Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 7/1 tsamba 18-23
  • Mapeto Akudzawo a “Buku la Nkhondo za Yehova”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapeto Akudzawo a “Buku la Nkhondo za Yehova”
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Bukhu la Nkhondo za Yehova
  • Melikizedeke Wamkulu​—Munthu Wankhondo
  • Mulungu Wankhondo Adzitengera Mbiri Yaulemerero
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kuthetseratu Nkhani ya Chilengedwe Chonse
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mphamvu Zowononga—‘Yehova Ndi Msilikali Wamphamvu’
    Yandikirani Yehova
  • Opulumuka a m’Mitundu Yonse
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 7/1 tsamba 18-23

Mapeto Akudzawo a “Buku la Nkhondo za Yehova”

“Ananena m’buku la Nkhondo za Yehova.”​—NUMERI 21:14.

1, 2. Kodi mpachochitika chiti chakale pamene Yehova anasonyeza Aigupto kuti iye anali Mulungu wankhondo, ndipo kodi anachita motani?

ANTHU samavomereza kwenikweni lerolino kuti Mulungu wa m’Baibulo, Yehova, ndi munthu wankhondo, ngwazi yankhondo. Nsonga imeneyi inasonyezedwa pamene anapulumutsa anthu ake akalekale ku kutsenderezedwa mu Igupto. Farao anasonkhezeredwa ndi mdani wosawoneka wa anthu amenewo, Satana Mdyerekezi, kuyesera kuwapha ndi ntchito yakalavulagaga. Pozindikira tsopano chomwe anataikiridwa mwakumasula Aisrayeli, Farao ndi makamu ake ankhondo anaŵalondola iwo.

2 Komabe, Farao sanazindikire kuti Mulungu wa Aisrayeli akakhala Mulungu wankhondo kuti apulumutse anthu Ake. Pamene makamu a Aigupto ankaoloka pamalo ouma a Nyanja Yofiira m’kulondola kobwezera, Mulungu wa Aisrayeli okhala pangoziwo anachitapo kanthu ndi kumiza okwera pamagareta ndi a pakavalo, mwakumasula madzi oundanawo kuthira pamalo othaŵira omwe anatsegulidwira Aisrayeli mozizwitsa.​—Eksodo 14:14, 24-28.

3. M’nyimbo yawo ya chilakiko, kodi Aisrayeli anazindikiritsa Yehova kukhala Mulungu wa mtundu wotani, koma kodi mitundu yamakono imanyalanyaza mfundo iti?

3 Pokhala osungika pagombe la kummawa kwa Nyanja Yofiira, Aisrayeli okondwerawo anaimba nyimbo yachilakiko iyi kutamanda Mpulumutsi wawo wakumwamba: ‘Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; Kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; Ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzammveketsa. Yehova ndiye wankhondo; Dzina lake ndiye Yehova. Magareta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m’nyanja; Ndi akazembe ake osankhika anamira m’Nyanja Yofiira.’ (Eksodo 15:1-4) Pompo pa Nyanja Yofiirayo, Yehova anadzisonyeza yekha kukhala munthu wankhondo wokhoza kuchita zinthu zadzaoneni. Mitundu yadziko yanyalanyaza nsonga imeneyi.

4, 5. Kodi mafuko okondwera 12 a Israyeli anachokera kwa kholo limodzi liti, ndipo kodi ameneyu anakhala bwenzi la yani chifukwa cha mkhalidwe uti?

4 Mneneri Mose, yemwe anatsogolera kuimbidwa kwa nyimbo youziridwa imeneyo, anamutcha Yehova “Mulungu wa kholo langa.” Abrahamu Wachihebri anali kholo lapadera la mtundu wa Israyeli. Kunali kwa iye, kupyolera mwa Isake ndi Yakobo ndi ana aamuna 12 a Yakobo, kumene mafuko 12 a Israyeli anachokera. Abrahamu anadzitsimikizira kukhala mlambiri wa Yehova Mulungu wopereka chitsanzo. Iye anali mwamuna wa chikhulupiriro champhamvu choterocho kwakuti pamene Yehova anamuuza kuti achoke m’dziko lakwawo la Uri wa Akasidi, iye mosazengereza ananka kudziko limene Yehova anati akamsonyeze, nchidaliro chakuti Mulungu akakwaniritsa lonjezo Lake kulipereka kwa iye ndi kwa mbadwa zake.

