwanda, kuchokera ku chizolowezi cha fodya, ndi kuchokera m’malingaliro aliwongo lalikulu. Mkupita kwanthaŵi, chidziŵitso chowownjezereka cha Baibulo ndi mzimu wa Yehova zinamthandiza kwambiri. Ndiponso, misonkhano inamlimbikitsa, pamene mwaphamphu anaikonzekera. Tsopano ngwobatizidwa ndipo ali ndi mzimu waupainiya. Akuchititsa kale maphunziro a Baibulo angapo, mmodzi wa iwo ndamake, amene tsopano akufika pa misonkhano ina. Ndithudi, Yehova wamthandiza!
◻ Awo opindula ndi mipata yopezeka msukulu amasangalala ndi chipambano chabwino kwambiri mkufalitsa mbiri yabwino. Mlongo wina wachichepere msukulu ku Belgium anapatsidwa gawo la kulankhula pankhani yodzisankhira. Iye anasankha kulankhula za Mboni za Yehova ndi zikhulupiriro zawo, akumatenga nkhani yakeyo m’kabrosha ka Jehovah’s Witnesses in the 20th Century. Profesa wake anachita chidwi. Pambuyo pa kupereka nkhani mkalasi, ophunzirawo analoledwa kufunsa mafunso. Pambuyo pake amkalasi anzake angapo anafunsa zimene akayenera kuchita kuti akhale ndi moyo m’Paradaiso wa Mulungu wotchulidwa m’nkhani yake. Ambiri, kuphatikizapo profesa, anapempha makope a mabrosha osiyanasiyana amene mlongoyo adali nawo. Makalsi ena anapempha mabrosha ndi chidziŵitso chowonjezereka, ndipo profesa wachipembedzo anapenda mabrosha ndipo anawavomereza m’kalasi yake.
Mchitidwe wolimba mtima wa mlongo wathu wachichepereyu unadalitsidwa. Mabrosha makumi aŵiri ndi atatu anagaŵiridwa kwa aprofesa aŵiri ndi kwa ophunzira ambiri; wophunzira mmodzi, atamva nkhaniyo, anapempha mawu ofotokoza ntchito ya Mboni za Yehova m’kalasi mwake.
Ambiri akuvomereza mbiri yabwino m’Belgium. Akuvomereza Mawu a Mulungu, ‘osati monga mawu a anthu, koma, monga momwe iwo aliridi, monga mawu a Mulungu, amene akugwiranso ntchito mwa inu okhulupirira.’—1 Atesalonika 2:13.