Ripoti la Olengeza Ufumu
Umboni Wamwamwaŵi Ubala Zipatso
YESU anayambitsa kukambirana kumene kunatsogolera ku ulaliki wamwamwaŵi koma wokhutiritsa kwenikweni pamene anati kwa mkazi Wachisamariya: “Undipatse Ine ndimwe.” (Yohane 4:7) Nafenso lerolino tingakhale okhutiritsa mofananamo ngati tikhala ogalamuka ku mipata yonse ya umboni wamwamwaŵi. Mbale wina mu Australia anayambitsa kukambirana kwamwamwaŵi mwakuŵerenga lemba latsiku pa benchi ya m’paki. Mwamuna wolakalaka anawona bukhulo nati nayenso anali wokondweretsedwa m’Malemba. Iye sanali Mkatolika wachangu amene anaphunzitsidwa chisinthiko m’sukulu Yachikatolika ndipo tsopano sanadziŵe chokhulupirira. Mbaleyo anapanga makonzedwe ompezera bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?a Masiku aŵiri pambuyo pake anapereka bukhulo kumalo antchito a mwamunayo, kungopeza kuti anali atachokapo. Mlembi wake anatsomphola bukhulo, nati: “Takhala tikuyembekezera bukhuli.”
Maola aŵiri pambuyo pake mbaleyo analandira foni yochokera kwa mwamunayo akumapempha makope ena aŵiri a bukhu la Creation ndi kumpempha Mboniyo kuti ikamchezere mu ofesi yake. Pamene mbaleyo anapita ku ofesi imeneyo, anakapeza mwamunayo ndi ena aŵiri alipo. Phunziro Labaibulo linayambidwa kwa iwo, kuphatikizapo mlembiyo, ndipo zinakonzedwa kuti mbaleyo adzifikira kaŵiri pa mlungu. M’milungu yapambuyo pake, bwenzi lachikazi la mwamunayo, ‘Mkristu wobadwanso,’ anapitirizabe kutumiza makalata akumafunsa mafunso a m’Baibulo. Pomalizira pake, nayenso anadziphatika m’phunzirolo, monga anachitira mnzake wa m’bizinesi wa mwamunayo ndi bwenzi lake, amene anali wachisinthiko.
Iwo anapitirizabe ndi maphunziro awo a Baibulo mokhazikika kwa miyezi isanu, ndi phunziro lachiŵiri likumachitidwira m’paki mlungu uliwonse. Kenaka bwenzi lachimuna la mlembiyo linaloŵamo m’gulu la phunzirolo. Mwamsanga pambuyo pake, bwenzi la mwamuna woyambayo ndi mnzake anasamukira ku Idaho mu United States, kumene anapitiriza kuphunzira. Milungu yochepa pambuyo pake, mwamuna woyambayo anafikiridwa ndi mlendo kotheratu, yemwe anafunsa chimene chinachitika ku makambitsirano a Baibulo a m’paki. Mwachiwonekere, iye anali kumvetserako pamaphunziro awo. Makonzedwe anapangidwa kuti nayenso aphunzire.
Kodi nchiyani chinali chotulukapo cha zonsezi? Miyezi khumi kudza isanu ndi itatu kuchokera pa kukambitsirana koyamba m’paki muja, mwamuna woyamba ndi bwenzi lake lachikazi, yemwe kale anali ‘Mkristu wobadwanso,’ anakwatirana ndipo anabatizidwa. Mlembiyo ndi bwenzi lake lachimuna nawonso anakwatirana ndipo anabatizidwa. Mnzake wa m’bizinesi ndi bwenzi lake amene anapita ku United States anabatizidwa, ndipo mmodzi wa iwo tsopano akutumikira mokhazikika monga mpainiya wothandizira. Uja amene anamvetsera ku makambitsirano a Baibulo m’paki anapitiriza ndi maphunziro ake. Iye kenaka anasamukira ku Ireland, ndipo ankayembekezera kubatizidwa!
Zonsezi zinachitika chifukwa chakuti mbale anatenga mwaŵi wa kupuma kwachakudya chamasana kuchitira umboni wamwamwaŵi, ndipo Yehova anadalitsa zoyesayesa zake. Lolani kuti nafenso titenge mwaŵi wa mpata uliwonse kufalitsa mbiri yabwino kwa akumva njala ya uthenga wa Ufumu wa Yehova!
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.