5 Chifukwa cha chikhulupiriro chopambana cha Abrahamu, Yehova analonjeza kumpatsa Abrahamu “mbewu,” kapena mbadwa, mwa imene mabanja onse adziko lapansi, kuphatikizapo mabanja a lerolino, akadzidalitsa okha. (Genesis 12:2, 3; 22:17, 18) Abrahamu anabweretsedwa muunansi wathithithi woterowo ndi Mulungu wake kwakuti anatchedwa “bwenzi la Mulungu,” Mulungu iyemwini anatcha kholo lokhulupirikali “bwenzi langa.”​—Yakobo 2:23; Yesaya 41:8.

6. Ngakhale kuti anali woyendayenda wamtendere m’Dziko Lolonjezedwa, kodi Abrahamu anadzitsimikizira yekha kukhala wankhondo wodalira mwa Yehova motani?

6 Ngakhale kuti ankayendayenda monga mlendo m’Dziko Lolonjezedwa, Abrahamu anatsimikizira kuti iye akachita monga msilikali, munthu wankhondo. Nthaŵi ina mafumu anayi akunja analowerera Dziko Lolonjezedwalo natenga Loti mphwake wa Abrahamu ndi banja la Loti. Atasonkhezeredwa ndi unansi wa pabanja, Abrahamu anakonzekeretsa akapolo ake aamuna 318 ndi zida, ndipo limodzi ndi kuchilikizidwa ndi magulu atatu ogwirizana nawo akwawoko, Aneri, Esikolo, ndi Mamre, iye anapitikitsa adaniwo. Mwakuwukira mowadabwitsa usiku, Abrahamu ndi makamu ake anagonjetsa olowererawo, ngakhale kuti linali gulu lamphamvu kwenikweni. ‘Kuphedwa kwa mafumu’ kunachitika. (Ahebri 7:1; Genesis 14:13-17) Abrahamu anapulumutsa Loti ndi banja lake ndikubwezeretsa zinthu zonse zimene zidabedwa.

7-9. (a) Kodi Abrahamu anakachezera wansembe uti, ndipo kodi anakapatsidwa dalitso lotani? (b) Kodi Abrahamu anasonyeza motani kuti anafuna kulemeretsedwa ndi Mulungu Wamkulukulu yekha? (c) Monga momwe zatsimikiziridwa ndi Melikizedeke, kodi ndani anapatsa Abrahamu chilakiko chankhondo?

7 Abrahamu anazindikira kuti kugonjetsa kwa gulu lake lankhondo kunatsimikizira kukhala chipambano mwa thandizo la Yehova Mulungu lokha, ndipo paulendo wake wolakika wobwerera kwawo, iye anatha kuvomereza nsongayi poyera. Iye anadziŵa kuti wansembe wovomerezedwa ndi Mulungu wake akapezeka mumzinda wa Salemu. Chotero anagubira ku mzinda umenewo. Mbali yomalizira ya Genesis mutu 14 ikutidziŵitsa motere chomwe chinachitika pambuyo pake:

8 ‘Ndipo Melikizedeke mfumu ya ku Salemu, anatuluka nawo mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu. Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi; ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m’dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse. Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha. Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi, kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale chingwe cha nsapato, ngakhale kanthu kali konse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu; koma chokhachi anadya anyamata, ndi gawo lawo la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Aneri, Esikolo, ndi Mamre, iwo atenge gawo lawo.’​—Genesis 14:18-24.

9 Monga mmene mavesiwa akusonyezera, Melikizedeke, wansembe wachifumu wa mzinda wa Salemu, anatsimikizira chikhutiro cha Abrahamu kuti anali Mulungu Wamkulukulu amene anamenyera iye ndi magulu ake ankhondo ndikumpatsa chilakiko. Melikizedeke Mfumu ndi Wansembe sanapatuke kumbali ya Yehova pankhaniyi.

Bukhu la Nkhondo za Yehova

10. Kodi nkuti kumene kuli kutchulidwa koyamba kwa nkhondo m’Baibulo, ndipo kodi nchifukwa ninji kunali chiyambi chokha cha nkhondo zolakika za Yehova?

10 Mafotokozedwe a mu Genesis 14 onena za kuloŵerera Dziko Lolonjezedwa ndi kugonjetsa kwa Abrahamu makamu oukira okonzekeretsedwa ndi zida ndiko kutchulidwa koyamba kwa nkhondo m’Malemba Oyera. Chotero, zaka zoposa mazana anayi chilakiko chake chisanachitike pa Nyanja Yofiira, Yehova anadzisonyeza yekha kukhala munthu wankhondo, “ngwazi yankhondo.” Komabe, kumeneko kunali chiyambi chokha. Zilakiko zazikulu kwenikweni ndi zodabwitsa zikatsatira, kuphatikizapo chomalizira pa ‘mapeto a dongosolo iri la zinthu.’​—Mateyu 24:3.

11. Kodi ndiliti limene liri “buku la Nkhondo za Yehova,” koma nkuti kwinanso kumene kuli zolembera zambirimbiri za nkhondo zake zolakika?

11 Mogwirizana ndi zimene zanenedwa pa Numeri 21:14, “buku la Nkhondo za Yehova” linalembedwa. Cholembera, kapena mbiri yodalirika imeneyi ya nkhondo za Mulungu mokomera anthu ake, mwinamwake inayambira ndi nkhondo iyi yomenyedwera Abrahamu wokhulupirika. Mose anadziŵa za bukhuli koma samatipatsa tsatanetsatane aliyense wonena za ilo. Chotero, sitinadziŵitsidwe njira zonse zimene Yehova anadzisonyeza yekha kukhala munthu wankhondo mkati mwa nyengo ya nthaŵi yolembedwa m’bukhu limenelo, la Nkhondo za Yehova. Komabe, chiyambire kutchulidwa kwa bukhu limenelo mbali yaikulu ya Baibulo Loyera linadzalembedwa, ndipo ichi chikutipatsa ife zolembera zambirimbiri za kulakika kwankhondo za Yehova.

Melikizedeke Wamkulu​—Munthu Wankhondo

12. Kodi Melikizedeke anachitira chithunzi Nduna yaikulu iti ya Mulungu Wamkulukulu, ndipo kodi ndi salmo liti lolembedwa ndi Davide limene lalunjikitsidwa kwa ameneyu kukhala wansembe ndi munthu wankhondo?

12 Pamene Abrahamu anagonjetsa Kedorelaomere ndi mafumu ake ogwirizana nawo, Melikizedeke anamdalitsa. Melikizedeke Mfumu ndi Wansembe mwaulosi anachitira chithunzi Yemwe akakhala Wansembe Wamkulu wa Mulungu Wamkulukulu ndiponso munthu wankhondo wamphamvu wochilikizidwa ndi Mulungu Wamkulu. Salmo 110, lolembedwa ndi Davide mfumu yankhondo pansi pa kuuziridwa, lalembedwera kwa wamkulu koposa Melikizedeke wa ku Salemu Ameneyu pamene limati: ‘Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; Chitani ufumu pakati pa adani anu. Yehova walamulira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melikizedeke. Yehova pa dzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake.’​—Salmo 110:2, 4, 5.

13. Mu Ahebri mitu 7 ndi 8, kodi Amene ali wamkulu kuposa Melikizedeke wakale wazindikiritsidwa kukhala yani, ndipo ndi mmalo okwezeka otani omwe Ameneyu anakalowa ndipo ndi nsembe ya mtundu wotani?

13 Mlembi wouziridwa wa bukhu la Ahebri anavumbula chizindikiro cha Ameneyu kwa amene mawu amenewo analembedweradi pamene anati: ‘Mmene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthaŵi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.’ (Ahebri 6:20) M’mutu wotsatira wa Ahebri, ukulu wa Melikizedeke wakale walongosoledwa. Komabe, ukulu wake wansembe wapambanidwa ndi Yemwe anamuchitira chithunzi, Yesu Kristu wolemekezedwa, woukitsidwa, amene anakafika pamaso poyera pa Yehova Mulungu iyemwini ndi mtengo wa nsembe yoposadi chirichonse chimene Melikizedeke Mfumu ndi Wansembe wa ku Salemu anapereka.​—Ahebri 7:1–8:2.

14. Kodi Melikizedeke Wamkulu ndiye walamulira atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko kukhalamo ndi phande m’ntchito zankhondo za yotchedwa mitundu Yachikristu?

14 Wansembe wachifumu Melikizedeke anadalitsa munthu wankhondo, Abrahamu wolakika. Koma kodi bwanji ponena za Melikizedeke Wamkulu, Muyambitsi wa Chikristu chowona? Atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko amati amaimira Yesu Kristu podalitsa magulu ankhondo a yotchedwa mitundu Yachikristu ndi kuwapempherera. Koma kodi Wansembe Wamkulu wa Yehova m’mwamba waŵachilikiza atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko m’kuchita izi? Chotero kodi iye walandira liŵongo la kukhetsa mwazi konseku komwe kwapitirizabe mu yotchedwa Nyengo Yachikristu, kuphatikizapo mwazi umene unakhetsedwa mu Nkhondo Zadziko I ndi II? Ndithudi ayi! Palibe nthaŵi pamene iye analamulira ophunzira ake owona kukhala mbali ya dziko iri ndi kugwirizana m’nkhondo zake zokhetsa mwazi.

Mulungu Wankhondo Adzitengera Mbiri Yaulemerero

15, 16. Kodi Yehova anadzitengera chiyani pamene anamenyera anthu ake kuwapulumutsa kutuluka mu Igupto?

15 Nehemiya 9:10 amalozera ku kupulumutsa kwa Yehova mafuko 12 a Israyeli kuchoka mu Igupto, ndikuti: ‘Nimuchitira zizindikilo ndi zodabwiza Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m’dziko lake; popeza munadziŵa kuti anawachitira modzikuza [Aisrayeli]; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.’​—Yerekezerani Eksodo 14:18.

16 Mneneri Yesaya akulozera ku mtundu wa mbiri imeneyi pamene akunena za Yehova kukhala ‘Amene anayendetsa mkono wake waulemerero pa dzanja lamanja la Mose. Amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha.’ Ndipo polankhula kwa Yehova, iye akuti: ‘Chomwecho inu munatsogolera anthu anu kudzitengera mbiri yaulemerero.’ (Yesaya 63:12-14) Pochonderera Yehova kuti achitireponso kanthu anthu ake, Danieli anamfikira iye mwakuti “amene munatulutsa anthu anu m’dziko la Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino.”​—Danieli 9:15; Yeremiya 32:20.

17. Kodi Yehova adzatumiza yani kukamenyera m’dzina lake, ndipo chotero kodi adzaisonyezanji mitundu yonse ya lerolino?

17 Panthaŵi yake, Yehova Mulungu adzatumiza Yesu Kristu, Melikizedeke Wamkulu, monga munthu wankhondo wamphamvu. Kupyolera mwa iye, Yehova adzadzitengera mbiri yoposa iriyonse ya kumbuyoko yofotokozedwa m’bukhu la Nkhondo za Yehova kapena m’Malemba Achihebri a Baibulo Loyera. M’mutu womalizira wa bukhu lachiŵiri ku lomalizira la Malemba Achihebri, kuwukira kwa mitundu yonse kolimbana ndi Yerusalemu kunanenedweratu. Kenaka, mogwirizana ndi Zekariya 14:3, ‘Yehova adzatuluka, nadzachita nkhondo ndi amitundu aja, monga anachitira nkhondo tsiku lakudumana.’ Mwanjirayi Mulungu wa Baibulo adzasonyeza mitundu yonse yamakono kuti iye adakali Mulungu wankhondo monga momwe analiri m’masiku a Israyeli wakale.

18, 19. Kodi ndi Yerusalemu uti amene adzakhala mnkhole wa kuwukiridwa kwakukulu kwa mitundu?

18 Ichi n’chiyembekezo chomwe chidakali kutsogolo kwathu. Koma kodi ndi Yerusalemu uti amene adzavutika ndi kuwukiridwa konseku? Ulosiwu sunakwaniritsidwe pa Yerusalemu wa m’tsiku la Zekariya. Mzinda umenewo unawonongedwa ndi magulu ankhondo Achiroma mu 70 C.E. Komabe, Yerusalemu anamangidwanso, ndipo lerolino akuwonedwa kukhala wopatulika ndi Chikristu Chadziko limodzinso ndi mtundu wa Israyeli wa kuthupi. M’nkhondo ya masiku asanu ndi limodzi ya mu 1967, Israyeli wakuthupi analanda Yerusalemu yense womangidwanso padziko lapansi. Komabe, palibe umboni ndiumodzi womwe wakuti Yehova Mulungu anakhalamo ndi mbali iriyonse m’kumenyanako. Mfumu yake yovekedwa ufumu, Yesu Kristu, sakulamulira m’Yerusalemu wa padziko lapansi, ndipo suulinso “mzinda wa Mfumu yaikurukuru,” ndiko kuti, wa Yehova.​—Mateyu 5:35.

19 Ayi, mzinda waukulu wa lamulo Wachiyuda umenewu, chiŵalo cha Mitundu Yogwirizana sindiwo Yerusalemu wotchulidwa muulosi wa Zekariya. Mmalo mwake, Zekariya akulozera ku Yerusalemu amene timaŵerenga m’bukhu la Ahebri. Mmenemo, Paulo akulembera Akristu odzozedwa ndikuti: ‘Mwayandikira ku phiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angero.” (Ahebri 12:22) Yerusalemu wakumwamba ameneyu siwina kuposa Ufumu Waumesiya wa Mulungu, woimiridwa padziko lapansi lerolino ndi gulu laling’ono la Akristu odzozedwa omwe amasangalala ndi chiyembekezo cha kukhala olamulira anzake a Yesu Kristu mu Ufumu umenewo. Awa adzakhala chandamali cha kuwukiridwa konenedweratuko.

20. Kodi ndi mawu ati amene Mfumu Hezekiya anauza anthu ake owopsyezedwa kuwadalira, ndipo kodi Mboni za Yehova zimadalira pa mawu a Mfumu iti yoposa Hezekiya?

20 Komabe, awa, kapena khamu lalikulu la Akristu okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi omwe atuluka m’mitundu yonse kudzagwirizana nawo m’kulambira kowona safunikira kuchititsidwa mantha ndi chotulukapo cha kuwukiraku. Pamene magulu ankhondo ochititsa mantha a Sanakeribu, mfumu ya Asuri, anadzalimbana ndi Yerusalemu m’kulamulira kwa Mfumu Hezekiya, Aisrayeli okhala m’ngoziwo anauzidwa kulingalira mkhalidwewo mwabata pamene Mfumu Hezekiya anati kwa iwo: “Pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo.” Chotulukapo chinali chakuti ‘anthu anachirikizika ndi mawu a Hezekiya mfumu ya Yuda.’ (2 Mbiri 32:8) Mboni za Yehova lerolino, zitawopsyezedwa ndi makamu a dongosolo iri ladziko, zingadalire pa mawu ofananawo ochokera kwa mfumu yaikulu kuposa Hezekiya, Yesu Kristu.

21. (a) Kodi nchifukwa ninji mawu a Yahazieli adzakumbukiridwa m’kuwukiridwa kukudzako pa Yerusalemu wakumwamba? (b) Kodi nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo cha nkhondo yomwe idzamenyedwa?

21 Panthaŵiyo, mawu olimbikitsa chikhulupiriro a Yahazieli Mlevi adzakumbukiridwa akuti: ‘Si kwanu kuchita nkhondo kuno ai; chirimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu.’ (2 Mbiri 20:17) Inde, kupyola m’nthaŵi yoopsya imeneyo, Yehova adzakhala ndi anthu ake. Chisungiko chawo ndi chipulumutso zidzadalira pa iye kuŵamenyera. Ndipo adzaŵamenyeradi, kupyolera mwa Mfumu yake yankhondo, Yesu Kristu! Chotulukapo chake? Kuwonongedweratu kwa gulu lowoneka ndi maso la Mdyerekezi padziko lapansi.​—Chibvumbulutso 19:11-21.

22. (a) Kodi nchiyani chimene chidzakhala mapeto achilakiko a bukhu la Nkhondo za Yehova, ndipo kodi Yehova adzadzitengeranji pamenepo? (b) Kodi nchiyani chimene okonda dzina la Yehova adzasonkhezeredwa kuchita ndi chilakiko chake?

22 Ndi mbiri yabwino chotani nanga imene Mulungu adzadzitengera ndi chilakiko chake chochititsa mantha pa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse’ imeneyi pa Harmagedo! (Chibvumbulutso 16:14, 16) Chaputala chatsopano, kunena kwake titero, chidzawonjezeredwa ku bukhu la Nkhondo za Yehova. Adzakhala mathedwe olakika, mapeto aakulu a dongosolo iri la zinthu. Bukhu lonse lathunthu lidzasonyeza kuti Mulungu Wamphamvuyonse sanalepherepo nkhondo. Okonda dzina la Yehova adzamthokoza mokondwera chotani nanga pambuyo pake! Pamenepo, ndithudi, vesi lomalizira la bukhu la Masalmo lidzakwaniritsidwa kwakukulukulu lakuti: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Haleluya.”​—Salmo 150:6.

Mafunso a Kubwereramo

◻ Kodi anthu amakono samayamikira chiyani ponena za Mulungu wa Baibulo, Yehova?

◻ Kodi Abrahamu anamenya nkhondo iti, ndipo kodi ndani anampatsa chilakiko?

◻ Kodi ndiliti limene liri “buku la Nkhondo za Yehova”?

◻ Kodi nchiyani chimene chidzakhala mapeto a “buku la Nkhondo za Yehova,” ndipo kodi adzatulukapo chiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena